Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • scl tsamba 3-5
  • Mawu Oyamba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mawu Oyamba
  • Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
scl tsamba 3-5

Mawu Oyamba

Buku la Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu likuthandizani kuti musamavutike kupeza mavesi ndi nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni kuthana ndi mavuto. Lingakuthandizeninso kupeza mavesi amene mungawagwiritse ntchito polimbikitsa ena komanso kuwathandiza kusankha zochita zimene zingalemekeze Yehova. Sankhani mutu wa nkhani imene mukufuna. Pa mutu uliwonse, pali mafunso othandiza komanso mawu achidule ofotokozera nkhani za m’Baibulo. (Onani kabokosi kakuti “Mmene Mungapezere Mitu ya Nkhani M’bukuli.”) Mupeza malemba osiyanasiyana amene angakuthandizeni kupeza malangizo, kukulimbikitsani ndiponso kukutonthozani. Mupezanso mfundo za m’Baibulo zomwe mungatsitsimule nazo anthu amene afooka, kuwathandiza kuthana ndi mavuto komanso kuwapatsa malangizo ndi kuwalimbikitsa.

Mmene Mungapezere Mitu ya Nkhani M’bukuli

Kuti mupeze nkhani imene mukufuna mukhoza kufufuza pogwiritsa ntchito kabokosi kofufuzira kapena mungafufuze potengera mutu wa nkhani yomwe mukufuna. Bukuli lagawidwa m’zigawo zokwana 7 zomwe ndi: Mavuto, Makhalidwe, Mpingo, Zochitika pa Moyo Wathu, Banja, Ubwenzi Wathu Ndi Yehova komanso Zochita Zathu. Sitikukayikira kuti mukhoza kupeza nkhani yomwe mukufuna m’zigawo zimenezi. Sankhani chigawo chimodzi n’kufufuza mutu wa nkhaniyo. Koma ngati simukudziwa chigawo chake, sankhani Zonse kuti mupeze nkhaniyo. Pamutu uliwonse muzipeza mitu ing’onoing’ono yomwe yalembedwa ndi zilembo zakuda. Mitu ina yalembedwa ngati ziganizo pomwe ina ndi mafunso. Choncho mukamawerenga mavesi osagwidwa mawu azilembo zakuda pansi pa kamutu kalikonse, muziganizira mmene mavesiwo akugwirizanirana ndi chiganizo kapena yankho la funso. Mitu ina yagawidwa m’zigawo zing’onozing’ono pofuna kukuthandizani kupeza mwamsanga nkhani imene mukufuna. Nthawi zina muzipeza mavesi owonjezera ndipo mavesiwa alembedwa ndi mawu akuti, “Onaninso.” Mavesi amenewa ali ndi mfundo zogwirizana ndi mutu wa nkhani. Muzipezanso mbali yakuti, “Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni.” M’munsi mwa mavesi omwe ali pakamutu kameneka, muli chiganizo chofotokozera mwachidule mfundo yaikulu m’mavesi amenewo. Chiganizochi chikuthandizani kuganizira mfundo yomwe mukufunikira kufufuza m’mavesi omwe mukuwerengawo.

Bukuli silinasonyeze m’ndandanda wa malemba onse okhudza mitu ya nkhani. Koma lakonzedwa kuti likuthandizeni kupeza malemba ofunika kwambiri koma ngati mukufuna kudziwa zambiri mungafufuze m’mabuku ena. (Miy 2:1-6) Kuti mufufuze mozama, gwiritsani ntchito malifalensi amudanga lapakati komanso mfundo zothandiza pophunzira mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika. Kuti mumvetse bwino tanthauzo la lemba linalake, gwiritsani ntchito Buku Lofufuzira Nkhani la Mboni za Yehova komanso buku la Chingelezi lakuti Watch Tower Publications Index. Muzifufuza m’mabuku omwe afalitsidwa chaposachedwapa kuti mutsimikizire ngati mfundo za m’Malemba zomwe mukudziwa zikugwirizana ndi kamvekedwe katsopano.

Buku la Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu likuthandizeni pamene mukufufuza nzeru, kudziwa zinthu komanso kumvetsa zinthu m’Malemba Opatulika. Mukamagwiritsa ntchito bukuli, mudzafika potsimikizira kuti “mawu a Mulungu ndi amoyo komanso amphamvu.”—Ahe 4:12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena