April
Loweruka, April 1
Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha.—Yoh. 3:16.
Yesu anatisonyeza chikondi chachikulu pololera kupereka moyo wake chifukwa cha ife. (Yoh. 15:13) Sitingathe kubwezera Yehova ndi Yesu pa chikondi chimene anatisonyeza. Komabe tingasonyeze kuyamikira ndi zimene timachita pa moyo wathu tsiku lililonse. (Akol. 3:15) Odzozedwa amaona kuti dipo ndi lamtengo wapatali chifukwa limachititsa kuti chiyembekezo chawo chikhale chotheka. (Mat. 20:28) Chifukwa chakuti amakhulupirira nsembe ya Khristu, Yehova amawaona monga olungama komanso ana ake. (Aroma 5:1; 8:15-17, 23) A nkhosa zina nawonso amayamikira dipo. Chifukwa chokhulupirira magazi a Khristu, Mulungu amawaona kuti ndi oyera komanso ali ndi chiyembekezo ‘chodzatuluka ‘m’chisautso chachikulu.’ (Chiv. 7:13-15) Magulu onsewa amasonyeza kuti amayamikira dipo popezeka pa Chikumbutso chaka chilichonse. w22.01 23 ¶14-15
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 10 kutacha) Mateyu 21:18, 19; 21:12, 13; Yohane 12:20-50
Lamlungu, April 2
Khristu anatigula.—Agal. 3:13.
Yesu ankada nkhawa kwambiri ndi chifukwa chimene anamuphera. Iye ankaimbidwa mlandu wakuti anali wonyoza Mulungu, munthu amene sankalemekeza Mulungu komanso dzina lake. (Mat. 26:64-66) Zimenezi zinkamupweteka kwambiri Yesu moti ankalakalaka Atate wake atamuchotsera chitonzo chimenechi. (Mat. 26:38, 39, 42) Yesu ankayenera kupachikidwa pamtengo kuti amasule Ayuda ku temberero linalake. (Agal. 3:10) Iwo anali atalonjeza kuti adzamvera Chilamulo cha Mulungu koma analephera kuchitsatira. Choncho iwo anali otembereredwa kuwonjezera pa mfundo yoti ankayenera kufa popeza anali ana a Adamu yemwe anali wochimwa. (Aroma 5:12) Chilamulo cha Mulungu chinkanena kuti munthu amene wapalamula mlandu womwe chilango chake ndi imfa, aziphedwa kenako thupi lake lizipachikidwa pamtengo. (Deut. 21:22, 23; 27:26) Choncho pamene Yesu anapachikidwa pamtengo, anathandiza kuti Ayuda amasulidwe ku temberero lawo ndiponso kuti athe kupindula ndi nsembe ya dipo ngakhale kuti anali atamukana. w21.04 16 ¶5-6
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 11 kutacha) Mateyu 21:33-41; 22:15-22; 23:1-12; 24:1-3
Lolemba, April 3
Ndikupereka moyo wanga.—Yoh. 10:17.
Taganizirani zimene zinachitika patsiku lomaliza Yesu asanafe. Asilikali a Chiroma anamumenya mopanda chifundo. (Mat. 26:52-54; Yoh. 18:3; 19:1) Iwo anamukwapula ndi chikwapu chimene chinasiya mabala aakulu pathupi lake. Kenako anamunyamulitsa mtengo wolemera kumsana kwake komwe kunali mabala okhaokha. Yesu anayamba kukwakwaza mtengowo kupita nawo kumalo komwe ankakamuphera koma atangoyenda pang’ono, asilikaliwo analamula munthu wina kuti amunyamulire mtengowo. (Mat. 27:32) Atafika kumalowo, asilikaliwo anakhomerera manja ndi mapazi ake kumtengowo ndi misomali. Ataimika mtengowo, mabala a misomali aja anawonjezeka chifukwa cha kulemera kwa thupi lake. Anzake a Yesu anamva chisoni kwambiri ndipo mayi ake ankangolira koma atsogoleri a Chiyuda ankamunyogodola. (Luka 23:32-38; Yoh. 19:25) Yesu anavutika ndi ululu umenewu kwa maola angapo. Mtima ndi mapapo ake zinkalephera kugwira bwino ntchito ndipo ankapuma movutikira. Atangotsala pang’ono kufa komanso ataona kuti wayesetsa kuchita zonse mokhulupirika, anapereka pemphero lake lomaliza kwa Yehova. Kenako anaweramitsa mutu wake n’kupereka moyo wake. (Maliko 15:37; Luka 23:46; Yoh. 10:18; 19:30) Imeneyitu inali imfa yopweteka kwambiri komanso yochititsa manyazi. w21.04 16 ¶4
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 12 kutacha) Mateyu 26:1-5, 14-16; Luka 22:1-6
TSIKU LA CHIKUMBUTSO
Dzuwa Litalowa
Lachiwiri, April 4
Muzichita zimenezi pondikumbukira.—Luka 22:19.
