Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • scl tsamba 122-123
  • Zikondwerero

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zikondwerero
  • Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
scl tsamba 122-123

Zikondwerero

Zikondwerero zimene Akhristu amachita nawo

Kodi ndi chikondwerero chiti chimene Akhristu anauzidwa kuti azichita?

Lu 22:19; 1Ak 11:23-26

Atumiki a Mulungu amasangalala kusonkhana pamodzi kuti alambire Yehova

De 31:12; Ahe 10:24, 25

  • Nkhani ya m’Baibulo yomwe ingakuthandizeni:

    • 2Mb 30:1, 6, 13, 14, 18-27​—Mfumu Hezekiya inakonza phwando lalikulu la chikondwerero cha Pasika

Zikondwerero zimene Akhristu sachita nawo

N’chifukwa chiyani n’kulakwa kuchita nawo zikondwerero zokhudzana ndi chipembedzo chonyenga?

1Ak 10:21; 2Ak 6:14-18; Aef 5:10, 11

Onaninso “Kuphatikiza Chipembedzo Choona ndi Chonyenga”

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Eks 32:1-10​—Aisiraeli anaputa mkwiyo wa Yehova pamene anasakaniza kulambira koona ndi konyenga

    • Nu 25:1-9​—Yehova analanga anthu ake chifukwa chochita zachiwerewere komanso zikondwerero zokhudzana ndi kulambira konyenga

Kodi Akhristu ayenera kukondwerera Khirisimasi?

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Lu 2:1-5​—Yesu anabadwa pa nthawi ya kalembera. Pa nthawiyi, Aroma sakanakakamiza Ayuda opanduka kupita kwina chifukwa inali nyengo yozizira ndiponso yamvula

    • Lu 2:8, 12​—Pamene Yesu ankabadwa, abusa ankagonera kunja komwe ankadyetsera ziweto zawo, choncho sizikanatheka kuchita zimenezi m’nyengo yozizira m’mwezi wa December

Kodi Akhristu ayenera kukondwerera masiku akubadwa?

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 40:20-22​—Farao yemwe sankalambira Mulungu woona anakondwerera tsiku lake lobadwa ndipo patsikuli munthu anaphedwa

    • Mt 14:6-11​—Herode Mfumu yoipa yomwe inkatsutsa otsatira a Khristu inkakondwerera tsiku lake lobadwa ndipo inalamula kuti Yohane M’batizi aphedwe

Zikondwerero zochokera m’Chilamulo cha Mose

Kodi Akhristu angagwiritse ntchito mfundo za m’Chilamulo cha Mose zomwe zikuphatikizapo zikondwerero zosiyanasiyana?

Aro 10:4; Aef 2:15

Onaninso Aga 4:4, 5, 9-11; Ahe 8:7-13; 9:1-3, 9, 10, 24

Kodi Akhristu ayenera kumvera lamulo lokhudza kusunga Sabata?

Akl 2:16, 17

Onaninso Eks 31:16, 17

Zikondwerero zam’dziko lanu

Kodi Akhristu ayenera kuchita nawo zikondwerero zokumbukira zimene dziko lawo linachita?

Yoh 15:19; 18:36; Yak 4:4

Onaninso “Maboma​—Akhristu Salowerera Zochitika za Dziko”

Kodi Akhristu ayenera kuchita nawo miyambo yokumbukira nkhondo za mayiko?

Sl 11:5; Yes 2:4

Onaninso “Maboma​—Akhristu Salowerera Zochitika za Dziko” ndi “Nkhondo”

Kodi Akhristu ayenera kuchita nawo miyambo yopereka ulemu wapadera kwa anthu otchuka?

Eks 20:5; Aro 1:25

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mac 12:21-23​—Mulungu analanga Mfumu Herode Agiripa 1 chifukwa cholandira ulemu woyenera kupita kwa Mulungu yekha

    • Mac 14:11-15​—Mtumwi Baranaba ndi Paulo anakana kulambiridwa

    • Chv 22:8, 9​—Mngelo wa Yehova anakana kulambiridwa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena