Ukalamba; Achikulire
Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamakula?
Onaninso “Chitonthozo—Kulephera kuchita zambiri chifukwa cha matenda kapena ukalamba”
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mla 12:1-8—Mfumu Solomo anafotokoza mwandakatulo mavuto omwe amabwera chifukwa cha ukalamba monga kuvutika kuona, (“akazi oyang’ana pawindo azidzaona mdima”) kuvutika kumva, (“ana onse aakazi azidzaimba nyimbo ndi mawu ofooka”)
Kodi achikulire akhoza kumakhalabe osangalala ngakhale kuti akukumana ndi mavuto komanso akulephera kuchita zambiri chifukwa cha ukalamba?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Sa 12:2, 23—Mneneri Samueli ali wachikulire ankadziwa kufunika kopitiriza kupempherera anthu a Yehova
2Sa 19:31-39—Mfumu Davide anayamikira kwambiri Barizilai yemwe anali wachikulire chifukwa chomuchitira zinthu mokhulupirika. Kenako modzichepetsa, Barizilai anauza Davide kuti sakanatha kuchita zinthu zomwe sakanakwanitsa
Sl 71:9, 18—Mfumu Davide ankaopa kuti Yehova sangamugwiritsenso ntchito chifukwa choti wakalamba, choncho anamuchonderera kuti asamusiye koma amupatse mphamvu kuti adzaphunzitse m’badwo wotsatira zokhudza Iye
Lu 2:36-38—Mneneri wamkazi, Anna, yemwe anali wachikulire, anadalitsidwa chifukwa cha kudzipereka komanso kukhulupirika kwake potumikira Yehova
Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amasamalira achikulire?
Sl 92:12-14; Miy 16:31; 20:29; Yes 46:4; Tit 2:2-5
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 12:1-4—Abulahamu ali ndi zaka 75, analandira utumiki watsopano womwe unasintha moyo wake wonse
Da 10:11, 19; 12:13—Mngelo analimbikitsa mneneri Danieli ali ndi zaka za m’ma 90, n’kumuuza kuti iye ndi wofunika kwambiri kwa Yehova komanso adzadalitsidwa chifukwa cha kukhulupirika kwake
Lu 1:5-13—Ngakhale kuti Zekariya ndi Elizabeti anali okalamba, Yehova anawadalitsa pochititsa kuti abereke mwana wamwamuna dzina lake Yohane
Lu 2:25-35—Ngakhale kuti Simiyoni anali wokalamba, Yehova anamupatsa mwayi woona kubadwa kwa Mesiya; kenako Simiyoni analankhula ulosi wokhudza Mesiya
Mac 7:23, 30-36—Mose ali ndi zaka 80, Yehova anamupatsa udindo wotsogolera anthu Ake, Aisiraeli
Kodi tiyenera kuchita bwanji zinthu ndi achikulire okhulupirika?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 45:9-11; 47:12—Yosefe anaitanitsa bambo ake a Yakobo omwe anali achikulire, kuti aziwasamalira kwa moyo wawo wonse
Ru 1:14-17; 2:2, 17, 18, 23—Rute anathandiza a Naomi omwe anali achikulire akamalankhula nawo komanso akamachita nawo zinthu
Yoh 19:26, 27—Yesu atatsala pang’ono kufa pamtengo wozunzikirapo, anapempha mtumwi Yohane kuti asamalire mayi ake omwe anali achikulire