Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lv tsamba 3
  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
  • Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Nkhani Yofanana
  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • ‘Pitirizani Kuyenda M’choonadi’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kodi Choonadi Ndi Chofunikabe Masiku Ano?
    Nkhani Zina
Onani Zambiri
Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
lv tsamba 3

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Wokondedwa Bwenzi la Yehova:

Yesu anati: “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:​32) Mawu amenewatu ndi olimbikitsa kwambiri. Tangoganizani, n’zotheka kudziwa choonadi ngakhale “m’masiku otsiriza” ovuta ano, pamene ziphunzitso zonyenga zafala kwambiri. (2 Timoteyo 3:1) Kodi mumakumbukira nthawi imene munayamba kudziwa choonadi cha m’Mawu a Mulungu? Muyenera kuti munasangalala kwambiri.

N’zoona kuti kudziwa choonadi cha m’Baibulo molondola komanso kuuza ena zimenezi nthawi zonse n’kofunika kwambiri. Komabe, chofunikanso kwambiri n’chakuti tizichita zogwirizana ndi choonadicho. Kuti tithe kuchita zimenezi, tiyenera kupitiriza kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kutikonda. Kodi zimenezi ndi zinthu ngati ziti? Zimene Yesu ananena usiku woti mawa lake aphedwa, zimayankha funso limeneli. Iye anauza atumwi ake okhulupirika kuti: “Mukasunga malamulo anga, mudzakhalabe m’chikondi changa, monga mmene ine ndasungira malamulo a Atate ndi kukhalabe m’chikondi chake.”​—Yohane 15:10.

Onani kuti Yesu anapitiriza kukondedwa ndi Mulungu chifukwa chosunga malamulo a Atate wake. N’zimenenso tiyenera kuchita masiku ano. Kuti tipitirize kukondedwa ndi Mulungu, nthawi zonse tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi choonadi. Usiku womwewo, Yesu ananenanso kuti: “Ngati zimenezi mukuzidziwa, ndinu odala mukamazichita.”​—Yohane 13:17.

Sitikukayikira kuti buku lino likuthandizani kupitiriza kugwiritsa ntchito choonadi pa moyo wanu, ndipo zimenezi zikuthandizani kuti ‘muzichita zinthu zimene zingachititse Mulungu kukukondani . . . pamene mukuyembezera kuti . . . mulandire moyo wosatha.’​—Yuda 21.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena