Mmene Mungagwiritsire Ntchito Kabukuka
M’masamba otsatirawa muona kuti tsiku lililonse lili ndi lemba lake komanso ndemanga yake. Ngakhale kuti mukhoza kupanga lemba la tsiku nthawi ina iliyonse, ena amaona kuti zimakhala zothandiza kwambiri kupanga m’mawa. Zimenezi zimawathandiza kuti aziganizira mfundo za m’lembalo tsiku lonse. Kupanga lemba la tsiku ndi banja lanu n’kothandizanso kwambiri. Anthu otumikira pa Beteli padziko lonse amakambirana lemba la tsiku pa nthawi ya chakudya cham’mawa.
Ndemanga zomwe zili m’kabukuka zinatengedwa mu Nsanja ya Olonda (w) yophunzira kuyambira ya mwezi wa April 2015 mpaka March 2016. Manambala olembedwa kumapeto kwa deti la magazini a Nsanja ya Olonda, akusonyeza nambala ya nkhani yophunzira (1, 2, 3, 4 kapena 5) ya m’magaziniyo. Kenako pali nambala ya ndime imene ndemangayo yachokera. (Onani chitsanzo chili m’munsichi.) Komanso mungapeze mfundo zambiri mu nkhani imene mwachokera ndemangayo. Kuti mudziwe tsamba limene nkhani iliyonse yayambira, onani tsamba 2 mu Nsanja ya Olonda imene nkhaniyo yachokera.