Kusiyana kwa Anthu
Kodi Mulungu amaona kuti anthu ena ndi apamwamba kuposa anzawo chifukwa chosiyana kochokera, mtundu, kapena kuchuluka kwa ndalama zomwe ali nazo?
Mac 17:26, 27; Aro 3:23-27; Aga 2:6; 3:28
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Yoh 8:31-40—Ayuda ena ankanyadira kuti anali mbadwa za Abulahamu koma Yesu anawadzudzula chifukwa chakuti sankachita ntchito za Abulahamu
Kodi pali chifukwa chilichonse choonera anthu ena kuti ndi otsika chifukwa cha mtundu wawo kapena dziko limene akuchokera?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Yon 4:1-11—Yehova anachita zinthu moleza mtima pophunzitsa mneneri Yona kufunika kosonyeza chifundo anthu a ku Nineve omwe anali adziko lina
Mac 10:1-8, 24-29, 34, 35—Mtumwi Petulo anaphunzira mfundo yakuti sakuyenera kuona anthu omwe sanali Ayuda kukhala odetsedwa, choncho anathandiza Koneliyo limodzi ndi banja lake kukhala Akhristu oyambirira omwe anali osadulidwa
Kodi Akhristu olemera ayenera kumadziona kuti ndi apamwamba kuposa anthu ena a ndalama zochepa kapenanso kufuna kuti anthu aziwachitira zinthu mwapadera?
Onaninso De 8:12-14; Yer 9:23, 24
Kodi oyang’anira ayenera kumadziona kuti ndi apamwamba kuposa ena kapenanso kuchita zinthu mwankhanza?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
De 17:18-20—Yehova anachenjeza mafumu a Chiisiraeli kuti asamaganize kuti ndi apamwamba kuposa anthu ena onse, m’malomwake aziwaona ngati abale awo
Mko 10:35-45—Yesu anadzudzula aphunzira ake chifukwa chodera nkhawa kwambiri zopatsidwa udindo komanso kulamulira ena
Kodi Mulungu amavomereza munthu wotani?
Kodi Akhristu ayenera kutenga nawo mbali m’magulu omenyera ufulu?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Yoh 6:14, 15—Ngakhale kuti anthu ambiri ankafuna kuti Yesu akhale mfumu yawo kuti awathetsere mavuto awo, iye anakana n’kuchokapo