Kudzipereka
Kodi tiyenera kukhala ndi cholinga chabwino chiti tikamadzipereka kwa Yehova Mulungu?
Onaninso Eks 20:5
Ngati tikufuna kutumikira Mulungu, kodi Baibulo tiyenera kumaliona bwanji?
Sl 119:105; 1At 2:13; 2Ti 3:16
Onaninso Yoh 17:17; Ahe 4:12
Kodi tiyenera kuzindikira mfundo iti pa nkhani ya mmene Yehova amatithandizira kupewa tchimo?
Kodi kulapa machimo omwe tinachita kumaphatikizapo kuchita chiyani?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Lu 19:1-10—Zakeyu, mkulu wa okhometsa misonkho ankalanda anthu zinthu powanamizira milandu koma iye analapa ndi kubweza zomwe analandazo
1Ti 1:12-16 —Mtumwi Paulo anafotokoza mmene anasiyira kuchita zoipa komanso mmene Mulungu ndi Khristu anamukhululukira pomusonyeza chifundo
Kodi ndi zinthu zinanso ziti zomwe tingachite kuwonjezera pa kusiya makhalidwe oipa?
Kodi ndi mfundo zamakhalidwe abwino ziti zomwe tiyenera kumatsatira kuti tizitumikira Mulungu m’njira yovomerezeka?
1Ak 6:9-11; Akl 3:5-9; 1Pe 1:14, 15; 4:3, 4
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Ak 5:1-13—Mtumwi Paulo analamula mpingo wa ku Korinto kuti uchotse mumpingo munthu wachiwerewere
2Ti 2:16-19—Mtumwi Paulo anachenjeza Timoteyo kuti apewe nkhani za anthu ampatuko zomwe zimafalikira ngati chilonda chonyeka
N’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu sayenera kulowelera m’zochitika za maboma a anthu?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Yoh 6:10-15—Yesu atadyetsa gulu la anthu mozizwitsa, anthuwo ankafuna kumuveka ufumu koma iye anachoka n’kupita kwina
Yoh 18:33-36—Yesu anafotokoza kuti Ufumu wake suli mbali ya maboma a anthu
Kodi mzimu woyera umatithandiza bwanji pamene tikutumikira Mulungu?
Onaninso Mac 20:28; Aef 5:18
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mac 15:28, 29—Bungwe lolamulira ku Yerusalemu linatsogoleredwa ndi mzimu woyera posankha zoyenera kuchita pa nkhani yofunika kwambiri yokhudza mdulidwe
Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhani yotumikira Mulungu?
N’chifukwa chiyani Akhristu odzipereka amafunika kubatizidwa?
Mt 28:19, 20; Mac 2:40, 41; 8:12; 1Pe 3:21
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mt 3:13-17—Yesu anabwera kudzachita chifuniro cha Atate wake ndipo anasonyeza kuti wadzipereka pamene anabatizidwa
Mac 8:26-39—Nduna ya ku Itiyopiya yomwe inkalambira kale Yehova inali yokonzeka kubatizidwa itaphunzira zokhudza Yesu Khristu