Ndandanda ya Mlungu wa October 26
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 26
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 28, ndime 1 mpaka 13
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Deuteronomo 11-13
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Konzekerani Kugawira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Nkhani. Kambiranani zomwe zili m’magazini atsopano, ndipo sonyezani nkhani zimene zingakhale zochititsa chidwi m’gawo lanu. Chitani chitsanzo chimodzi chosonyeza kholo likuthandiza mwana kukonzekera utumiki. Khololo ndi mwana wake asankhe nkhani, lemba ndiponso apeze funso limene angagwiritse ntchito. Kenako mwanayo achite chitsanzo, ndipo atchule dongosolo lopereka ndalama lothandizira ntchito yathu.
Mph. 10: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Kukambirana ndi omvera. Pemphani omvera kufotokoza mitu ya m’bukuli imene atha kugwiritsa ntchito mogwira mtima m’gawo lawo. Posonyeza buku kwa mwininyumba, kodi ndi funso liti, chithunzi, kapena lemba limene anagwiritsa ntchito? Chitani chitsanzo chimodzi.
Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Kukambirana ndi omvera. Werengani ndi kukambirana malemba amene ali m’bokosi.