Yesu anafotokozera atumwi ake 11 okhulupirika zokhudza mapangano awiri, omwe ndi pangano latsopano komanso pangano la Ufumu. (Luka 22:20, 28-30) Mapanganowa anatsegula mwayi woti atumwi ndi anthu ena owerengeka adzakhale mafumu komanso ansembe kumwamba. (Chiv. 5:10; 14:1) Odzozedwa amene adakali padzikoli, omwe ali m’mapangano awiriwa, ndi amene ayenera kudya mkate ndi kumwa vinyo pa Chikumbutso. Yehova wawapatsa chiyembekezo chabwino kwambiri, chomwe ndi kudzakhala ndi moyo umene sungafe kumwamba limodzi ndi anzawo a m’gulu la 144,000 komanso kukatumikira ndi Yesu Khristu, yemwe anapatsidwa ulemerero. Koposa zonse, iwo adzapatsidwa mwayi wokakhala ndi Yehova Mulungu. (1 Akor. 15:51-53; 1 Yoh. 3:2) Odzozedwa amazindikira kuti ayenera kukhala okhulupirika mpaka imfa yawo.—2 Tim. 4:7, 8. w22.01 21 ¶4-5
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 13 kutacha) Mateyu 26:17-19; Luka 22:7-13 (Zochitika pa Nisani 14 dzuwa litalowa) Mateyu 26:20-56
Lachitatu, April 5
Iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.—Luka 23:43.
Yesu anapachikidwa limodzi ndi achifwamba ena awiri. Mmodzi wa awiriwa anauza Yesu kuti: “Mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.” (Luka 23:42) Yesu analankhula mawu opatsa chiyembekezo kwa wachifwambayo chifukwa ankadziwa kuti Atate wake ndi wachifundo. (Sal. 103:8; Aheb. 1:3) Yehova ndi wokonzeka kutikhululukira komanso kutisonyeza chifundo ngati tikudzimvera chisoni chifukwa cha zinthu zoipa zimene tinachita komanso ngati timakhulupirira kuti iye angatikhululukire machimo athu kudzera m’magazi a Mwana wake Yesu Khristu. (1 Yoh. 1:7) Anthu ena zimawavuta kukhulupirira kuti Yehova angawakhululukire. Ngati inunso mumamva choncho nthawi zina, taganizirani izi: Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, anasonyeza chifundo kwa wachifwamba yemwe anali atangoyamba kumene kumukhulupirira. Choncho Yehova amachitira chifundo atumiki ake okhulupirika.—Sal. 51:1; 1 Yoh. 2:1, 2. w21.04 9 ¶5-6
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 14 kutacha) Mateyu 27:1, 2, 27-37
Lachinayi, April 6
Yesu anati: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!”—Yoh. 19:30.
Pokhalabe wokhulupirika mpaka imfa yake, Yesu anakwaniritsa zinthu zingapo. Choyamba, iye anasonyeza kuti Satana ndi wabodza. Yesu anasonyeza kuti munthu wangwiro akhoza kukhalabe wokhulupirika ngakhale Satana atamuyesa chotani. Chachiwiri, Yesu anapereka moyo wake monga dipo. Chifukwa chakuti iye anapereka moyo wake, zinakhala zotheka kuti anthu omwe si angwiro akhale pa ubwenzi ndi Mulungu komanso kukhala ndi chiyembekezo chodzapeza moyo wosatha. Chachitatu, Yesu anasonyeza kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndipo zimenezi zinathandiza kuti dzina la Atate wake lilemekezedwe. Tiyeni tiziona tsiku lililonse ngati mwayi wathu womaliza wosonyeza kuti ndife okhulupirika. Ndiye ngati titatsala pang’ono kufa, tingathe kunena kuti, “Yehova, ndayesetsa kuchita zomwe ndingathe kuti ndikhale wokhulupirika kwa inu, kuti ndisonyeze kuti Satana ndi wabodza komanso kuyeretsa dzina lanu ndi kusonyeza kuti ndinu woyenera kulamulira.” w21.04 12 ¶13-14
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 15 kutacha) Mateyu 27:62-66 (Zochitika pa Nisani 16 dzuwa litalowa) Mateyu 28:2-4
Lachisanu, April 7
Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwera naye, muzimumvera.—Mat. 17:5.
Pambuyo poti wanamiziridwa komanso kuweruzidwa pamlandu womwe sanapalamule, Yesu akunyozedwa, kuzunzidwa kwambiri ndipo kenako akukhomereredwa pamtengo wozunzikirapo. Amukhomerera ndi misomali imene yaboola manja ndi mapazi ake. Kuti alankhule, ngakhale kupuma kumene akumva ululu kwambiri. Komabe ayenera kulankhula, chifukwa pali zinthu zofunika kwambiri zoti anene. Pali mfundo zofunika zambiri zimene tingaphunzire pa mawu omaliza a Yesu. Tikuphunzirapo kufunika koti tizikhululukira ena komanso kumakhulupirira kuti Yehova adzatikhululukira. Tilinso ndi abale ndi alongo mumpingo omwe ndi okonzeka kutithandiza. Koma pamene tikufunikira thandizo, tiyenera kupempha ena kuti atithandize. Tikudziwa kuti Yehova adzatithandiza kupirira mayesero alionse amene tingakumane nawo. Ndipo tiziona tsiku lililonse ngati mwayi wathu womaliza wosonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova, n’kumakhulupirira kuti iye adzatiukitsa ngati tingamwalire. w21.04 8 ¶1; 13 ¶17
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 16 kutacha) Mateyu 28:1, 5-15
Loweruka, April 8
Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.—Yoh. 17:3.
Tikamatsatira mapazi a Yesu tidzapeza moyo wosatha. Wachinyamata wina wolemera atafunsa Yesu zimene angachite kuti adzapeze moyo wosatha, iye anamuuza kuti: “Ubwere udzakhale wotsatira wanga.” (Mat. 19:16-21) Kwa Ayuda ena omwe sankakhulupirira kuti iye anali Khristu, Yesu anawauza kuti: “Nkhosa zanga . . . zimanditsatira. Ndidzazipatsa moyo wosatha.” (Yoh. 10:24-29) Timasonyeza kuti timakhulupirira Yesu tikamatsatira zimene anaphunzitsa komanso kutengera chitsanzo chake. Tikamachita zimenezi tidzapitiriza kuyenda panjira yopita ku moyo wosatha. (Mat. 7:14) Kuti tizitsatira mapazi a Yesu mosamala kwambiri, choyamba tiyenera kumudziwa bwino. “Kudziwa” Yesu kulibe polekezera. Tiyenera kupitirizabe kuphunzira zambiri zokhudza iye kuti tidziwe makhalidwe ake, kaganizidwe kake komanso mfundo zake. Kaya takhala m’choonadi kwa nthawi yaitali bwanji, tiyenera kupitiriza kuchita khama kuti “tidziwe bwino” Yehova limodzi ndi Mwana wake. w21.04 4 ¶9-10
Lamlungu, April 9
Kale ndinali wonyoza Mulungu [ndiponso] wozunza anthu ake.—1 Tim. 1:13.
N’kutheka kuti nthawi zina mtumwi Paulo ankavutika maganizo ndi zinthu zimene anachita m’mbuyo. Iye anafika podzitchula kuti anali wochimwa “kwambiri,” ndipo izi n’zosadabwitsa. (1 Tim. 1:15) Poyamba asanaphunzire choonadi, ankazunza mwankhanza Akhristu m’mizinda yosiyanasiyana, kuwatsekera m’ndende komanso kuvomereza nawo kuti ena aphedwe. (Mac. 26:10, 11) Ndipo taganizirani mmene akanamvera kukumana ndi Mkhristu wachinyamata amene iye anavomereza nawo kuti makolo ake aphedwe. Paulo ankadziimba mlandu kwambiri chifukwa cha zimene analakwitsa, koma ankadziwa kuti sangasinthe zinthu zimene zinachitika kale. Iye anavomereza kuti Khristu anamufera, ndipo motsimikiza analemba kuti: “Mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndili monga ndililimu.” (1 Akor. 15:3, 10) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Muzivomereza kuti Khristu anafera inuyo ndipo zimenezi zinapereka mwayi woti mukhalenso pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova. (Mac. 3:19) Dziwani kuti kwa Mulungu chofunika kwambiri ndi zimene mungachite panopa komanso m’tsogolo, osati zimene munalakwitsa m’mbuyo.—Yes. 1:18. w21.04 23 ¶11
Lolemba, April 10
Muziyesa mawu ouziridwawo kuti muone ngati ali ochokeradi kwa Mulungu, chifukwa aneneri onyenga ambiri alowa m’dziko.—1 Yoh. 4:1.
Ngakhale kuti Ayuda ambiri m’nthawi ya Yesu sankayembekezera kuti Mesiya adzafunika kuti afe, taonani zimene Malemba ananeneratu zokhudza iye, kuti: “Anakhuthula moyo wake mu imfa ndipo anaonedwa monga mmodzi wa ochimwa. Iye ananyamula tchimo la anthu ambiri ndipo analowererapo kuti athandize olakwa.” (Yes. 53:12) Choncho kuphedwa kwa Yesu monga munthu wochimwa, sichinali chifukwa chomveka choti Ayudawo amukanire. Masiku ano, chomwe chingatithandize kuti tisakhumudwe n’kusiya kutumikira Yehova ndi kufufuza kuti tidziwe zoona zenizeni. Pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu anachenjeza anthu amene ankamumvetsera kuti anthu ena adzawanamizira “zoipa zilizonse.” (Mat. 5:11) Mabodza amenewa amachokera kwa Satana. Iye amagwiritsa ntchito otsutsa kuti azifalitsa mabodza okhudza anthu amene amakonda choonadi. (Chiv. 12:9, 10) Sitiyenera kumvetsera zinthu zabodza zimene adani athu amanena. Ndipo tisamalole kuti zinthu zabodzazi zitichititse mantha kapenanso kufooketsa chikhulupiriro chathu. w21.05 11 ¶14; 12 ¶16
Lachiwiri, April 11
Musachite mantha: Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zochuluka.—Mat. 10:31.
Muzithandiza wophunzira Baibulo wanu kuti azidalira Yehova. Yesu anatsimikizira ophunzira ake kuti Yehova adzawathandiza chifukwa amawakonda. (Mat. 10:19, 20, 29, 30) Muzikumbutsa wophunzira wanu kuti nayenso Yehova azimuthandiza. Mungamuthandize kuti azidalira Yehova mukamatchula zolinga zake pamene mukupemphera naye. Franciszek, yemwe amakhala ku Poland ananena kuti: “Mphunzitsi wanga ankatchula zolinga zanga akamapemphera nane. Nditaona mmene Yehova ankayankhira mapemphero a mphunzitsi wangayo, mwamsanga inenso ndinayamba kumapemphera. Ndinaona kuti Yehova anandithandiza pamene ndinkapempha nthawi kuntchito imene ndinali nditangoyamba kumene, kuti ndikachite nawo msonkhano wachigawo komanso ndizipezeka pamisonkhano ya mpingo.” Yehova amakonda kwambiri anthu amene timaphunzira nawo Baibulo. Amakondanso kwambiri Akhristu amene amachita khama kuphunzitsa ena kuti akhale naye pa ubwenzi ndipo amawayamikira chifukwa cha zimenezi. (Yes. 52:7) Ngati panopa simukuchititsa phunziro la Baibulo, mungathandizebe ophunzira Baibulo kupita patsogolo mpaka kufika pobatizidwa popita ndi ofalitsa ena kumaphunziro awo. w21.06 7 ¶17-18
Lachitatu, April 12
Amakondwera ndi chilamulo cha Yehova, ndipo amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulo chake usana ndi usiku.—Sal. 1:2.
