Nzeru
Kodi timafunika kuchita chiyani kuti tikhale ndi nzeru zenizeni?
Kodi tingapeze kuti nzeru zenizeni?
Kodi ndi zoyenera kupemphera kwa Mulungu kuti atipatse nzeru?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
2Mb 1:8-12—Mfumu Solomo ali wamng’ono anapemphera kuti akhale ndi nzeru n’cholinga choti azilamulira bwino Isiraeli ndipo Yehova anamupatsa nzeru
Miy 2:1-5—Baibulo limayerekezera nzeru, kumvetsa zinthu komanso kuzindikira ndi chuma chobisika chimene timafunika kuchifufuza ndipo Yehova amathandiza anthu omwe amachifunafuna ndi mtima wawo wonse
Kodi Yehova amapereka bwanji nzeru?
Yes 11:2; 1Ak 1:24, 30; 2:13; Aef 1:17; Akl 2:2, 3
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Miy 8:1-3, 22-31—Nzeru imafotokozedwa ngati munthu ndipo zimenezi zimatikumbutsa za Mwana wa Mulungu yemwe anali woyambirira kulengedwa zinthu zina zonse zisanalengedwe
Mt 13:51-54—Anthu ambiri omwe ankamvetsera zimene Yesu ankaphunzitsa, anadabwa kwambiri kuti zikutheka bwanji kuti munthu yemwe anakula akumuona akhale ndi nzeru zochuluka choncho
Kodi timadziwa bwanji kuti tili ndi nzeru zochokera kwa Mulungu?
Sl 111:10; Mla 8:1; Yak 3:13-17
Onaninso Sl 107:43; Miy 1:1-5
Kodi nzeru zimatithandiza komanso kutiteteza bwanji?
Onaninso Miy 7:2-5; Mla 7:12
Kodi nzeru zochokera kwa Mulungu ndi zothandiza bwanji?
Onaninso Yob 28:18
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Yob 28:12, 15-19—Ngakhale kuti Yobu anavutika kwambiri, iye anayamikira nzeru zochokera kwa Mulungu
Sl 19:7-9—Mfumu Davide ananena kuti chilamulo cha Yehova ndiponso zikumbutso zake zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu