NYIMBO 89
Mvera Kuti Udalitsidwe
Losindikizidwa
1. Kodi timamveradi Yesu Khritsu
Pa zonse zimene ananena?
Zomwe anaphunzitsa ndi zabwino.
Tikamumvera tidalitsidwa.
(KOLASI)
Mvera udalitsidwe
Kuti usangalale.
Zomwe Mulungu angakuuze,
Mvera udalitsidwe.
2. Monga nyumba yomangidwa pathanthwe
Osati yomangidwa pamchenga,
Zochita zathu zingatiteteze
Ngati timamvera Yesu Khristu.
(KOLASI)
Mvera udalitsidwe
Kuti usangalale.
Zomwe Mulungu angakuuze,
Mvera udalitsidwe.
3. Monga mtengo wamumbali mwa madzi
Umabereka mu nyengo yake,
Tikamamvera tidzadalitsidwa.
Tidzalandira moyo wosatha.
(KOLASI)
Mvera udalitsidwe
Kuti usangalale.
Zomwe Mulungu angakuuze,
Mvera udalitsidwe.
(Onaninso Deut. 28:2; Sal. 1:3; Miy. 10:22; Mat. 7:24-27; Luka 6:47-49.)