Kuphatikiza Chipembedzo Choona ndi Chonyenga
Kodi anthu onse okonda kupembedza amalambira Mulungu mmodzi?
Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu amavomereza zipembedzo zonse ngakhale kuti zimaphunzitsa zinthu zosiyanasiyana?
Mt 7:13, 14; Yoh 17:3; Aef 4:4-6
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Yos 24:15—Yoswa ananena kuti tili ndi ufulu wosankha kutumikira Yehova kapena milungu ina
1Mf 18:19-40—Yehova anagwiritsa ntchito mneneri Eliya posonyeza kuti anthu amene amalambira Mulungu woona sayenera kulambira milungu ina monga Baala
Kodi Yehova ananena kuti adzachita chiyani ndi milungu ya anthu amitundu ina? Nanga amamva bwanji anthu akamailambira?
Kodi Yehova amamva bwanji ngati anthu amene amati amamulambira akuchitanso zinthu zimene iye amadana nazo?
Yes 1:13-15; 1Ak 10:20-22; 2Ak 6:14, 15, 17
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Eks 32:1-10—Aroni atapanga fano la mwana wa ng’ombe, Yehova anamukwiyira kwambiri, ngakhale kuti Aisiraeli ananena kuti akugwiritsa ntchito fanolo pochita “chikondwerero cha Yehova”
1Mf 12:26-30—Mfumu Yerobowamu sankafuna kuti anthu azipita kukachisi wa ku Yerusalemu kukalambira Yehova. Choncho iye anapanga fano ndipo ananena kuti likuimira Yehova, koma zimenezi zinachititsa kuti anthu achimwire Yehova
Kodi Yehova anaphunzitsa bwanji Aisiraeli kufunika kosagwirizana ndi anthu omwe ankalambira milungu ina?
Kodi Yehova anachita chiyani anthu ake atayamba kutumikira milungu ina?
Owe 10:6, 7; Sl 106:35-40; Yer 44:2, 3
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Mf 11:1-9—Mfumu Solomo anakwiyitsa Yehova chifukwa akazi ake amitundu ina anamuchititsa kuti ayambe kulambira milungu yachilendo
Sl 78:40, 41, 55-62—Asafu anafotokoza kuti Aisiraeli atapandukira Yehova n’kuyamba kulambira mafano, Yehova anakwiya kwambiri ndipo zinamuchititsa kuti akane anthu ake
Kodi Yesu anachita zotani pa nkhani ya ziphunzitso zosemphana ndi Mawu a Mulungu zimene zipembedzo zinkaphunzitsa?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mt 16:6, 12—Yesu anayerekezera zomwe Afarisi ndi Alembi ankaphunzitsa ndi zofufumitsa, chifukwa chakuti ziphunzitso zabodza zimafalikira mwamsanga ndipo zimawononga mfundo za choonadi zochokera m’Mawu a Mulungu
Mt 23:5-7, 23-33—Yesu anadzudzula mwamphamvu Afarisi ndi Alembi chifukwa cha chinyengo chawo komanso ziphunzitso zabodza
Mko 7: 5-9—Yesu anaulula zomwe Alembi ndi Afarisi ankachita polemekeza kwambiri miyambo ya anthu m’malo molemekeza Mawu a Mulungu
Kodi Yesu ankafuna kuti otsatira ake apatukane n’kukhala m’zipembedzo zosiyanasiyana?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Yoh 15:4, 5—Yesu ananena fanizo la nthambi ya mpesa pofuna kuthandiza otsatira ake kuti apitirize kukhala pa mgwirizano ndi iye, komanso ndi Akhristu anzawo n’cholinga choti mgwirizano wawo usathe
Yoh 17:1, 6, 11, 20-23—Yesu ali ndi atumwi ake pa usiku wake womaliza, anapemphera kuti otsatira ake onse akhale ogwirizana
Kodi mipingo ya Chikhristu yosiyanasiyana m’nthawi ya atumwi, inkakhulupirira zinthu zofanana komanso kulambira Yehova m’njira yofanana?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mac 11:20-23, 25, 26—Mpingo wa ku Antiokeya unkachitira limodzi zinthu ndi mpingo wa ku Yerusalemu ndipo mipingoyi inali yogwirizana
Aro 15:25, 26; 2Ak 8:1-7—Mipingo ya Chikhristu yoyambirira inkasonyeza chikondi pothandizana pa nthawi ya mavuto ndipo zimenezi zinathandiza kuti mipingoyi ikhale yogwirizana
Kodi Mulungu amavomereza zipembedzo zonse zimene zimati zimakhulupirira Khristu?
Ngati anthu samvera zimene Khristu ndi atumwi anaphunzitsa, kodi kulambira kwawo kungakhale kovomerezeka?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mt 13:24-30, 36-43—Yesu anayerekezera Akhristu abodza ndi namsongole ndipo nanena kuti kudzakhala Akhristu abodza ambiri ndipo kwa nthawi inayake, adzalowerera mumpingo wa Chikhristu
1Yo 2:18, 19—Mtumwi Yohane atakalamba ananena kuti anthu ambiri okana Khristu anayamba kuonekera zaka 100 Yesu asanabadwe