Tingasonyeze kuti timayamikira mwayi wokhala ndi Mawu a Mulungu tikamawawerenga nthawi zonse. Sitiyenera kumaphunzira Mawu a Mulungu mwamwayi pamene taona kuti tili ndi nthawi. Tikamayesetsa kuti tiziphunzira Baibulo nthawi zonse, tingalimbitse chikhulupiriro chathu. Mosiyana ndi “anthu anzeru ndi ozindikira” a m’dzikoli, ifeyo tili ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa cha zimene timaphunzira m’Baibulo. (Mat. 11:25, 26) Zimene zili m’buku lopatulikali zimatithandiza kudziwa chifukwa chake zinthu zikuipiraipirabe padzikoli komanso zimene Yehova achite posachedwapa. Choncho tiyeni tipitirizebe kulimbitsa chikhulupiriro chathu ndiponso kuthandiza anthu ambiri kuti azikhulupirira Mlengi wathu. (1 Tim. 2:3, 4) Komanso tiyeni tipitirize kuyembekezera nthawi yomwe anthu onse padzikoli adzanene mawu opezeka pa Chivumbulutso 4:11, akuti: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu . . . , kulandira ulemerero . . . , chifukwa munalenga zinthu zonse.” w21.08 19 ¶18-20
Lachinayi, April 13
Pokonda abale, khalani ndi chikondi chenicheni pakati panu.—Aroma 12:10.
Monga abusa, akulu ali ndi udindo wopereka malangizo ngati pakufunika kutero. Iwo ayenera kuyesetsa kupereka malangizo othandiza, olimbikitsa komanso ‘osangalatsa mtima.’ (Miy. 27:9) Akulu amakonda abale ndi alongo awo. Nthawi zina iwo amasonyeza chikondi chimenechi popereka malangizo kwa munthu yemwe wayamba kuyenda panjira yolakwika. (Agal. 6:1) Komabe asanalankhule ndi munthuyo, mkulu angaganizire zinthu zina zokhudza chikondi zomwe mtumwi Paulo anafotokoza. Iye anati: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. . . . Chimakwirira zinthu zonse, chimakhulupirira zinthu zonse, chimayembekezera zinthu zonse, chimapirira zinthu zonse.” (1 Akor. 13:4, 7) Kuganizira kwambiri mavesi a m’Baibulo amenewa, kungathandize mkulu kuti afufuze zolinga zake popereka malangizo komanso kukhala ndi maganizo oyenera akamapereka malangizowo. Munthu yemwe akupatsidwa malangizoyo akazindikira kuti mkuluyo amamukonda, zingakhale zosavuta kuti awalandire. w22.02 14 ¶3; 15 ¶5
Lachisanu, April 14
Iwo anapanduka ndi kukhumudwitsa mzimu wake woyera.—Yes. 63:10.
Yehova analenga ana ake omwe ndi angelo komanso anthu ali angwiro. Koma mmodzi wa angelowo yemwe ndi Satana (kutanthauza “Wotsutsa”) anasankha kusamvera ndipo anachititsanso kuti Adamu ndi Hava asamvere Yehova. Patapita nthawi, angelo ndi anthu enanso anasankha kugwirizana nawo. (Yuda 6) Zimenezitu zinamupweteka kwambiri Yehova. Komabe iye wakhala akupirira ndipo apitirizabe kupirira mpaka nthawi imene adzawononge onse osamvera. Kenako Yehova ndi anthu onse omwe ndi okhulupirika kwa iye adzasangalala chifukwa sadzafunika kupiriranso zinthu zoipa za m’dzikoli. Satana ananena kuti mtumiki wokhulupirika wa Yehova, Yobu, komanso atumiki okhulupirika a Yehova masiku ano amatumikira Mulungu chifukwa cha dyera. (Yobu 1:8-11; 2:3-5) Satana amanenabe zimenezi mpaka pano. (Chiv. 12:10) Tingasonyeze kuti zimene Satana amanena ndi zabodza tikamapirira mayesero n’kukhalabe okhulupirika kwa Yehova chifukwa choti timamukonda. w21.07 9 ¶7-8
Loweruka, April 15
Chotsani zochita zanu zoipa pamaso panga. Lekani kuchita zoipa.—Yes. 1:16.
Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo chabwino kwambiri chosonyeza kuti tiyenera kutsimikiza mtima kusintha zinthu pa moyo wathu. Iye analemba kuti tiyenera kupachika umunthu wathu wakale “pamtengo.” (Aroma 6:6) M’mawu ena, tiyenera kutsanzira Khristu. Tifunika kuthetseratu maganizo ndi makhalidwe amene Yehova amadana nawo. Tikamatsatira malangizo amenewa ndi pamene tingakhale ndi chikumbumtima chabwino komanso chiyembekezo chodzapeza moyo wosatha. (Yoh. 17:3; 1 Pet. 3:21) Yehova sangasinthe mfundo zake n’cholinga chofuna kungotisangalatsa. M’malomwake, ifeyo tiyenera kusintha kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi mfundo zake. (Yes. 1:16-18; 55:9) Ngakhale pamene mwabatizidwa mumafunika kupitiriza kulimbana ndi zilakolako zoipa. Tizipempha Yehova kuti atithandize ndipo tizidalira mzimu wake osati mphamvu zathu. (Agal. 5:22; Afil. 4:6) Tiyenera kukhala otsimikiza mtima kuti tivule umunthu wakale ndiponso kuti tisauvalenso. w22.03 6 ¶15-17
Lamlungu, April 16
[Yehova] adzakuchirikiza.—Sal. 55:22.
Yehova amalonjeza kuti adzatipatsa chakudya, zovala ndi pogona ngati timaika Ufumu wake pamalo oyamba komanso ngati timachita zinthu mogwirizana ndi mfundo zake zolungama. (Mat. 6:33) Chifukwa cha zimenezi, timapewa kuganiza kuti chuma komanso zinthu za m’dzikoli zingatithandize kukhala otetezeka kapenanso osangalala. Timadziwa kuti chimene chingatithandize kupeza mtendere weniweni wamumtima, ndi kuchita zimene Yehova amafuna basi. (Afil. 4:6, 7) Ngakhale kuti tingakwanitse kugula zinthu zambiri, tiyenera kuganizira ngati tingakhale ndi nthawi komanso mphamvu zogwiritsa ntchito zinthuzo komanso kuzisamalira. Kodi timakonda kwambiri zinthu zimene tili nazo? Tizikumbukira kuti Mulungu watipatsa ntchito yoti tizigwira m’banja lake. Zimenezi zikutanthauza kuti sitiyenera kulola kusokonezedwa ndi chilichonse. Sitingafune ngakhale pang’ono kukhala ngati munthu wina, yemwe anakana mwayi wotumikira Yehova komanso kukhala m’gulu la ana ake chifukwa cha zinthu zochepa zimene anapeza m’dzikoli.—Maliko 10:17-22. w21.08 6 ¶17
Lolemba, April 17
Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene wakufunsani.—1 Pet. 3:15.
Mukamaphunzira Malemba mudzayamba kuona makhalidwe omwe Mulungu ali nawo, omwenso amaonekera bwino m’zinthu zimene analenga. Kuphunzira makhalidwe a Yehova kumatithandiza kutsimikizira kuti iye alipodi. (Eks. 34:6, 7; Sal. 145:8, 9) Mukamamudziwa bwino Yehova, m’pamenenso mumamukhulupirira kwambiri, kumukonda kwambiri komanso ubwenzi wanu ndi iye umalimba. Muziuza ena zimene mumakhulupirira zokhudza Mulungu. Nanga bwanji ngati munthu amene mwamulalikira atakufunsani kuti mumufotokozere umboni woti Mulungu alipo koma simukudziwa mmene mungayankhire? Muzifufuza yankho lake m’mabuku athu ndipo kenako muzikambirana ndi munthuyo. Mukhoza kupemphanso Mkhristu amene amadziwa zambiri kuti akuthandizeni. Kaya munthuyo avomereza zimene Baibulo limanena kapena ayi, inuyo mukhoza kupindula ndi zimene mwafufuzazo ndipo chikhulupiriro chanu chidzalimba. w21.08 18 ¶14-15
Lachiwiri, April 18
Sindinakubisireni chilichonse.—Mac. 20:20.
Sikuti timafunika kusiya zinthu zonse zabwino kuti tizisangalatsa Yehova. (Mlal. 5:19, 20) Komabe ngati titalephera kuchita zambiri potumikira Yehova, mwina pongofuna kusadzimana zinthu zina, tikhoza kukhala tikulakwitsa ngati munthu wamufanizo la Yesu. Iye anachita khama kuti azikhala moyo wawofuwofu koma sankaganizira za Mulungu. (Luka 12:16-21) Tikakumana ndi mavuto, tizipempha Yehova kuti atithandize ndipo tiziyesetsa kuganizira zimene tingachite kuti tithane ndi mavuto athuwo. (Miy. 3:21) Yehova amatidalitsa m’njira zambiri. Tingasonyeze kuti timayamikira kwambiri zimene amatichitira, pochita zonse zimene tingathe pomutamanda. (Aheb. 13:15) Zimenezi zikuphatikizapo kuwonjezera utumiki wathu zomwe zimachititsanso kuti Yehova atidalitse kwambiri. Tsiku lililonse, tiyeni tiziyesetsa kupeza njira zotithandiza kuti ‘tilawe ndi kuona kuti Yehova ndi wabwino.’ (Sal. 34:8) Tikamachita zimenezi, tingafanane ndi Yesu, yemwe ananena kuti: “Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha amene anandituma ndi kutsiriza ntchito yake.”—Yoh. 4:34. w21.08 30-31 ¶16-19
Lachitatu, April 19
Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko, ndipo mtima wodzikuza umachititsa munthu kupunthwa.—Miy. 16:18.
