Oyang’anira
Kodi akulu mumpingo afunika kumachita zotani kuti akhale oyenerera komanso kuti apitirize udindo wawo?
Kodi akulu mumpingo ayenera kuchitanso zinthu ziti posonyeza chitsanzo chabwino?
Mt 28:19, 20; Aga 5:22, 23; 6:1; Aef 5:28; 6:4; 1Ti 4:15; 2Ti 1:14; Tit 2:12, 14; Ahe 10:24, 25; 1Pe 3:13
Kodi atumiki othandiza mumpingo ayenera kukwaniritsa zinthu ziti?
Kodi mzimu wa Yehova umathandiza bwanji abale posankha oyang’anira?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mac 13:2-5; 14:23—Paulo ndi Baranaba ankasankha akulu m’mipingo yosiyanasiyana; n’chimodzimodzinso oyang’anira masiku ano. Iwo amapempha mzimu woyera kuti uwathandize kumvetsa bwino Malemba kuti athe kusankha bwino anthu omwe ali oyenerera kukhala pa udindo
Tit 1:1, 5—Tito anapatsidwa ntchito yoyendera mipingo yosiyanasiyana kuti asankhe akulu
Kodi mpingo ndi wa ndani? Nanga unagulidwa pa mtengo wotani?
N’chifukwa chiyani Baibulo limatchula akulu kuti atumiki, kapena kuti akapolo otumikira ena?
N’chifukwa chiyani oyang’anira afunika kukhala odzichepetsa?
Afi 1:1; 2:5-8; 1At 2:6-8; 1Pe 5:1-3, 5, 6
Nkhani ya m’Baibulo yomwe ingakuthandizeni:
Mac 20:17, 31-38—Mtumwi Paulo anakumbutsa akulu a ku Efeso zimene anawachitira kwa zaka zambiri ndipo iwo anasonyeza kuyamikira chikondi chake
Kodi oyang’anira ayenera kuona bwanji malangizo ochokera kwa “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru”?
Kodi ndi njira yabwino kwambiri iti yomwe akulu angaphunzitsire ena?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ne 5:14-16—Chifukwa choopa Yehova, Bwanamkubwa Nehemiya anapewa kugwiritsa ntchito udindo wake molakwika pakati anthu a Mulungu ngakhalenso kutenga zinthu zimene zinayenera kuperekedwa kwa iye
Yoh 13:12-15—Zimene Yesu anachita kwa otsatira ake zinawaphunzitsa kukhala odzichepetsa
Kodi abusa a Chikhristu angasonyeze bwanji kuti amadera nkhawa wina aliyense mumpingo?
Kodi akulu angathandize bwanji Mkhristu yemwe akudwala mwauzimu?
Kodi akulu ali ndi udindo wotani pa nkhani yophunzitsa?
1Ti 1:3-7; 2Ti 2:16-18; Tit 1:9
Onaninso 2Ak 11:2-4
N’chifukwa chiyani akulu ayenera kuchita khama poonetsetsa kuti mpingo ndi woyera?
1Ak 5:1-5, 12, 13; Yak 3:17; Yuda 3, 4; Chv 2:18, 20
Onaninso 1Ti 5:1, 2, 22
Kodi ayenera kuchita khama pophunzitsa ndani?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mt 10:5-20—Yesu anaphunzitsa otsatira ake 12 kenako anawatumiza kuti akagwire ntchito yolalikira
Lu 10:1-11—Yesu anapereka kaye malangizo kwa ophunzira ake 70 asanawatumize kukagwira ntchito yolalikira
N’chiyani chingathandize akulu kukwaniritsa ntchito zawo zosiyanasiyana?
Onaninso Miy 3:5, 6
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Mf 3:9-12—Solomo atakhala mfumu, anapempha kwa Yehova kuti amupatse nzeru komanso mtima womvetsa zinthu kuti amuthandize kuweruza anthu a Yehova
2Mb 19:4-7—Mfumu Yehosafati anasankha oweruza m’mizinda ya Yuda ndipo anawakumbutsa kuti Yehova adzakhala nawo pa nthawi imene akugwira ntchito yawo
Kodi Akhristu ayenera kuwaona bwanji akulu okhulupirika?
1At 5:12, 13; 1Ti 5:17; Ahe 13:7, 17
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mac 20:37—Akhristu a ku Efeso sankazengereza kusonyeza chikondi chawo kwa mtumwi Paulo
Mac 28:14-16—Pamene mtumwi Paulo ankayenda maulendo opita ku Roma, abale amumzindawo anayenda ulendo wa makilomita 65 kuti adzakumane naye ku Msika wa Apiyo ndipo anamulimbikitsa kwambiri