Kuthetsa Kusamvana
N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kupsa mtima kapena kubwezera munthu wina akatilakwira?
Miy 20:22; 24:29; Aro 12:17, 18; Yak 1:19, 20; 1Pe 3:8, 9
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Sa 25:9-13, 23-35—Nabala atanyoza Davide ndi anyamata ake n’kukana kuwapatsa thandizo, mopupuluma Davide anaganiza zopha Nabala ndi amuna onse am’banja lake. Kenako malangizo anzeru amene Abigayeli anapereka anathandiza kuti asabwezere
Miy 24:17-20—Mouziridwa, Mfumu Solomo inachenjeza anthu a Mulungu kuti Yehova samafuna kuti tizisangalala adani athu akamavutika; m’malomwake tizingozisiya m’manja mwa Yehova yemwe ndi woweruza wachilungamo
Kodi Mkhristu ayenera kusiya kulankhulana kapena kusiya kucheza ndi munthu amene wamulakwira?
Le 19:17, 18; 1Ak 13:4, 5; Aef 4:26
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Mt 5:23, 24—Yesu anafotokoza kuti ngati tasemphana maganizo ndi m’bale wathu, tifunika kuchita zonse zimene tingathe pokhazikitsa mtendere