Ukwati
Kodi anayambitsa ukwati ndi ndani?
Kodi Mkhristu amene akufuna kulowa m’banja ayenera kusankha munthu wotani?
N’chifukwa chiyani Mkhristu weniweni sayenera kuvomereza kuti mwana wake wobatizidwa akwatirane ndi munthu yemwe sanadzipereke kwa Yehova n’kubatizidwa?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 24:1-4, 7—Abulahamu atakalamba anathandiza mwana wake Isaki kusankha mkazi amene ankatumikira Yehova, osati Akanani amene ankalambira milungu yonyenga
Ge 28:1-4—Isaki anauza mwana wake Yakobo kuti asankhe mkazi wotumikira Yehova, osati Akanani
Kodi Yehova amaona bwanji anthu amene asankha kukwatirana ndi munthu wosakhulupirira?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Mf 11: 1-6, 9-11—Yehova anakwiyira Mfumu Solomo chifukwa chonyalanyaza machenjezo ake akuti asakwatire akazi amitundu ina, komanso pololera kuti apotoze mtima wake kuti azitsatira milungu yawo
Ne 13:23-27—Mofanana ndi Yehova, nayenso Bwanamkubwa Nehemiya anakwiya pamene amuna a Chiisiraeli anakwatira akazi amitundu ina omwe sankatumikira Yehova, choncho anawadzudzula
N’chifukwa chiyani ndi nzeru kusankha wokwatirana naye yemwe amatumikira Yehova mokhulupirika komanso wa mbiri yabwino?
Onaninso Aef 5: 28-31, 33
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Sa 25:2, 3, 14-17—Nabala yemwe anali mwamuna wa Abigayeli, anali munthu wolemera kwambiri koma wankhanza komanso wopanda nzeru
Miy 21:9—Ngati sitinasankhe mwanzeru munthu wokwatirana naye, zingakhale zovuta kwambiri kuti tizisangalala komanso tizikhala mwamtendere
Aro 7:2—Mtumwi Paulo anapereka malangizo osonyeza kuti mkazi akakwatiwa amakhala womangidwa mwalamulo kwa mwamuna wake wopanda ungwiro pamene mwamunayo ali moyo; choncho mkazi wanzeru amasankha bwino munthu wokwatirana naye
Kukonzekera ukwati
N’chifukwa chiyani mwamuna ayenera kukhala wokonzeka kusamalira mkazi wake ndi ana asanaganize zokwatira?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Miy 24:27—Mwamuna asanakwatire mwinanso n’kudzakhala ana, ayenera kugwira ntchito molimbikira n’cholinga choti akhale wokonzeka kusamalira banja
N’chifukwa chiyani anthu omwe ali pachibwenzi ayenera kupempha malangizo anzeru kwa ena komanso kuganizira kwambiri za khalidwe la mnzawoyo m’malo moganizira za kaonekedwe kake?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ru 2:4-7, 10-12—Boazi anadziwa zokhudza Rute poona mmene ankagwirira ntchito mwakhama, mmene ankachitira zinthu ndi Naomi, pomva zinthu zabwino zimene anthu odalirika ankanena komanso kuona mmene ankakondera Yehova
Ru 2:8, 9, 20—Rute anadziwa zokhudza Boazi poona makhalidwe ake abwino monga chifundo, kuwolowa manja komanso kukonda Yehova
N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti anthu omwe ali pachibwenzi akhale ndi makhalidwe oyera mpaka pamene adzakwatirane?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Miy 5:18, 19—Anthu omwe ali pachibwenzi ali ndi malire pa nkhani yosonyezana chikondi mosiyana ndi mmene okwatirana angachitire
Nym 1:2; 2:6—M’busa wachinyamata ndi Msulami ankasonyezana chikondi choyenerera, osati kuchita khalidwe lodetsa losonkhezera chilakolako cha chiwerewere
Nym 4:12; 8:8-10—Msulami anakhalabe woyera ndipo anasonyeza kudziletsa; choncho anali ngati munda umene watsekedwa
N’chifukwa chiyani anthu ayenera kukwatirana motsatira malamulo a ukwati?
Udindo wa mwamuna wokwatira
Kodi ndi maudindo akuluakulu ati amene mwamuna wokwatira anapatsidwa m’banja?
Kodi mwamuna wokwatira ayenera kutengera chitsanzo cha ndani pa nkhani yosonyeza umutu?
N’chifukwa chiyani mwamuna wokwatira amafunika kusonyeza chikondi kwa mkazi wake, komanso kumvetsa ndi kudziwa bwino mmene akumvera?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 21:8-12—Yehova anapereka malangizo mwachindunji kwa Abulahamu kuti amvere zimene mkazi wake Sara ananena ngakhale kuti maganizo a mkazi wakeyo sanamusangalatse
Miy 31:10, 11, 16, 28—Mwamuna wanzeru yemwe ali ndi mkazi wabwino wofotokozedwa m’mavesiwa, samalamulira kapena kupezera zifukwa mkazi wake, koma amamukhulupirira ndi kumuyamikira
Aef 5:33—Mtumwi Paulo ananena mouziridwa kuti mkazi amafunika kudziwa kuti mwamuna wake amamukonda mwapadera
Udindo wa mkazi wokwatiwa
Kodi Yehova wapereka udindo wotani kwa akazi wokwatiwa?
Kodi udindo wa mkazi wokwatiwa ndi wotsika?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Miy 1:8; 1Ak 7:4—Yehova anapereka udindo kwa mkazi wokwatiwa komanso kwa azimayi amene ali ndi ana
1Ak 11:3—Mtumwi Paulo anafotokoza kuti kupatulapo Mulungu Wamphamvuyonse, tonsefe timafunikira kugonjera dongosolo limene anaika lokhudza umutu
Ahe 13:7, 17—Mumpingo, amuna ndi akazi ayenera kugonjera anthu amene anasankhidwa kuti azitsogolera
Kodi akazi a Chikhristu omwe amuna awo ndi osakhulupirira angasangalatse bwanji Yehova?
N’chifukwa chiyani mkazi wa Chikhristu ayenera kulemekeza kwambiri mwamuna wake?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 18:12; 1Pe 3:5, 6—Sara ankasonyeza kuti amalemekeza kwambiri mwamuna wake Abulahamu monga mutu wa banja ndipo ankamutchula kuti, “mbuyanga”
Kodi Baibulo limatamanda mkazi wotani?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 24:62-67—Isaki anatonthozedwa ndi mkazi wake Rabeka pambuyo pa imfa ya amayi ake
1Sa 25:14-24, 32-38—Mwamuna wa Abigayeli atachita zinthu mopanda nzeru, Abigayeli anachonderera Davide modzichepetsa kuti ateteze banja lake
Est 4:6-17; 5:1-8; 7:1-6; 8: 3-6—Pofuna kupulumutsa anthu a Mulungu, Mfumukazi Esitere analolera kuika moyo wake pangozi pokaonekera kawiri kwa mwamuna wake, yemwe anali mfumu, asanamuitane
Kuthana ndi mavuto
Kodi ndi mfundo ziti zimene zingathandize anthu okwatirana kuthana ndi mavuto awo m’banja?
Kodi ndi mfundo ziti zimene zingathandize anthu okwatirana kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ndalama?
Lu 12:15; Afi 4:5; 1Ti 6:9, 10; Ahe 13:5
Onaninso “Ndalama”