Kumwa Mowa
Kodi Baibulo limanena kuti kumwa mowa n’kulakwa?
Sl 104:14, 15; Mla 9:7; 10:19; 1Ti 5:23
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Yoh 2:1-11—Yesu anachita chozizwitsa chake choyamba posandutsa madzi kukhala vinyo wabwino kwambiri ndipo zimenezi zinathandiza kuti mkwati ndi mkwatibwi asachititsidwe manyazi paphwando la ukwati wawo
Kodi kumwa kwambiri komanso kuledzera kumabweretsa mavuto otani?
Kodi atumiki a Mulungu amakuona bwanji kuledzera?
1Ak 5:11; 6:9, 10; Aef 5:18; 1Ti 3:2, 3
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 9:20-25—Nowa ataledzera, zinachititsa kuti mdzukulu wake achite tchimo lalikulu
1Sa 25:2, 3, 36—Nabala yemwe anali wouma mtima komanso wopanda nzeru anachita zinthu zochititsa manyazi kuphatikizapo kuledzera
Da 5:1-6, 22, 23, 30, 31—Mfumu Belisazara atamwa vinyo wambiri, ananyoza Yehova Mulungu ndipo zotsatirapo zake anaphedwa usiku womwewo
N’chifukwa chiyani tifunika kusamala kwambiri ndi kuchuluka kwa mowa umene timamwa ngakhale kuti sitingaledzere?
Miy 23:20; Yes 5:11; Lu 21:34; 1Ti 3:8
Onaninso 1Pe 4:3
Kodi tingathandize bwanji Akhristu anzathu omwe akulimbana ndi chizolowezi choledzera?
Aro 14:13, 21; 1Ak 13:4, 5; 1At 4:4
Onaninso “Kudziletsa”