Lachisanu
“Khala wolimba mtima kwambiri ndipo uchite zinthu mwamphamvu”—YOSWA 1:7
M’MAWA
9:20 Kuonera Vidiyo ya Nyimbo
9:30 Nyimbo Na. 110 ndi Pemphero
9:40 NKHANI YA TCHEYAMANI: Yehova Ndi Amene Amatithandiza Kuti Tikhale Olimba Mtima (Salimo 28:7; 31:24; 112:7, 8; 2 Timoteyo 1:7)
10:10 NKHANI YOSIYIRANA: N’chifukwa Chiyani Akhristu Oona Amafunika Kulimba Mtima?
Kuti Azilalikira (Chivumbulutso 14:6)
Kuti Akhalebe Oyera (1 Akorinto 16:13, 14)
Kuti Asamalowerere Ndale (Chivumbulutso 13:16, 17)
11:05 Nyimbo Na. 126 ndi Zilengezo
11:15 KUWERENGA BAIBULO MWA SEWERO: “Limba Mtima, Ugwire Ntchitoyi Mwamphamvu”! (1 Mbiri 28:1-20; 1 Samueli 16:1-23; 17:1-51)
11:45 “Chida Chilichonse Chimene Chidzapangidwe Kuti Chikuvulaze Sichidzapambana” (Yesaya 54:17; Salimo 118:5-7)
12:15 Nyimbo Na. 61 ndi Kupuma
MASANA
1:25 Kuonera Vidiyo ya Nyimbo
1:35 Nyimbo Na. 69
1:40 NKHANI YOSIYIRANA: Zinthu Zolepheretsa Kukhala Wolimba Mtima Ndiponso Zinthu Zothandiza Kukhala Wolimba Mtima
Kutaya Mtima Ndiponso Chiyembekezo (Salimo 27:13, 14)
Mtima Wodandaula Ndiponso Mtima Woyamikira (Salimo 27:1-3)
Zosangalatsa Zosayenera Ndiponso Kulowa mu Utumiki (Salimo 27:4)
Kugwirizana Ndi Anthu Oipa Ndiponso Kugwirizana Ndi Anthu Abwino (Salimo 27:5; Miyambo 13:20)
Nzeru za Dziko Ndiponso Kuphunzira Patokha (Salimo 27:11)
Kukayikira Ndiponso Chikhulupiriro (Salimo 27:7-10)
3:10 Nyimbo Na. 55 ndi Zilengezo
3:20 NKHANI YOSIYIRANA: Anadalitsidwa Chifukwa Chokhala Okonzeka Kukumana Ndi Mavuto
Hananiya, Misayeli ndi Azariya (Danieli 1:11-13; 3:27-29)
Akula ndi Purisikila (Aroma 16:3 4)
Sitefano (Machitidwe 6:11, 12)
3:55 “Limbani Mtima. Ine Ndaligonjetsa Dziko” (Yohane 16:33; 1 Petulo 2:21, 22)
4:15 Asilikali Olimba Mtima a Khristu (2 Akorinto 10:4, 5; Aefeso 6:12-18; 2 Timoteyo 2:3, 4)
4:50 Nyimbo Na. 22 ndi Pemphero Lomaliza