“Khalanibe M’chikondi cha Mulungu”
1. Kodi cholinga cha buku la “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu” n’chiyani?
1 Tikuyembekezera mwachidwi kudzayamba kuphunzira buku latsopano lakuti “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu” pa Phunziro la Baibulo la Mpingo kuyambira mlungu woyambira January 4, 2010. Kalata imene ili m’bukuli yomwe Bungwe Lolamulira linalembera wokonda Yehova aliyense inamaliza ndi mawu akuti: “Sitikukayikira kuti buku lino likuthandizani kupitiriza kugwiritsa ntchito choonadi pa moyo wanu, ndipo zimenezi zikuthandizani kukhalabe ‘m’chikondi cha Mulungu . . . pokhala ndi cholinga cha moyo wosatha.’—Yuda 21.”
2. Kodi buku latsopanoli lidzatithandiza pa nkhani ziti?
2 Zimene Tiyenera Kuyembekezera: Kodi mfundo za m’Baibulo zingatithandize bwanji pa nkhani zokhudza anthu ocheza nawo, zosangalatsa, kulemekeza amene ali ndi udindo, zizolowezi zathu, ukwati, zimene timalankhula ndiponso miyambo? Chikumbumtima chathu chidzaumbidwa kuti chizigwirizana ndi mfundo zolungama zimene zili m’Mawu a Mulungu. (Sal. 19:7, 8) Tikamamvetsa bwino mmene Yehova amaganizira, timakhala ofunitsitsa kum’kondweretsa ndipo zimenezi zimatilimbikitsa kukhala omvera pa chilichonse chimene timachita pa moyo wathu.—Miy. 27:11; 1 Yoh. 5:3.
3. N’chifukwa chiyani tiyenera kudzayesetsa kuyankha nawo pa phunziro la mlungu uliwonse?
3 Konzekerani Kudzayankha Nawo: Mukamakonzekera khalani ndi cholinga chotamanda Mulungu pakati pa anthu ake. (Aheb. 13:15) Mpingo wonse uzidzaphunzira limodzi buku latsopanoli. Mlungu uliwonse tizidzaphunzira ndime zochepa, choncho aliyense adzakwanitsa kukonzekera bwino. Ndipo zimenezi zidzatithandiza kulimba mtima kuti tifotokoze zimene taphunzira. Ndemanga zathu zazifupi ndiponso zokonzedwa bwino zidzalimbikitsa ena kusonyeza chikondi ndi kuchita ntchito zabwino ndiponso zidzathandiza kuti phunziro lathu lidzakhale losangalatsa ndi lopindulitsa. (Aheb. 10:24) Komanso tonsefe tidzasangalala kwambiri tikamadzapereka ndemanga zosonyeza chikhulupiriro chathu.
4. N’chifukwa chiyani tifunika kutsatira malamulo a Yehova?
4 Pa usiku wake womaliza padziko lino lapansi, Yesu ananena kuti kutsatira malamulo a Yehova n’kofunika kuti munthu akhalebe m’chikondi cha Mulungu. (Yoh. 15:10) Buku la “Chikondi cha Mulungu” lidzatithandiza kukhala otsimikiza mtima kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wathu ndiponso ‘kukhalabe m’chikondi cha Mulungu.’—Yuda 21.