Satana amafuna kuti tiyambe kukhala ndi mtima wonyada. Iye amadziwa kuti tikakhala ndi mtima umenewu tingafanane ndi iyeyo ndipo tikhoza kutaya mwayi wodzapeza moyo wosatha. Choncho mtumwi Paulo anachenjeza kuti munthu ayenera kusamala kuti “angakhale wotukumuka chifukwa cha kunyada, n’kulandira chiweruzo chofanana ndi chimene Mdyerekezi analandira.” (1 Tim. 3:6, 7) Zimenezi zingachitikire tonsefe, kaya tangoyamba kumene choonadi kapena takhala tikutumikira Yehova kwa zaka zambiri. Anthu amtima wonyada amakhala odzikonda. Satana amayesetsa kutipangitsa kukhala odzikonda pochititsa kuti tizingoganizira za ife tokha osati za Yehova makamaka tikakumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, kodi anthu ena akunenerani zinthu zabodza? Kapenanso ena akuchitirani zopanda chilungamo? Zikatero, Satana amasangalala ngati mukuimba mlandu Yehova kapena abale ndi alongo anu. Ndipo iye amafuna kuti muziganiza kuti njira yabwino yothetsera vuto lanulo ndi kuchita zinthu mongotsatira maganizo anu, osati kutsatira malangizo amene amapezeka m’Mawu a Mulungu.—Mlal. 7:16, 20. w21.06 15 ¶4-5
Lachinayi, April 20
“Limbani mtima anthu nonse a m’dzikoli ndipo gwirani ntchito,” watero Yehova. “Pakuti ine ndili ndi inu,” watero Yehova wa makamu.—Hag. 2:4.
Yehova anapatsa mneneri Hagai ntchito yofunika kwambiri yoti agwire. Hagai ayenera kuti anali m’gulu la anthu omwe anabwerera ku Yerusalemu mu 537 B.C.E., kuchokera ku ukapolo ku Babulo. Atangofika, mwamsanga atumiki okhulupirikawa anamanga maziko a nyumba ya Yehova, kapena kuti kachisi. (Ezara 3:8, 10) Koma pasanapite nthawi yaitali, iwo anakumana ndi mavuto omwe anawafooketsa ndipo anasiya kugwira ntchitoyi chifukwa chotsutsidwa. (Ezara 4:4; Hag. 1:1, 2) Choncho mu 520 B.C.E., Yehova anatumiza Hagai kukathandiza anthuwo kuti akhalenso ndi khama pa ntchito yomanga kachisi. (Ezara 6:14, 15) Cholinga cha uthenga wa Hagai chinali kulimbikitsa Ayuda kuti azikhulupirira kwambiri Yehova. Mawu akuti “Yehova wa makamu” ayenera kuti anawalimbikitsa kwambiri. Yehova ali ndi gulu lalikulu lankhondo la angelo, choncho Ayudawo ankafunika kumudalira kuti zinthu ziwayendere bwino. w21.09 15 ¶4-5
Lachisanu, April 21
Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.—Yoh. 13:35.
Masiku ano a Mboni za Yehova amakondana komanso amakhala ogwirizana padziko lonse. Ndife osiyana ndi zipembedzo zina zonse chifukwa timachita zinthu ngati a m’banja limodzi ngakhale kuti timachokera m’mayiko komanso m’zikhalidwe zosiyanasiyana. Umboni wakuti timakondana kwambiri timauona pamisonkhano yathu yampingo, yadera komanso yachigawo. Zimenezi zimatithandiza kutsimikizira kwambiri kuti tikulambira Yehova m’njira imene iyeyo amaivomereza. (Yoh. 13:34) Malemba amatilimbikitsa kuti ‘tikhale okondana kwambiri.’ (1 Pet. 4:8) Njira imodzi imene tingasonyezere kuti timakondana ndi kukhululukirana komanso kulolerana. Timayesetsanso kukhala ochereza komanso owolowa manja kwa onse mumpingo, ngakhalenso amene atilakwira. (Akol. 3:12-14) Chikondi chimenechi ndi khalidwe lofunika kwambiri limene limadziwikitsa Akhristu oona. w21.10 22 ¶13-14
Loweruka, April 22
Womukonda [mwana wake] ndi amene amamuyang’anira kuti amulangize.—Miy. 13:24.
Kodi kuchotsa munthu wosalapa mumpingo kungamuthandize kuti asinthe? Inde. Abale ndi alongo ambiri omwe ankachita machimo aakulu ananena kuti kuchotsedwa mumpingo n’kumene kunawathandiza kuzindikira kulakwa kwawo, kulapa komanso kusintha khalidwe lawo n’kubwerera kwa Yehova. (Aheb. 12:5, 6) Taganizirani chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti m’busa wazindikira kuti nkhosa yake ina ikudwala. Pofuna kuthandiza kuti nkhosayo ichire, iye akudziwa kuti ayenera kuichotsa kaye pakati pa zinzake. Komabe nkhosa zimakonda kukhala pamodzi ndipo zikhoza kusokonezeka ngati munthu atazilekanitsa. Kodi pamenepa tinganene kuti m’busayo akuchita nkhanza popatula nkhosa yodwalayo? Ayi si choncho. Iye akudziwa kuti ngati atalola nkhosayo kumayendabe ndi zinzake, ikhoza kupatsira nkhosa zinazo matenda akewo. Choncho kupatula nkhosa yodwalayo kungateteze gulu lonselo. w21.10 10 ¶9-10
Lamlungu, April 23
Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.—Mat. 5:16.
Timayamikira kwambiri kukhala m’banja la padziko lonse lomwe anthu ake amakondana. Timafunitsitsa kuthandiza anthu ambiri mmene tingathere kuti nawonso ayambe kulambira Mulungu wathu. Poganizira mfundo imeneyi, tiyenera kukhala osamala kuti tisamachite chilichonse chomwe chingachititse kuti anthu aziganiza zoipa zokhudza anthu a Yehova kapena Atate wathu wakumwamba. Nthawi zonse tiziyesetsa kuchita zinthu zimene zingathandize anthu kuti azichita chidwi ndi uthenga wabwino. Nthawi zina anthu ena akhoza kumatinyoza kapena kutizunza chifukwa timamvera Atate wathu wakumwamba. Ndiye kodi tiyenera kuchita chiyani ngati timaopa kuuza ena zimene timakhulupirira? Tizidalira Yehova komanso Mwana wake kuti atithandiza. Yesu anauza ophunzira ake kuti sankayenera kuda nkhawa za mmene akalankhulire kapena zimene akanene. Chifukwa chiyani? Iye anafotokoza kuti, “Mudzapatsidwa nthawi yomweyo zoti mulankhule.” Anapitirizanso kuti, “Pakuti wolankhula simudzakhala inu panokha, koma mzimu wa Atate wanu udzalankhula kudzera mwa inu.”—Mat. 10:19, 20. w21.09 24 ¶17-18
Lolemba, April 24
Ndidzauza Yehova kuti: “Inu ndinu pothawirapo panga ndi malo anga achitetezo.”—Sal. 91:2.
Mose anatchula za malo othawirako. (Sal. 90:1) Ndipotu chakumapeto kwa moyo wake, Mose anatchulanso mfundo ina yokhazika mtima pansi. Iye analemba kuti: “Mulungu wakale lomwe ndiwo malo ako obisalamo, ndipo iwe uli m’manja [ake] amene adzakhalapo mpaka kalekale.” (Deut. 33:27) Kodi mawu akuti ‘uli m’manja ake amene adzakhalapo mpaka kalekale,’ akutiuza chiyani za Yehova? Yehova akakhala malo athu othawirako, timamva kuti ndife otetezeka. Komabe nthawi zina tikhoza kufooka n’kumalephera kusiya kumva choncho. Ndiye kodi Yehova angatichitire zotani pa nthawi ngati imeneyo? (Sal. 136:23) Pang’onopang’ono, iye adzatinyamula m’manja ake n’kutithandiza kuti tikhalenso olimba. (Sal. 28:9; 94:18) Kudziwa kuti tingadalire Mulungu kuti azitithandiza, kumatikumbutsa kuti anthufe tinadalitsidwa m’njira ziwiri. Choyamba, tili ndi malo achitetezo othawirako posatengera kumene timakhala. Ndipo chachiwiri, Atate wathu wakumwamba amatikonda kwambiri. w21.11 6 ¶15-16
Lachiwiri, April 25
Mayesero osiyanasiyana . . . akukuchititsani chisoni.—1 Pet. 1:6.
Yesu ankadziwa kuti ophunzira ake adzachitiridwa zinthu zopanda chilungamo ndipo zimenezi zidzayesa chikhulupiriro chawo. Pofuna kuwathandiza kupirira, iye anafotokoza fanizo lina lomwe limapezeka m’buku la Luka. Anafotokoza nkhani ya mayi wamasiye yemwe sanasiye kupempha woweruza wina wosaopa Mulungu kuti amuweruzire nkhani yake mwachilungamo. Iye sankakayikira kuti khama lake lichititsa kuti athandizidwe. Pamapeto pake woweruzayo anamuthandizadi. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Yehova si wosalungama. Choncho Yesu ananena kuti: ‘Ndithu, kodi Mulungu sadzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa osankhidwa ake, amene amafuulira kwa iye usana ndi usiku?’ (Luka 18:1-8) Kenako anawonjezera kuti: “Mwana wa munthu akadzafika, kodi adzapezadi chikhulupiriro padziko lapansi?” Tikachitiridwa zopanda chilungamo, timafunika kusonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba ngati cha mayi wamasiyeyu pokhala oleza mtima komanso opirira. Tikakhala ndi chikhulupiriro ngati chimenechi, sitingakayikire kuti mulimonse mmene zingakhalire Yehova adzatithandiza. Tizikhulupiriranso kuti pemphero ndi lothandiza kwambiri. w21.11 23 ¶12; 24 ¶14
Lachitatu, April 26
Kodi wachinyamata angakhale bwanji woyera pa moyo wake? Mwa kudziyang’anira ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi mawu anu.—Sal. 119:9.
Achinyamata, kodi nthawi zina mumaona kuti mfundo za Yehova ndi zopanikiza kwambiri? Izi ndi zimene Satana amafuna kuti muziganiza. Iye amafuna kuti muziganizira kwambiri zochita za anthu amene akuyenda pamsewu wotakasuka komanso zimene amaoneka ngati akusangalala nazo. Angagwiritse ntchito zomwe anzanu a kusukulu amachita kapena zimene mumaona pa intaneti pokuchititsani kuona ngati mukumanidwa zinthu zabwino. Satana amafuna kuti muziona kuti mfundo za Yehova zikukulepheretsani kusangalala mokwanira. Koma kumbukirani kuti Satana safuna kuti anthu amene akuyenda pamsewu wake adziwe kuti akumana ndi zotani kutsogolo. (Mat. 7:13, 14) Pomwe Yehova watidziwitsa kale zimene watisungira ngati tipitirizabe kuyenda pamsewu wopita kumoyo.—Sal. 37:29; Yes. 35:5, 6; 65:21-23. w21.12 23 ¶6-7
Lachinayi, April 27
Aliyense wa inu [azikhululukira] m’bale wake ndi mtima wonse.—Mat. 18:35.
Timadziwa kuti timayenera kukhululukira ena ndipo zimenezi ndi zofunika kwambiri. Komabe nthawi zina zingamativute kuti tichite zimenezi. N’kutheka kuti nayenso mtumwi Petulo ankamva choncho. (Mat. 18:21, 22) Ndiye kodi chingatithandize n’chiyani? Choyamba, muziganizira kwambiri zimene Yehova wakukhululukirani. (Mat. 18:32, 33) Iye amatikhululukira ndi mtima wonse ngakhale kuti sitinali anthu oyenera kukhululukidwa. (Sal. 103:8-10) Ndiye ifenso, “tiyenera kukondana.” Choncho nkhani yokhululukira ena si nkhani yochita kusankha, ndi zomwe timayenera kuchitira abale ndi alongo athu. (1 Yoh. 4:11) Chachiwiri, tiziganizira zimene zimachitika tikakhululukira ena. Tikhoza kuthandiza munthu amene watilakwirayo, kulimbikitsa mgwirizano mumpingo, kuteteza ubwenzi wathu ndi Yehova komanso zingatithandize kuti tizimva bwino mumtima. (2 Akor. 2:7; Akol. 3:14) Ndipo chomaliza, tizipemphera kwa Mulungu yemwe amafuna tizikhululukira ena. Musamalole Satana kusokoneza mtendere umene muli nawo ndi Akhristu anzanu. (Aef. 4:26, 27) Nthawi zonse timafunika kuthandizidwa ndi Yehova kuti tisakodwe mumsampha wa Satana. w21.06 22 ¶11; 23 ¶14
Lachisanu, April 28
Iwe ukhaladi mfumu ya Isiraeli.—1 Sam. 23:17.
Davide ankathawa chifukwa moyo wake unali pangozi. Sauli, yemwe anali mfumu yamphamvu ya Isiraeli, anali atatsimikiza mtima kuti amuphe. Pa nthawi imene ankafuna chakudya, Davide anaima mumzinda wa Nobu ndipo anapempha mitanda 5 ya mkate. (1 Sam. 21:1, 3) Pambuyo pake, iye ndi amuna amene anali nawo, anakabisala kuphanga. (1 Sam. 22:1) Kodi chinachitika n’chiyani kuti zinthu zikhale chonchi pa moyo wa Davide? Sauli ankachitira nsanje Davide chifukwa choti anatchuka komanso anali atapambana pa nkhondo zambiri. Sauli ankadziwanso kuti kusamvera kwake kunachititsa kuti Yehova amukane kuti asakhalenso mfumu ya Isiraeli ndipo anali atasankha Davide kuti akhale mfumu. (1 Sam. 23:16, 17) Monga mfumu ya Isiraeli, Sauli anali ndi gulu lalikulu la asilikali ndiponso anthu ambiri omwe anali kumbali yake. Choncho Davide anathawa kuti apulumutse moyo wake. Kodi Sauli ankaganiza kuti akanatha kulepheretsa cholinga cha Mulungu choti Davide akhale mfumu? (Yes. 55:11) Baibulo silinena koma chomwe tikudziwa n’chakuti Sauli ankaika moyo wake pangozi. Tikutero chifukwa nthawi zonse anthu amene amalimbana ndi Mulungu sapambana. w22.01 2 ¶1-2
Loweruka, April 29
Nikodemo, . . . anabwera kwa Yesu usiku.—Yoh. 3:1, 2.
Yesu ankachita khama pa ntchito yolalikira. Iye anasonyeza kuti ankakonda anthu powaphunzitsa pa mpata uliwonse umene wapezeka. (Luka 19:47, 48) N’chiyani chinkamuchititsa zimenezi? Ankawachitira chifundo. Nthawi zambiri anthu ankafuna kumvetsera mawu ake ndipo iye limodzi ndi ophunzira ake ‘sankatha n’komwe kudya chakudya.’ (Maliko 3:20) Pa nthawi ina Yesu anaphunzitsa munthu wina usiku, nthawi yomwe inali yabwino kwa munthuyo. Anthu ambiri omwe poyamba anamvetsera uthenga wake, sanakhale ophunzira ake. Koma onse omwe anamumvetsera, Yesu anawachitira umboni mokwanira. Masiku ano timafunika kuthandiza aliyense kuti amve uthenga wabwino. (Mac. 10:42) Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kusintha mmene timagwirira ntchito yolalikira. M’malo molalikira pa nthawi yomwe ndi yabwino kwa ife, tizikhala okonzeka kusintha n’cholinga choti tizilalikira pa nthawi imene tingakumane ndi anthu. Tikamachita zimenezi, tikhoza kukhala otsimikiza kuti Yehova akusangalala nafe. w22.01 17 ¶13-14
Lamlungu, April 30
Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.—Mlal. 8:9.
Masiku ano anthu ambiri zimawavuta kukhulupirira amene ali ndi udindo. Iwo amaona kuti maboma komanso malamulo amateteza anthu olemera komanso audindo, koma sachitira chilungamo anthu osauka. Kuwonjezera pamenepo, atsogoleri ena achipembedzo amachita zinthu zoipa. Zimenezi zachititsa kuti anthu ena asamakhulupirire Mulungu. Choncho tikamaphunzira Baibulo ndi munthu, timafunika kumuthandiza kuti ayambe kukhulupirira Yehova komanso anthu amene iye wawasankha kuti azitsogolera gulu lake. Komabe si ophunzira Baibulo okha amene amafunika kuphunzira kuti azikhulupirira Yehova ndi gulu lake. Ngakhale ife amene takhala tikutumikira Yehova kwa zaka zambiri, timafunika tisamakayikire kuti nthawi zonse Yehova amachita zinthu m’njira yoyenera. Nthawi zina pangachitike zinthu zina zomwe zingachititse kuti tiyambe kukayikira Yehova. w22.02 2 ¶1-2