Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • hf gawo 5 mbali 1-2
  • Zimene Mungachite Kuti Muzigwirizana ndi Achibale

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Mungachite Kuti Muzigwirizana ndi Achibale
  • Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • 1 MUZIWALEMEKEZA
  • 2 MUZIKHALA NDI MALIRE
  • Muzikhala Okhulupirika
    Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Muzidalira Kwambiri Mulungu
    Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Muzilemekeza Mwamuna Kapena Mkazi Wanu
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Pambuyo pa Tsiku la Ukwati
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
Onani Zambiri
Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
hf gawo 5 mbali 1-2
Apongozi sakusangalala ndi mmene mpongozi wawo akuphikira zakudya

MUTU 5

Zimene Mungachite Kuti Muzigwirizana ndi Achibale

“Valani . . . kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima.”—Akolose 3:12

N’zoona kuti mukakwatirana, mumakondabe makolo anu koma munthu wofunika kwambiri tsopano ndi mwamuna kapena mkazi wanu. Achibale ena angavutike kuvomereza zimenezi. Koma mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni kuti mupitirize kugwirizana ndi achibale anu pamene mukulimbitsa banja lanu latsopano.

1 MUZIWALEMEKEZA

Mwamuna ndi mkazi wake akukaona makolo awo

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.” (Aefeso 6:2) Kaya muli ndi zaka zingati, muyenera kulemekezabe makolo anu. Muzikumbukira kuti mwamuna kapena mkazi wanu nayenso ayenera kulemekeza makolo ake. Pajatu “chikondi sichichita nsanje,” choncho simuyenera kuchita nsanje ngati mnzanuyo amagwirizana kwambiri ndi makolo ake.—1 Akorinto 13:4; Agalatiya 5:26.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muzipewa kunena mawu ngati akuti, “Achibale ako amandiderera nthawi zonse” kapena akuti, “Nthawi zonse, mayi ako sasangalala ndi zimene ndimachita”

  • Yesetsani kumvetsa maganizo a mwamuna kapena mkazi wanu

2 MUZIKHALA NDI MALIRE

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Mukalowa m’banja, makolo anu angaonebe kuti ayenera kukusamalirani ndipo angayambe kulowerera banja lanu.

Choncho inuyo ndi mwamuna kapena mkazi wanu muyenera kukambirana malire a zimene makolo anu angachite n’kuwafotokozera mokoma mtima. Muziwafotokozera momasuka ndiponso mosabisa mawu koma mwaulemu. (Miyambo 15:1) Makhalidwe monga kudzichepetsa, kufatsa komanso kuleza mtima angakuthandizeni kuti muzigwirizana ndi achibale anu komanso kukhala ololera pochita nawo zinthu.—Aefeso 4:2.

Mwamuna ndi mkazi wake akukambirana; mwamuna ndi mkazi wake akupatsa makolo awo mphatso

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Ngati mukuona kuti achibale akulowerera kwambiri banja lanu, muyenera kupeza nthawi yabwino n’kukambirana ndi mwamuna kapena mkazi wanu

  • Muyenera kugwirizana zimene mungachite pothana ndi vutoli

MUZIWAMVETSA

Muziyesetsa kumvetsa maganizo a makolo anu komanso mmene akumvera mumtima mwawo. Iwo amakukondani kwambiri ndipo cholinga chawo si kusokoneza banja lanu. Kungoti zingawavute kuvomereza kuti mwayamba kudziimira panokha. Nthawi zina angaganize kuti mwasiya kuwawerengera. Kutsatira mfundo za m’Baibulo komanso kukambirana momasuka kungakuthandizeni kuti muzigwirizana ndi makolo anu popanda kusokoneza banja lanu.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • N’chifukwa chiyani m’pomveka kuti makolo amachita chidwi ndi zimene tikuchita m’banja lathu?

  • Kodi ndingasonyeze bwanji kuti mwamuna kapena mkazi wanga ndi wofunika kwambiri popanda kunyalanyaza makolo anga?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena