Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • scl tsamba 99-102
  • Pemphero

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pemphero
  • Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
scl tsamba 99-102

Pemphero

Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amamvetsera komanso amayankha mapemphero?

Sl 65:2; 145:18; 1Yo 5:14

Onaninso Sl 66:19; Mac 10:31; Ahe 5:7

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Mf 18:36-38​—Yehova anayankha mofulumira pemphero la mneneri Eliya pa Phiri la Karimeli pa nthawi yomwe anakumana ndi aneneri a Baala

    • Mt 7:7-11​—Yesu anatilimbikitsa kuti tizipemphera mwakhama ndipo anatitsimikizira kuti Yehova, yemwe ndi Atate wathu wachikondi amatimvetsera

Kodi Akhristu ayenera kupemphera kwa ndani yekha?

Sl 5:1, 2; 69:13; Mt 6:9; Afi 4:6

Kodi tiyenera kupemphera m’dzina la ndani?

Yoh 15:16; 16:23, 24

Kodi Yehova amamvetsera mapemphero a ndani?

Mac 10:34, 35; 1Pe 3:12; 1Yo 3:22; 5:14

Kodi Yehova samamvetsera mapemphero a ndani?

Miy 15:29; 28:9; Yes 1:15; Mik 3:4; Yak 4:3; 1Pe 3:7

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Yos 24:9, 10​—Yehova anakana kumvetsera pemphero la Balamu chifukwa anapempha zinthu zosemphana ndi chifuniro cha Mulungu

    • Yes 1:15-17​—Yehova anakana kumvetsera mapemphero a anthu ake chifukwa anayamba kuchita zachinyengo komanso anali ndi mlandu wa magazi

Kodi tiyenera kumanena zotani kumapeto kwa pemphero, nanga n’chifukwa chiyani?

1Mb 16:36; Sl 41:13; 72:19; 89:52; 1Ak 14:16

Kodi Baibulo limapereka malangizo apadera okhudza malo kapena mmene tiyenera kukhalira popemphera?

1Mf 8:54; Mko 11:25; Lu 22:39, 41; Yoh 11:41

Onaninso Yon 2:1

Ndi zinthu ziti zimene atumiki a Yehova angazitchule m’pemphero akasonkhana pamodzi kuti alambire Mulungu?

Mac 4:23, 24; 12:5

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Mb 29:10-19​—Mfumu Davide anapemphera pamaso pa Aisiraeli, pa nthawi imene anthuwo ankapereka zopereka zothandizira kumanga kachisi

    • Mac 1:12-14​—Atumwi, abale a Yesu, Mariya mayi ake a Yesu komanso azimayi ena okhulupirika anasonkhana m’chipinda cham’mwamba ku Yerusalemu kuti apemphere limodzi

N’chifukwa chiyani popemphera sitiyenera kudzikweza kapena kulankhula n’cholinga choti anthu ena atitamande?

Mt 6:5; Lu 18:10-14

N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera tisanayambe kudya?

Mt 14:19; Mac 27:35; 1Ak 10:25, 26, 30, 31

N’chifukwa chiyani sitiyenera kunyalanyaza kupemphera kwa Atate wathu wakumwamba?

Aro 12:12; Aef 6:18; 1At 5:17; 1Pe 4:7

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Da 6:6-10​—Danieli anapitiriza kupemphera kwa Yehova pamalo oonekera, ngakhale kuti anali pachiopsezo choti akhoza kuphedwa akamachita zimenezi

    • Lu 18:1-8​—Yesu ananena fanizo la woweruza wosalungama yemwe anathandiza mzimayi amene anamukakamira kuti aweruze mlandu wake mwachilungamo. Anayerekezera ndi Atate wathu wachilungamo, yemwe amamvetsera atumiki ake omwe amachita khama popemphera

Ngati tikufuna kuti Mulungu atikhululukire, kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani tikamapemphera?

