Mkati Mwachikuto
Kwa Wowerenga Bukuli:
Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata [kapena mtsikana] iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m’njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona.” (Mlaliki 11:9) Munthu ukakhala wachinyamata moyo umasangalatsa kwambiri. Ifenso tikufuna kuti muzisangalala. Komabe muzichita zimenezi m’njira imene Yehova Mulungu amasangalala nayo. Musaiwale kuti Mulungu amaona chilichonse chimene mukuchita pamoyo wanu ndipo adzakuweruzani mogwirizana ndi zimene mukuchitazo. Choncho, ndi nzeru kumvera malangizo amene Solomo anapereka, akuti: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo.”—Mlaliki 12:1.
Tikupempherera kuti mfundo zimene zili m’buku lino zikuthandizeni polimbana ndi mayesero amene achinyamata ambiri amakumana nawo ndiponso kuti muzichita zinthu zogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Mukamachita zimenezi mudzasangalatsa mtima wa Yehova.—Miyambo 27:11.
Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova