Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es20 tsamba 88-98
  • September

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • September
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2020
  • Timitu
  • Lachiwiri, September 1
  • Lachitatu, September 2
  • Lachinayi, September 3
  • Lachisanu, September 4
  • Loweruka, September 5
  • Lamlungu, September 6
  • Lolemba, September 7
  • Lachiwiri, September 8
  • Lachitatu, September 9
  • Lachinayi, September 10
  • Lachisanu, September 11
  • Loweruka, September 12
  • Lamlungu, September 13
  • Lolemba, September 14
  • Lachiwiri, September 15
  • Lachitatu, September 16
  • Lachinayi, September 17
  • Lachisanu, September 18
  • Loweruka, September 19
  • Lamlungu, September 20
  • Lolemba, September 21
  • Lachiwiri, September 22
  • Lachitatu, September 23
  • Lachinayi, September 24
  • Lachisanu, September 25
  • Loweruka, September 26
  • Lamlungu, September 27
  • Lolemba, September 28
  • Lachiwiri, September 29
  • Lachitatu, September 30
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2020
es20 tsamba 88-98

September

Lachiwiri, September 1

Ngakhale kuti simunamuonepo, mumamukonda.​—1 Pet. 1:8.

Yesu anamvera chisoni Marita ndi Mariya. Mwachitsanzo, “Yesu anagwetsa misozi” ataona azimayi awiriwa ali ndi chisoni chifukwa cha imfa ya Lazaro. (Yoh. 11:32-35) Sikuti analira chifukwa choti mnzake wapamtima wamwalira. Tikutero chifukwa chakuti ankadziwa zoti amuukitsa. Koma analira chifukwa chokhudzidwa ndi chisoni cha anzakewo. Mfundo yakuti Yesu ali ndi mtima woganizira ena ndi yolimbikitsa kwambiri. N’zoona kuti ife si angwiro ngati mmene iye analili. Koma timasangalala tikaganizira mmene iye ankachitira zinthu ndi anthu. Timasangalalanso kudziwa kuti panopa Yesu ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo posachedwapa athetsa mavuto onse. Popeza nayenso anakhalapo munthu, iye ndi woyenera kwambiri kuthandiza anthu m’njira yabwino kuti aiwale mavuto onse amene akumana nawo mu ulamuliro wa Satana. Ndi mwayi waukulu kukhala ndi Wolamulira amene ‘angatimvere chisoni pa zofooka zathu.’​—Aheb. 2:17, 18; 4:15, 16. w19.03 17 ¶12-13

Lachitatu, September 2

Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine.​—Yoh. 6:44.

Tizikumbukira kuti mbali yathu pa ntchito yothandiza anthu kuti aphunzire za Mulungu ndi yochepa kwambiri. (1 Akor. 3:6, 7) Yehova ndi amene amakokera anthu m’gulu lake. Ndipo pamapeto pake, munthu aliyense amalandira kapena kukana uthenga wabwino malinga ndi mmene mtima wake ulili. (Mat. 13:4-8) Tizikumbukiranso kuti Yesu anali Mphunzitsi wabwino kwambiri koma anthu ambiri sanalandire uthenga wake. Choncho tisamakhumudwe ngati anthu ena sanatilandire bwino. Tikamasonyeza chifundo mu utumiki zotsatira zake zimakhala zabwino ndipo utumikiwo umakhala wosangalatsa. Paja Baibulo limanena kuti munthu amakhala ndi chimwemwe ngati ali wopatsa. Tikamalalikira timapereka uthenga wabwino kwa anthu amene ali ndi maganizo oyenera moyo wosatha. (Mac. 13:48) Choncho “ngati tingathe, tiyeni tichitire onse zabwino.” (Agal. 6:10) Tikatero tidzakhala osangalala podziwa kuti tikulemekeza Atate wathu wakumwamba.​—Mat. 5:16. w19.03 25 ¶18-19

Lachinayi, September 3

Ndidzakutamandani pakati pa mpingo.​—Sal. 22:22.

Mfumu Davide analemba kuti: “Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kutamandidwa kwambiri.” (Sal. 145:3) Iye ankakonda Yehova ndipo zimenezi zinamulimbikitsa kuti azimutamanda “pakati pa mpingo.” (1 Mbiri 29:10-13; Sal. 40:5) Tikamayankha pamisonkhano timakhala tikutamanda Yehova. Tonsefe timasangalala tikamva ndemanga zosiyanasiyana pamisonkhano. Mwachitsanzo, mawu ochepa amene mwana amayankha mochokera pansi pa mtima amatisangalatsa. Timalimbikitsidwanso munthu akafotokoza mfundo yosangalatsa imene waphunzira. Timayamikiranso anthu amene amalimba mtima n’kuyankha ngakhale kuti ndi amanyazi kapena akuphunzira chilankhulo chathu. (1 Ates. 2:2) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zimene achita? Misonkhano ikatha, tikhoza kuwathokoza chifukwa cha ndemanga zawo zolimbikitsa. Tingasonyezenso kuyamikira ndemanga zawo tikamapereka ndemanga zathu. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti sitikufuna kungolimbikitsidwa koma nafenso tikufuna kulimbikitsa anthu ena.​—Aroma 1:11, 12. w19.01 8 ¶1-2; 9 ¶6

Lachisanu, September 4

Sonyezani kuti ndinu oyamikira.​—Akol. 3:15.

Tsiku lina anthu 10 amene ankadwala khate anaona Yesu akubwera. Anthuwa analibe mtengo wogwira koma anali atamva kuti Yesu amachiritsa anthu odwala matenda osiyanasiyana ndipo ankakhulupirira kuti awathandiza. Choncho anafuula kuti: “Yesu, Mlangizi, tichitireni chifundo!” Yesu anachiritsadi anthuwa. N’zosachita kufunsa kuti onsewa anayamikira zimene Yesu anawachitira. Koma mmodzi wa iwo, yemwe anali wochokera ku Samariya sanangoyamikira mumtima. Iye anapita kwa Yesu kukathokoza. Munthuyo anakhudzidwa mumtima moti anatamanda Mulungu “mokweza mawu.” (Luka 17:12-19) Ifenso tiyenera kuthokoza munthu aliyense amene watichitira zinthu mokoma mtima. Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yoyamikira. Njira ina imene amachitira zimenezi ndi kupereka mphoto kwa anthu amene amachita zinthu zomusangalatsa. (2 Sam. 22:21; Sal. 13:6; Mat. 10:40, 41) Malemba amatilimbikitsa kuti ‘tizitsanzira Mulungu monga ana ake okondedwa.’ (Aef. 5:1) Choncho chifukwa chachikulu chotichititsa kuyamikira n’chakuti timafuna kutsanzira Yehova. w19.02 14 ¶1-2; 15 ¶4

Loweruka, September 5

Sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.​—Yobu 27:5.

Mlongo wachitsikana ali kusukulu ndipo akukana mwaulemu kuti achite zinthu zina zokhudza holide imene sisangalatsa Mulungu. M’bale wachinyamata, yemwe ndi wamanyazi, akulalikira kunyumba ndi nyumba ndipo akupita kunyumba ya mnzake wakusukulu yemwe amanyoza a Mboni za Yehova. M’bale wina akugwira ntchito mwakhama kuti apezere banja lake zofunika pa moyo ndipo abwana ake amupempha kuti achite zinthu zina zachinyengo. Ngakhale kuti akhoza kuchotsedwa ntchito, m’baleyo akufotokozera abwana akewo kuti ayenera kuchita zinthu moona mtima ndiponso kumvera malamulo a boma chifukwa ndi zimene Mulungu amafuna. (Aroma 13:1-4; Aheb. 13:18) Kodi anthu atatuwa asonyeza khalidwe liti? Mwina mwaona kuti asonyeza makhalidwe monga kulimba mtima komanso kuona mtima. Koma khalidwe lina lofunika kwambiri limene asonyeza ndi kukhala ndi mtima wosagawanika. Aliyense wasonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa Yehova. Tikutero chifukwa chakuti wakana kuchita zinthu zosemphana ndi mfundo za Mulungu. Iwo akwanitsa kukana chifukwa chokhala ndi mtima wosagawanika. Yehova akhoza kusangalala kwambiri ndi zimene aliyense wa anthuwa anachita. Nafenso tiziyesetsa kusangalatsa Atate wathu wakumwamba. w19.02 2 ¶1-2

Lamlungu, September 6

Chilamulo ndicho mthunzi chabe wa zinthu zabwino zimene zikubwera.​—Aheb. 10:1.

Chilamulo chinkateteza makamaka anthu amene sankatha kudziteteza monga ana ndi akazi amasiye komanso alendo. Oweruza a ku Isiraeli anauzidwa kuti: “Usapotoze chiweruzo cha mlandu wa mlendo kapena mlandu wa mwana wamasiye, ndipo usalande mkazi wamasiye chovala chake monga chikole.” (Deut. 24:17) Yehova ankaganizira kwambiri anthu amene ankaponderezedwa mosavuta. Ndipo ankalanga anthu amene ankawapondereza. (Eks. 22:22-24) Yehova amafuna kuti anthu amene wawapatsa udindo azichita zinthu mwachikondi ndi anthu amene akuwayang’anira. Iye amadana ndi nkhanza zokhudza kugonana ndipo amafuna kuti anthu onse, makamaka amene angaponderezedwe mosavuta, azitetezedwa komanso kuchitiridwa zinthu mwachilungamo. (Lev. 18:6-30) Tikamaona kuti Yehova amatichitira zinthu mwachilungamo timayamba kumukonda kwambiri. Ndipo tikamakonda Yehova ndi mfundo zake zachilungamo, timalimbikitsidwa kukonda anzathu komanso kuwachitira zinthu mwachilungamo. w19.02 24-25 ¶22-26

Lolemba, September 7

[Kanani] moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko.​—Tito 2:12.

Taganizirani chitsanzo cha mmene tingadzitetezere kuti tisasokonezedwe ndi maganizo a Satana. Yehova watiphunzitsa kuti ‘dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse zisatchulidwe n’komwe pakati pathu.’ (Aef. 5:3) Koma kodi tingatani ngati anzathu akuntchito kapena kusukulu ayamba kulankhula za chiwerewere? Chikumbumtima chathu, chomwe chili ngati mlonda, chikhoza kutichenjeza. (Aroma 2:15) Ndiye kodi zikatero, tingachimvere? Mwina tikhoza kukopeka n’kuyamba kumvetsera nkhani zawozo kapena kuona nawo zithunzi zimene akuona. Koma chofunika pa nthawi ngati imeneyi ndi kusintha mwamsanga nkhani kapena kuchokapo. Tikatero timakhala ngati tikutseka mageti a mtima wathu. Timafunika kulimba mtima kuti tisamangotengera maganizo kapena zochita za anzathu. Chosangalatsa n’chakuti Yehova amaona zimene tikuyesetsa kuchita ndipo amatipatsa mphamvu komanso nzeru zotithandiza kuti tisamatengere maganizo a Satana.​—2 Mbiri 16:9; Yes. 40:29; Yak. 1:5. w19.01 17-18 ¶12-13

Lachiwiri, September 8

Ineyo ndinaganizira ntchito zonse zimene manja anga anagwira . . . ndinaona kuti zonse zinali zachabechabe.​—Mlal. 2:11.

Solomo, yemwe anali wachuma kwambiri komanso mfumu, anasankha zoti ‘ayesereko kusangalala komanso kupeza zinthu zabwino.’ (Mlal. 2:1-10) Iye anamanga nyumba, kudzala mitengo ndi maluwa okongola ndiponso kuchita chilichonse chimene ankafuna. Kodi atachita zimenezi anamva bwanji? Kodi anakhala wosangalala? Mawu amulemba la leroli akufotokoza zimene Solomo analemba yekha. Kodi inuyo mukuphunzirapo chiyani pa nkhani ya Solomoyi? Yehova safuna kuti muziphunzira nkhwangwa ili m’mutu. Koma pamafunika chikhulupiriro champhamvu kuti muzimvera Mulungu komanso kuika zofuna zake pamalo oyamba. Mukamasankha zochita chifukwa chokhulupirira Yehova simudzanong’oneza bondo ngakhale pang’ono. Ndipotu Yehova sadzaiwala ‘chikondi chimene mumachisonyeza pa dzina lake.’ (Aheb. 6:10) Choncho yesetsani kulimbitsa chikhulupiriro chanu ndipo mudzaona nokha kuti Yehova amakufunirani zabwino.​—Sal. 32:8. w18.12 22 ¶14-15

Lachitatu, September 9

Mulungu akuonetsa chikondi chake kwa ife, moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.​—Aroma 5:8.

Munthu wauzimu amakhulupirira Mulungu ndipo amaona zinthu mmene iye amazionera. Amadalira malangizo a Yehova ndipo amamumvera. (1 Akor. 2:12, 13) Davide ndi chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iye anaimba kuti: “Yehova ndiye gawo langa, gawo limene ndinapatsidwa, komanso chikho changa.” (Sal. 16:5) Ponena mawu oti “gawo” Davide ankatanthauza zinthu monga ubwenzi wake ndi Mulungu amene iye ankamuona ngati pothawirapo pake. (Sal. 16:1) Kodi zotsatira zake zinali zotani? Iye analemba kuti: “Moyo wanga ukukondwera.” Mawu amenewa akusonyeza kuti palibe chimene chinkamusangalatsa kwambiri kuposa ubwenzi wake ndi Yehova. (Salimo 16:9, 11) Anthu amene amangokhalira kufunafuna chuma ndi zosangalatsa sangakhale osangalala ngati mmene Davide ankachitira. (1 Tim. 6:9, 10) Kukhulupirira Yehova komanso kumutumikira kungakuthandizeni kuti muzikhala osangalala. Ndiye kodi mungatani kuti mukhale ndi chikhulupiriro cholimba? Muzipeza nthawi yoti mudziwe bwino Yehova. Mungachite zimenezi powerenga Mawu ake, kuona chilengedwe chake komanso kuganizira makhalidwe ake monga chikondi chimene amakusonyezani.​—Aroma 1:20. w18.12 25 ¶7-8

Lachinayi, September 10

Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse.​—Aheb. 13:4.

Apa sikuti Paulo ankangotchula mfundo basi. Lembali likulamula Akhristu kuti azilemekeza ukwati n’kumaona kuti ndi wamtengo wapatali. Kodi umu ndi mmene inuyo mumaonera ukwati? Ngati muli pa banja, kodi mumalemekeza ukwati wanu? Yesu ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yolemekeza ukwati. Afarisi atamufunsa nkhani yothetsa banja, iye anafotokoza zimene Mulungu ananena zokhudza ukwati wa anthu oyambirira. Paja Mulungu anati: “Pa chifukwa chimenechi, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.” Ndiyeno Yesu anapitiriza kuti: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Maliko 10:2-12; Gen. 2:24) Yesu anasonyeza kuti Mulungu ndi amene anayambitsa ukwati ndipo anatsindika kuti suyenera kutha. Paja Mulungu sanauze Adamu ndi Hava kuti iwo akhoza kuthetsa banja lawo. Zimene zinachitika mu Edeni zimasonyeza kuti ukwati ndi mgwirizano wosatha wa pakati pa mwamuna mmodzi ndi mkazi mmodzi. w18.12 10-11 ¶2-4

Lachisanu, September 11

Sandulikani mwa kusintha maganizo anu.​—Aroma 12:2.

Tikayamba kuphunzira choonadi, timaphunzira kufunika komvera malamulo akuluakulu a Yehova. Koma tikamakula mwauzimu, timayamba kudziwa maganizo a Yehova, zimene amakonda, zimene amadana nazo komanso mmene amaonera zinthu zosiyanasiyana. Ndiye tikayamba kuona zinthu mmene iye amaonera n’kumachita zinthu mogwirizana ndi maganizo ake zimakhala kuti tayamba kuyendera maganizo akewo. Kutengera maganizo a Yehova kumakhala kosangalatsa koma si kophweka. Popeza si ife angwiro, nthawi zina zimativuta. Mwachitsanzo, tikhoza kuvutika kumvetsa maganizo a Yehova pa nkhani ya makhalidwe abwino, chuma, ntchito yolalikira, kugwiritsa ntchito magazi ndi nkhani zina. Ndiye kodi zikatero tiyenera kuchita chiyani? Kodi tingatani kuti tipitirize kuyendera maganizo a Yehova? Tiyenera kuphunzira Mawu a Mulungu n’cholinga choti tizindikire maganizo a Yehova, tiwaganizire kwambiri ndipo tiyambe kuwatengera. w18.11 23-24 ¶2-4

Loweruka, September 12

Kodi ndidzapempha thandizo kuti mundipulumutse ku chiwawa koma inu osandimva kufikira liti?—Hab. 1:2.

Habakuku anakhala ndi moyo pa nthawi yovuta kwambiri. Iye anakhumudwa chifukwa anthu ambiri anali oipa komanso ankhanza. Ndiye Habakuku ankati akaona kupanda chilungamo komanso kuzunzana kwa anthu ankadzifunsa kuti, ‘Kodi zoipazi zidzatha liti? N’chifukwa chiyani Yehova watenga nthawi yaitali asanathetse zoipa?’ Habakuku atasowa mtengo wogwira anapemphera kwa Yehova kuti athandizepo. Mwina iye anafika poganiza kuti Yehova sankamvera chisoni anthu amene akuvutikawo chifukwa zinaoneka ngati akuchedwa kuwathandiza. Muyenera kuti mukumvetsa mmene Habakuku ankamvera mumtima mwake. Koma kodi Habakuku anasiya kukhulupirira Mulungu? Kodi anayamba kuganiza kuti malonjezo a Mulungu sangakwaniritsidwe? Ayi. Umboni wake ndi wakuti anafotokozera Mulungu zimene zinkamudetsa nkhawa osati anthu. Zikuoneka kuti chimene chinkamudetsa nkhawa ndi nthawi imene inadutsa Mulungu asanathandize anthu kapena chifukwa chimene Mulunguyo analolera kuti iye avutike choncho. w18.11 14 ¶4-5

Lamlungu, September 13

Lekani kudziunjikira chuma padziko lapansi.​—Mat. 6:19.

Yesu ataitana Petulo ndi Andireya kuti akhale “asodzi a anthu,” nthawi yomweyo “anasiya maukonde awo.” (Mat. 4:18-20) Sikuti aliyense amene amaphunzira choonadi masiku ano amafunika kusiya ntchito yake. Paja anthufe timakhalanso ndi maudindo ena. (1 Tim. 5:8) Koma mfundo ndi yakuti munthu amene akuphunzira choonadi amafunika kusintha maganizo ake pa nkhani ya chuma komanso zimene amaziona kuti n’zofunika kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene anachita mtsikana wina dzina lake Maria. Iye ankasewera gofu kuyambira ali wamng’ono, asanayambe n’komwe sukulu. Ankasewerabe mpaka pamene anapita kusekondale, moti anapeza mwayi wolipiriridwa kuyunivesite. Iye ankakonda masewerawa moti ankafuna kuti adzakhale katswiri. Kenako Maria anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anayamba kukonda kwambiri zimene ankaphunzira. Iye ankasangalala chifukwa choonadi chinamuthandiza kusintha zinthu zambiri. Kenako anazindikira kuti n’zosatheka kuti akule mwauzimu uku akusakasaka chuma. (Mat. 6:24) Choncho analolera kusiya mtima wofuna kukhala katswiri wa gofu. Panopa iye akuchita upainiya. Mariya akuona kuti anasankha bwino moti anati panopa “moyo wake ndi wabwino kwambiri.” w18.11 5-6 ¶9-10

Lolemba, September 14

[Iye ndi] mmisiri wamatabwa, mwana wa Mariya.​—Maliko 6:3.

Ali ndi zaka 30, Yesu anasiya ukalipentala chifukwa ankaona kuti ntchito yophunzitsa anthu inali yofunika kwambiri. Iye ananena kuti chifukwa china chimene Mulungu anamutumizira padzikoli chinali choti adzalengeze uthenga wabwino wa Ufumu. (Mat. 20:28; Luka 3:23; 4:43) Choncho pa moyo wake wonse, Yesu ankaona kuti ntchito yophunzitsa anthu ndi yofunika kwambiri ndipo ankafuna kuti anthu ena azigwira nawonso ntchito imeneyi. (Mat. 9:35-38) Mwina ife si akalipentala koma tonsefe timagwira ntchito yophunzitsa anthu uthenga wabwino. Ntchito imeneyi ndi yofunika kwambiri chifukwa timaigwira ndi Mulungu. Paja Baibulo limati ndife “antchito anzake.” (1 Akor. 3:9; 2 Akor. 6:4) Koma timadziwanso kuti mawu onse a Yehova “ndi choonadi chokhachokha.” (Sal. 119:159, 160) N’chifukwa chake tiyenera kuyesetsa ‘kuphunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi.’ (2 Tim. 2:15) Choncho tiyenera kukulitsa luso lathu pogwiritsa ntchito Baibulo chifukwa ndi limene timaligwiritsa ntchito kwambiri pophunzitsa anthu za Yehova, Yesu ndi Ufumu. w18.10 11 ¶1-2

Lachiwiri, September 15

Muthandize ofookawo, ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu.​—Mac. 20:35.

Mwamuna akamatsanzira Yesu Khristu, yemwe ndi mutu wake, amathandiza mkazi wake kuti ‘azimulemekeza kwambiri.’ (Aef. 5:22-25, 33) Ulemu umenewo ungathandize kuti nayenso mkaziyo azichita zinthu moganizira mwamuna wake. Makolo akamachita zinthu moganizirana amapereka chitsanzo chabwino kwa ana awo. Makolo ali ndi udindo wophunzitsa ana awo kuti azichita zinthu moganizira ena. Mwachitsanzo, angawaphunzitse kuti asamathamangethamange m’Nyumba ya Ufumu. Angawaphunzitsenso kuti akapita kokacheza azichita zinthu mwaulemu pa nthawi yachakudya. Mwana akatichitira zinthu zabwino tiyenera kumuthokoza. Zimenezi zingathandize anawo kuzindikira kuti “kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” w18.09 29 ¶5-6

Lachitatu, September 16

Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu.​—Mat. 23:10.

Tikaganizira zimene Mfumu yathu Yesu Khristu akuchita potitsogolera timadziwiratu kuti iye akuganizira kwambiri zam’tsogolo. Choncho tizisangalala ndi madalitso amene timapeza chifukwa cha zinthu zimene zasintha m’gulu la Yehova. Mukhoza kulimbikitsidwa mukamakambirana pa kulambira kwa pabanja ubwino umene timapeza chifukwa cha zimene zasinthidwa pamisonkhano yathu kapena mu utumiki. Tikazindikira cholinga cha malangizo amene timapatsidwa m’gulu la Yehova komanso ubwino wake, tikhoza kuwatsatira mosavuta. Mwachitsanzo, chiwerengero cha mabuku amene amasindikizidwa chinachepetsedwa chifukwa tikugwiritsa ntchito zipangizo zamakono. Zimenezi zathandiza kuti gulu lisamawononge ndalama zambiri komanso kuti ntchito ya Ufumu iziyenda bwino padziko lonse. Choncho tingachite bwino kugwiritsa ntchito kwambiri zipangizo zamakono pophunzira kapena mu utumiki ngati n’zotheka. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tikuyesetsa kutsatira Khristu pa nkhani yogwiritsa ntchito mwanzeru zinthu za gulu. Tikamatsatira Khristu mokhulupirika timalimbitsa chikhulupiriro cha anzathu ndipo timakhala ogwirizana. w18.10 25-26 ¶17-19

Lachinayi, September 17

Popeza timakukondani kwambiri, tinali okonzeka kukupatsani uthenga wabwino wa Mulungu. Ndipotu osati uthenga wokha ayi, komanso miyoyo yathu yeniyeniyo.​—1 Ates. 2:8.

Tikamakhala achifundo ngati Mulungu, iye akhoza kutigwiritsa ntchito poyankha mapemphero a anthu amene ali ndi nkhawa. (2 Akor. 1:3-6) Tiyenera kuona abale ndi alongo athu moyenera. Munthu akamaganiza kuti Akhristu anzake sangalakwitse kalikonse ndiye kuti akuyembekezera zinthu zosatheka ndipo akhoza kukhumudwa. (Mlal. 7:21, 22) Tizikumbukira kuti Yehova sayembekezera kuti atumiki ake achite zimene sangakwanitse. Tikamamutsanzira, tidzakhala ololera ngati ena alakwitsa zinazake. (Aef. 4:2, 32) M’malo mowachititsa kuganiza kuti akulephera kuchita zinthu zina, ndi bwino kuwayamikira pa zomwe akuchita. Tikamatero tidzawalimbikitsa kwambiri. Tikamayamikira abale ndi alongo athu timawalimbikitsa ndiponso kuwathandiza kuti azisangalala ndi utumiki wawo.​—Agal. 6:4. w18.09 16 ¶16-17

Lachisanu, September 18

Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha amene anandituma ndi kutsiriza ntchito yake.​—Yoh. 4:34.

Yesu ankaona kuti kutsatira malangizo a Mulungu kunali ngati kudya chakudya chauzimu. Kodi n’chifukwa chiyani ananena zimenezi? Munthu akadya chakudya chabwino amapeza mphamvu komanso amasangalala. N’chimodzimodzinso ndi chakudya chauzimu. Tikutero chifukwa tikamachita zimene Mulungu amafuna timapeza mphamvu komanso timalimbitsa chikhulupiriro chathu. Munthu akamatsatira malangizo ochokera kwa Mulungu amasonyeza kuti ndi wanzeru. (Sal. 107:43) Ndipo munthu akamachita zinthu mwanzeru amapeza madalitso ambiri. Pofotokoza za nzeru, Baibulo limanena kuti: “Zonse zimene umakonda sizingafanane nazo. . . . Munthu akagwiritsitsa nzeru, zidzakhala ngati mtengo wa moyo kwa iye, ndipo ozigwiritsitsa adzatchedwa odala.” (Miy. 3:13-18) Nayenso Yesu ananena kuti: “Ngati zimenezi mukuzidziwa, ndinu odala mukamazichita.” (Yoh. 13:17) Apa ankatanthauza kuti ophunzira ake akhoza kukhalabe osangalala akamachita zimene Yesu anawauza. Iwo ankayenera kutsatira chitsanzo chake komanso zimene ankaphunzitsa kwa moyo wawo wonse. w18.09 4 ¶4-5

Loweruka, September 19

Mulungu analenga munthu m’chifaniziro chake.​—Gen. 1:27.

Mulungu anapatsa Adamu ndi Hava malangizo amene akanawathandiza kuganizira za ena ngakhale kuti pa nthawiyo anali awiriwiri m’munda wa Edeni. Yehova anawadalitsa n’kuwauza kuti aberekane, adzaze dziko lapansi ndi kuliyang’anira. (Gen. 1:28) Popeza Yehova ankaganizira anthu amene anawalenga, Adamu ndi Hava anafunikanso kuchita zinthu moganizira ana amene adzabereke. Yehova anafuna kuti dziko lonse likonzedwe kuti likhale paradaiso n’cholinga choti ana onse a Adamu adzakhale osangalala. Kuti zimenezi zitheke panafunika kuti banja lonse lizichita zinthu mogwirizana. Anthu angwirowa anayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi Yehova kuti akwaniritse cholinga chake komanso akonze dziko kuti likhale paradaiso. Zimenezi zikanawathandizanso kuti alowe mu mpumulo wake. (Aheb. 4:11) Kunena zoona akanasangalala kwambiri kugwira ntchito imeneyi. Mtima wofuna kuthandiza enawu ukanawathandiza kuti adalitsidwe komanso azikhala osangalala. w18.08 18 ¶2; 19-20 ¶8-9

Lamlungu, September 20

Anandinenera ine mtumiki wanu miseche kwa inu mbuyanga mfumu.​—2 Sam. 19:27.

Kodi mungatani ngati anthu akunenerani zinthu zabodza? Zoterezi zinachitikiranso Yesu ndi Yohane M’batizi. (Mat. 11:18, 19) Kodi Yesu anatani? Iye sanataye nthawi ndi kuyankha zimene anthu ankamunenazo. M’malomwake analimbikitsa anthu kuti azingoona zimene akuchita komanso kuphunzitsa kuti adziwe zoona zake. Iye anati: “Nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.” (Mat. 11:19) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene anachitazi? Ngati anthu atinenera zinthu zoipa, tikhoza kufunitsitsa kuti chilungamo chichitike komanso tikonze zinthu kuti mbiri yathu isaipe. Koma pali zinthu zina zimene tingachite. Anthu akatinenera zinthu zabodza, zochita zathu n’zimene zingathandize anthu ena kuti asakhulupirire mabodzawo. Zimene Yesu anachita zikusonyeza kuti khalidwe lathu labwino lingachititse kuti anthu aiwale zoipa zimene anthu ena anatinenera. w18.08 6 ¶11-13

Lolemba, September 21

Muziopa Yehova Mulungu wanu. Muzim’tumikira [ndi] kum’mamatira.​—Deut. 10:20.

Nkhani ya Kaini, Solomo komanso ya Aisiraeli paphiri la Sinai ikufanana pa mfundo imodzi. Onse anali ndi mpata woti ‘alape n’kutembenuka.’ (Mac. 3:19) Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova safulumira kutayiratu munthu amene walakwa. Mwachitsanzo, Yehova anakhululukira Aroni ataona kuti wasintha. Masiku anonso Yehova angatichenjeze pogwiritsa ntchito nkhani za m’Baibulo, za m’mabuku athu kapena malangizo ochokera kwa Mkhristu mnzathu. Tikamamvera machenjezo amenewa Yehova akhoza kutichitira chifundo. Koma kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova kuli ndi cholinga chake. (2 Akor. 6:1) Kumatipatsa mwayi woti tikane “moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko.” (Tito 2:11-14) Popeza tili m’dziko loipali, tizikumanabe ndi zinthu zimene zingayese chikhulupiriro chathu. Tiyeni tiziyesetsa nthawi zonse kuti tizikhala kumbali ya Yehova. w18.07 21 ¶20-21

Lachiwiri, September 22

Yehova amadziwa anthu ake.​—2 Tim. 2:19.

Kodi tingatani kuti titsimikize mumtima mwathu zokhala odziwika kwa Mulungu osati m’dzikoli? Kuti tichite zimenezi, tiyenera kukumbukira mfundo ziwiri zofunika kwambiri. Yoyamba ndi yakuti nthawi zonse Yehova amadalitsa anthu amene amamutumikira mokhulupirika. (Aheb. 6:10; 11:6) Iye amaona kuti mtumiki wake aliyense ndi wamtengo wapatali, ndipo kwa iye sichingakhale chilungamo kuiwala anthu okhulupirika. Baibulo limanena kuti iye “amadziwa njira za olungama” ndipo amadziwanso kuwapulumutsa akakhala pa mayesero. (Sal. 1:6; 2 Pet. 2:9) Mfundo yachiwiri ndi yakuti: Yehova amadalitsa anthu amene akuwadziwa m’njira imene anthuwo sankayembekezera. Malemba amasonyeza kuti anthu amene amachita zabwino n’cholinga choti angoonedwa ndi anthu sadzadalitsidwa ndi Yehova ngakhale pang’ono. Zili choncho chifukwa amakhala atalandiriratu mphoto yawo yonse. (Mat. 6:1-5) Koma Yesu ananena kuti Atate ake amayang’ana zinthu zamseri n’kuona anthu amene zochita zawo zabwino sizionekera kwa anthu ena. Iye amaona zinthu zimene anthu oterewa akuchita n’kuwadalitsa moyenerera. w18.07 9 ¶8, 10

Lachitatu, September 23

Zinthu zimene Mulungu waziyeretsa usiyiretu kuzinena kuti n’zoipitsidwa.​—Mac. 10:15.

Petulo sankamvetsa zimene mawuwo ankatanthauza. Nthawi yomweyo panafika anthu amene Koneliyo anawatuma. Ndiye Petulo atalandira malangizo ochokera kwa mzimu woyera, anapita ndi anthuwo kunyumba kwa Koneliyo. Ngati Petulo akanatengera zinthu zongooneka ndi maso, sakanalowa m’nyumba ya Koneliyo. Zili choncho chifukwa Ayuda sankalowa m’nyumba za anthu amitundu ina. Ndiye n’chifukwa chiyani Petulo anasintha maganizo n’kukalowa m’nyumba ya Koneliyo? Anatero chifukwa cha masomphenya amene anawaona komanso malangizo amene mzimu woyera unamupatsa. N’zosakayikitsa kuti Petulo anakhudzidwa mtima atamvetsera zimene Koneliyo ananena moti anati: “Ndazindikira ndithu kuti Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Mac. 10:34, 35) Apatu Petulo anamvetsa mfundo yatsopano ya choonadi imene inasintha zinthu kwambiri. w18.08 9 ¶3-4

Lachinayi, September 24

Danani ndi choipa.​—Amosi 5:15.

N’kutheka kuti timapeweratu kuchita zinthu zimene Mulungu amadana nazo. Koma nanga bwanji pa nkhani zimene palibe lamulo lake m’Baibulo? Kodi tingadziwe bwanji zimene Mulungu angasangalale nazo pa nkhani ngati zimenezi? Apa tsopano m’pamene chikumbumtima chophunzitsidwa mfundo za m’Baibulo chingatithandize. Yehova amatikonda ndipo watipatsa mfundo zimene zingatithandize kuti chikumbumtima chathu chizisankha zinthu mwanzeru. Paja iye ananena kuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo.” (Yes. 48:17, 18) Tikamaganizira kwambiri mfundo za m’Baibulo mumtima mwathu, timakhala ngati tikuphunzitsa komanso kuumba chikumbumtima chathu. Zimenezi zimathandiza kuti tizisankha zochita mwanzeru. Mfundo za Mulungu ndi mfundo zachoonadi zomwe zingagwire ntchito pa nkhani zosiyanasiyana ndipo zimathandiza kuti munthu aganizire bwino nkhani inayake kapena asankhe zochita mwanzeru. Kuti munthu amvetse mfundo, amafunika kumvetsanso maganizo a amene anazipereka komanso zifukwa zimene anaziperekera. w18.06 17 ¶5; 18 ¶8-10

Lachisanu, September 25

Kodi n’kololeka kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?—Mat. 22:17.

Anthu achipani cha Herode anayambitsa nkhaniyi poganiza kuti Yesu akanena kuti anthu asamapereke msonkho akhoza kuimbidwa mlandu woukira boma. Komanso Yesu akanena kuti n’zoyenera kuti anthu azipereka msonkho, ndiye kuti anthu akhoza kusiya kumutsatira. Yesu anapewa kusonyeza kuti ali kumbali inayake pa nkhani yamisonkho. Yesu ankadziwa kuti okhometsa misonkho ankachita zachinyengo. Koma sankafuna kuti zimenezi zimusokoneze n’kusiya nkhani yofunika kwambiri yokhudza Ufumu wa Mulungu. Iye ankadziwa kuti Ufumuwo ndi umene ungathetse mavuto onse a anthu. Pamenepatu anapereka chitsanzo chabwino kwa otsatira ake onse. Tiyenera kupewa kusonyeza kuti tili kumbali inayake pa nkhani zandale ngakhale mbaliyo itaoneka kuti ndi yabwino kwambiri. Akhristu ayenera kufunafuna Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake m’malo molimbana ndi zinthu zopanda chilungamo m’dzikoli. (Mat. 6:33) N’zosangalatsa kuti anthu amene poyamba ankakonda kwambiri zandale anasintha atakhala a Mboni za Yehova. w18.06 6 ¶9-11

Loweruka, September 26

Ana a Mulungu woona anayamba kuona kuti ana aakazi a anthu anali okongola.​—Gen. 6:2.

N’kutheka kuti Satana anawanyengerera powauza kuti agone ndi akaziwo komanso kuti akachita zimenezo adzayamba kulamulira anthu. Mwina anachita izi pofuna kusokoneza kubwera kwa ‘mbewu ya mkazi.’ (Gen. 3:15) Kaya zinthu zinalidi choncho kapena ayi, Yehova analepheretsa zolinga zake. Anabweretsa Chigumula chimene chinalepheretsa mapulani a Satana ndi ziwanda zakezo. Choncho tiyenera kusamala kwambiri ndi msampha wa chiwerewere komanso kudzikuza. Tizikumbukira kuti angelo amene anapusitsidwa ndi Satana anatumikira pamaso pa Mulungu kwa zaka zambirimbiri. Koma iwo analola kuti maganizo oipa akhazikike komanso akule mumtima mwawo. Mwina nafenso tatumikira kwa zaka zambiri m’gulu la Yehova. Koma ngakhale tili m’gulu momwemu, maganizo oipa akhoza kuyamba n’kukula m’mitima yathu. (1 Akor. 10:12) Choncho tiyenera kudzifufuza moona mtima n’kumachotseratu maganizo achiwerewere komanso odzikuza.​—Agal. 5:26; Akol. 3:5. w18.05 25 ¶11-12

Lamlungu, September 27

Ndili ndi chisoni chachikulu ndiponso mtima ukundipweteka nthawi zonse.​—Aroma 9:2.

Paulo anakhumudwa chifukwa choti Ayuda ankakana uthenga wa Ufumu. Komabe sankawaona ngati anthu okanika. Onani zimene iye anauza Akhristu a ku Roma zokhudza mmene ankaonera Ayuda. Iye anati: “Chimene ndikufunitsitsa mumtima mwanga ndiponso pembedzero langa kwa Mulungu ndi lakuti Aisiraeli apulumutsidwe. Pakuti ndikuwachitira umboni kuti ndi odzipereka potumikira Mulungu, koma samudziwa molondola.” (Aroma 10:1, 2) Paulo anatchula zifukwa zimene zinkamuchititsa kuti apitirize kulalikira kwa Ayuda. Iye ‘ankafunitsitsa mumtima mwake’ kuti Ayuda ena adzapulumuke. (Aroma 11:13, 14) Paulo ankachonderera Mulungu m’pemphero kuti athandize Ayuda kuti azilandira uthenga wa Ufumu. Iye ananena kuti Ayuda anali “odzipereka potumikira Mulungu.” Izi zikusonyeza kuti ankaona zinthu zabwino zimene anthu ankachita. Paulo ankadziwa kuti anthu amtima wabwino, omwe ndi odzipereka pa zinthu zina, akhoza kusintha n’kukhala odzipereka potsatira Khristu. w18.05 13 ¶4; 15-16 ¶13-14

Lolemba, September 28

[Muzilankhula] mawu alionse . . . olimbikitsa monga mmene kungafunikire, kuti asangalatse owamva.​—Aef. 4:29.

Aliyense ayenera kukhala tcheru kuti azindikire mavuto amene anthu ena akukumana nawo. Paja Paulo analangiza Akhristu achiheberi kuti: “Limbitsani manja amene ali lende ndi mawondo olobodoka, ndipo pitirizani kuwongola njira zimene mapazi anu akuyendamo, kuti chiwalo chimene chavulala chisaguluke polumikizira, koma chichiritsidwe.” (Aheb. 12:12, 13) Kaya ndife achikulire kapena achinyamata, tikhoza kuuza anzathu mawu olimbikitsa. Paulo anapereka malangizo awa kwa Akhristu onse amumpingo wa Filipi: “Chotero, ngati pakati panu pali kulimbikitsana kulikonse mwa Khristu, kaya kutonthozana kulikonse kwa chikondi, kaya mzimu woganizirana, kaya chikondi chachikulu chilichonse ndi chifundo, chititsani chimwemwe changa kusefukira pokhala ndi maganizo amodzi, ndi chikondi chofanana. Mukhalenso ogwirizana mu mzimu umodzi, ndi mtima umodzi. Musachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani. Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”​—Afil. 2:1-4. w18.04 22 ¶10; 23 ¶12

Lachiwiri, September 29

Khalani mfulu, koma ufulu wanu usakhale ngati chophimbira zoipa, koma monga akapolo a Mulungu.​—1 Pet. 2:16.

Cholinga chachikulu chimene Mulungu anatimasulira ku ukapolo wa uchimo ndi imfa, pogwiritsa ntchito Yesu, n’chakuti tizimutumikira ndi moyo wathu wonse ngati akapolo ake. Choncho kuti tisakopeke ndi zinthu za m’dzikoli n’kubwerera ku ukapolo woipa uja, tiyenera kutanganidwa ndi zinthu zauzimu. (Agal. 5:16) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Nowa ndi banja lake. Iwo ankakhala m’dziko la anthu achiwawa komanso achiwerewere. Koma sanakopeke ndi zimene anthu ankakonda pa nthawiyo. Kodi iwo anakwanitsa bwanji kuchita zimenezi? Iwo ankatanganidwa kwambiri kuchita zimene Mulungu anawauza kuti azichita. Ankamanga chingalawa, kusonkhanitsa chakudya chawo ndi cha zinyama komanso kuchenjeza anthu. Baibulo limanena kuti: “Nowa anachita zonse motsatira zimene Mulungu anamulamula. Anachitadi momwemo.” (Gen. 6:22) Kodi zotsatira zake zinali zotani? Nowa ndi banja lake anapulumuka pamene dziko linkawonongedwa.​—Aheb. 11:7. w18.04 10 ¶8; 11 ¶11-12

Lachitatu, September 30

Ndikupatsani ulamuliro pa maufumu onsewa ndi ulemerero wawo wonse, chifukwa unaperekedwa kwa ine. Ndikhoza kuupereka kwa aliyense amene ndakonda kum’patsa.—Luka 4:6.

Kuwonjezera pa maboma a anthu, Satana ndi ziwanda zake amagwiritsanso ntchito zipembedzo zonyenga ndiponso mabungwe a zamalonda kuti azisocheretsa “dziko lonse lapansi.” (Chiv. 12:9) Iye amagwiritsa ntchito zipembedzo zonyenga kuti azifalitsa mabodza okhudza Yehova. Zikuoneka kuti amafunitsitsanso kuti anthu aiwale dzina la Mulungu. (Yer. 23:26, 27) Izi zimachititsa kuti anthu omwe akufuna kuchita zabwino aziganiza kuti akulambira Mulungu koma akulambira ziwanda. (1 Akor. 10:20; 2 Akor. 11:13-15) Satana amagwiritsanso ntchito mabungwe a zamalonda kuti azifalitsa mabodza. Mwachitsanzo, mabungwewo amachititsa anthu kuganiza kuti akhoza kukhala osangalala pokhapokha ngati atapeza ndalama komanso zinthu zambiri. (Miy. 18:11) Anthu amene amakhulupirira bodza limeneli, amangokhalira kufunafuna chuma m’malo motumikira Mulungu. (Mat. 6:24) Pakapita nthawi, kukonda chuma kumawasokoneza moti amasiyiratu kukonda Mulungu.​—Mat. 13:22; 1 Yoh. 2:15, 16. w18.05 23 ¶6-7

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena