Yesu Khristu
Kodi ndi njira yapadera iti imene Yehova amakwaniritsira chifuniro chake kudzera mwa Yesu?
Mac 4:12; 10:43; 2Ak 1:20; Afi 2:9, 10
Onaninso Miy 8:22, 23, 30, 31; Yoh 1:10; Chv 3:14
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mt 16:13-17—Mtumwi Petulo anayankha kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu
Mt 17:1-9—Yesu anasintha maonekedwe ake pamaso pa atumwi ake atatu ndipo iwo anamva Yehova akunena kuti Yesu ndi Mwana Wake
Ndi zinthu ziti zimene zimachititsa kuti Yesu akhale wosiyana ndi anthu ena onse?
Yoh 8:58; 14:9, 10; Akl 1:15-17; 1Pe 2:22
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mt 21:1-9—Yesu akulowa mu Yerusalemu atakwera bulu anakwaniritsa ulosi wakuti ndi Mesiya, Mfumu yosankhidwa ndi Yehova
Ahe 7:26-28—Mtumwi Paulo anafotokoza mmene Yesu, Mkulu wa Ansembe amasiyanirana ndi akulu a ansembe ena
Kodi zozizwitsa zimene Yesu ankachita zimatiphunzitsa chiyani zokhudza Yesu ndi Atate wake?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mt 4:23, 24—Yesu anasonyeza kuti anali wamphamvu kuposa ziwanda ndipo anatha kuchiritsa nthenda yamtundu uliwonse
Mt 14:15-21—Yesu anachulukitsa mikate 5 ndi nsomba ziwiri n’kudyetsa anthu masauzande ambirimbiri mozizwitsa
Mt 17:24-27—Pofuna kusakhumudwitsa anthu, Yesu anachita chozizwitsa n’cholinga choti Petulo apeze ndalama zolipirira msonkho wapakachisi
Mko 1:40, 41—Yesu atagwidwa ndi chifundo, anachiritsa munthu wakhate ndipo umenewu ndi umboni wakuti ndi wofunitsitsa kuchiritsa odwala
Mko 4:36-41—Yesu analetsa mphepo yamkuntho kusonyeza kuti Yehova anamupatsa mphamvu zolamulira mphepo
Yoh 11:11-15, 31-45—Yesu analira mnzake wapamtima Lazaro atamwalira; kenako Yesu anaukitsa Lazaro posonyeza kuti amadana ndi imfa komanso amakhudzidwa ndi ululu umene anthu amamva chifukwa choferedwa
Kodi mfundo yaikulu ya uthenga womwe Yesu ankaphunzitsa inali yotani?
Kodi ndi makhalidwe ena ati omwe Yesu anasonyeza ali padzikoli? Onani mmene anasonyezera kuti anali . . .
Wofikirika—Mt 13:2; Mko 10:13-16; Lu 7:36-50
Wachifundo—Mko 5:25-34; Lu 7:11-15
Wolimba mtima—Mt 4:2-11; Yoh 2:13-17; 18:1-6
Wodzichepetsa—Mt 11:29; 20:28; Yoh 13: 1-5; Afi 2:7, 8
Wachikondi—Yoh 13:1; 14:31; 15:13; 1Yo 3:16
Womvera—Lu 2:40, 51, 52; Ahe 5:8
Wanzeru—Mt 12:42; 13:54; Akl 2:3
N’chifukwa chiyani Yesu anapereka moyo wake? Nanga nsembe yake imatithandiza bwanji?
N’chifukwa chiyani tiyenera kusangalala kuti Yesu Khristu akulamulira monga Mfumu kumwamba?
Sl 72:12-14; Da 2:44; 7:13, 14; Chv 12:9, 10
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Sl 45:2-7, 16, 17—Salimoli likusonyeza kuti Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu idzagonjetsa adani ake onse ndipo idzalamulira mogwirizana ndi choonadi, modzichepetsa komanso mwachilungamo
Yes 11:1-10—Yesu akamadzalamulira monga Mfumu, dzikoli lidzakhala paradaiso ndipo kudzakhala mtendere wochuluka