2Mb 7:13, 14

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 2Mf 22:11-13, 18-20​—Yehova anachitira chifundo komanso kukomera mtima Mfumu Yosiya chifukwa choti anadzichepetsa n’kuyamba kuchita zinthu zabwino

    • 2Mb 33:10-13​—Mfumu Manase anadzichepetsa n’kuchonderera Yehova kuti amukhululukire ndipo anamukhululukira n’kumupatsanso udindo wake monga mfumu

Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova atikhululukire?

Mt 6:14, 15; Mko 11:25; Lu 17:3, 4

N’chifukwa chiyani tikamapemphera kwa Yehova tifunika kupemphereranso kuti zofuna zake zichitike?

Mt 6:10; Lu 22:41, 42

N’chifukwa chiyani mapemphero athu ayenera kusonyeza kuti timadalira Atate wathu wakumwamba?

Mko 11:24; Ahe 6:10; Yak 1:5-7

Kodi tiyenera kutchula zinthu ziti m’pemphero?

Kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu

Lu 11:2

Kubwera kwa Ufumu wa Mulungu kuti udzalamulire dziko lonse lapansi

Mt 6:10

Zofuna za Yehova zichitike

Mt 6:10; 26:42

Zinthu zimene tikufunikira pa moyo wathu

Lu 11:3

Tizipempha kuti atikhululukire machimo athu

Da 9:19; Lu 11:4

Tizipempha kuti atiteteze kuti tisachite zoipa tikamayesedwa

Mt 6:13

Tiziyamikira

Aef 5:20; Afi 4:6; 1At 5:17, 18

Tizipempha kuti tidziwe zofuna zake, tikhale omvetsa zinthu komanso anzeru

Miy 2:3-6; Afi 1:9; Yak 1:5

Onaninso Sl 119:34

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Mf 3:11, 12​—Mfumu Solomo anapempha nzeru kwa Yehova ndipo anamupatsa nzeru zochuluka

Tizipempha mzimu woyera

Lu 11:13; Mac 8:14, 15

Tizipempherera Akhristu anzathu kuphatikizapo amene akuzunzidwa

Mac 12:5; Aro 15:30, 31; Yak 5:16

Onaninso Akl 4:12; 2Ti 1:3

Tizilankhula mawu otamanda Yehova

Sl 86:12; Yes 25:1; Da 2:23

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Lu 10:21​—Yesu anatamanda Atate wake pagulu chifukwa choti anaulula mfundo za choonadi kwa anthu omwe anali odzichepetsa ngati ana aang’ono

    • Chv 4:9-11​—Angelo anapereka ulemu ndi ulemerero womwe Yehova amafunikira

Tizipempha kuti olamulira adzikoli azitilola kulambira Yehova mwamtendere ndiponso kulalikira kwa anthu

Mt 5:44; 1Ti 2:1, 2

Onaninso Yer 29:7

Kodi n’zoyenera kupemphera pa nthawi ya ubatizo wathu?

Lu 3:21

Kodi n’zoyenera kuti tizipempherera anthu amene akudwala mwauzimu?

Yak 5:14, 15

N’chifukwa chiyani nthawi zambiri amuna akamapemphera savala chophimba kumutu, nanga n’chifukwa chiyani nthawi zina akazi akamapemphera amavala chophimba kumutu?

1Ak 11:2-16

Kodi Mulungu amaona kuti chofunika kwambiri n’kutalika kwa pemphero, kapena mmene timakhudzidwira popemphera?

Mlr 3:41; Mt 6:7

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Mf 18:25-29, 36-39​—Poyankha zimene mneneri Eliya anawauza, aneneri a Baala anapemphera mobwerezabwereza kwa mulungu wawo koma sanawayankhe

    • Mac 19:32-41​—Anthu olambira mafano mumzinda wa Efeso anafuula mokweza potamanda mulungu wamkazi dzina lake Atemi kwa maola awiri. Koma zotsatirapo zake, woyang’anira mzindawo analetsa anthuwo kuti asachite zachipolowe

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena