Nyimbo 4
Tipange Dzina Labwino kwa Mulungu
Losindikizidwa
1. Pamoyo wathu, Tsiku lililonse
Tipange dzina Labwino kwa M’lungu.
Tikachita ntchito Zabwino kwa M’lungu,
Tisangalatsa Mtima wake.
2. Kufunitsitsa Kutchuka m’dzikoli,
Kufuna kuti Anthu atikonde
Kulibetu phindu Chifukwa Yehova
Sangatikonde Tikatero.
3. Tifuna M’lungu Atilembe dzina
Kuti tikhale, Mu buku la moyo.
Choncho tikhaletu Ndi dzina labwino
Kwa M’lungu wathu, Nthawi zonse.
(Onaninso Gen. 11:4; Miy. 22:1; Mal. 3:16; Chiv. 20:15.)