Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 14 tsamba 70-tsamba 73
  • Anasankha Yehova Kukhala Mulungu Wake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anasankha Yehova Kukhala Mulungu Wake
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Zomwe Tikuphunzirapo
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • ‘Anaonedwa Ngati Wolungama Chifukwa cha Ntchito Zake’
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Rahabi Ankakhulupirira Yehova
    Phunzitsani Ana Anu
  • Rahabi Anamvetsera Uthenga
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Rahabi—Anayesedwa Wolungama ndi Ntchito za Chikhulupiriro
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 14 tsamba 70-tsamba 73

14 RAHABI

Anasankha Yehova Kukhala Mulungu Wake

Losindikizidwa
Losindikizidwa

MZINDA wa Yeriko unali m’dera lomwe linkalandira kuwala kokwanira kwa dzuwa. Baibulo limatchulanso mzindawu kuti “mzinda wa mitengo ya kanjedza.” (Deut. 34:3) Mumzindawu munkakhala hule lina dzina lake Rahabi. Kuchokera m’nyumba yake yomwe inali m’mbali mwa mpanda wa mzindawo, ankatha kuona chilichonse cha kunja. Koma mkatimo, anthu anali ndi nkhope zachisoni. Iwo ankadziwa kuti Yehova akuthandiza anthu ake Aisiraeli pomwe iwowo ankayembekezera kuwonongedwa. Ndipo zinali zomveka kuti awawononge.

Aisiraeli anakunga matenti awo pafupi ndi mzindawu. Zaka 40 m’mbuyomo, Yehova anapulumutsa anthu akewa pomiza gulu la nkhondo la Farao m’Nyanja Yofiira. Osati kale kwambiri, Yehova anathandiza anthu ake kupambana pa nkhondo yolimbana ndi mizinda yamphamvu ya Sihoni ndi Ogi. Tsopano ankayembekezera kulanda Yeriko. Yehova ankafuna kulanga anthu amumzindawu chifukwa cha zoipa zomwe ankachita.

Rahabi ankadziwa kuti anthu a mtundu wake ankachita zoipa. Iyenso ankakhala moyo wochititsa manyazi wa uhule. N’zosakayikitsa kuti ankafuna kukhala moyo wabwino. Zomwe anamva zokhudza Yehova zinamuthandiza kukhala ndi chiyembekezo m’malo mochita mantha. Anaphunzira kuti Yehova amateteza anthu ake komanso kuwalemekeza mosiyana kwambiri ndi milungu imene Akanani ankalambira. Rahabi anasankha kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, Mulungu woyera, wachilungamo komanso amene amateteza anthu ake.

Tsiku lina usiku, anthu awiri achilendo anafika kunyumba kwake kudzafuna malo ogona. Mwamsanga Rahabi anazindikira kuti anthuwo anali Aisiraeli. Nayonso mfumu ya Yeriko inamva za anthuwo ndipo inatumiza asilikali kwa Rahabi kukamuuza kuti atulutse amunawo. Rahabi anafunika kusankha zoti achite. Kodi anasankha kuteteza anthu a mtundu wake kapena kukhala kumbali ya Yehova?

Molimba mtima, Rahabi anasankha kuti Yehova akhale Mulungu wake. Iye anabisa amuna aja padenga la nyumba yake n’kuuza asilikali kuti amunawo apita. Asilikali aja atangonyamuka, anauza amunawo chifukwa chake anaganiza zowabisa. Anawauza kuti: “Ndikudziwa kuti Yehova akupatsani dzikoli.” Iye anayamba kukhulupirira Mulungu wa Aisiraeli ndipo anaulula kuti, amuna a ku Yeriko mitima yawo siinali m’malo chifukwa choopa Aisiraeli. Rahabi anapemphanso amunawo kuti adzamuteteze Aisiraeli akamadzawononga mzindawo.

Munthu yemwe anali hule anakwanitsa bwanji kusiya anthu a mtundu wake komanso zachiwerewere?

Rahabi anateteza moyo wa amunawo ndipo nawo anaona kuti Rahabi ali kumbali ya Yehova. Iwo anavomereza kumuchitira zomwe anawapempha. Iye ndi am’banja lake anali ndi mwayi wopulumuka. Amunawo anamuuza kuti asaulule zoti anali kunyumba kwake. Anamuuzanso kuti adzamange chingwe chofiira pawindo la nyumba yake n’kukhalabe m’nyumbamo kuti adzapulumuke Aisiraeli akamadzawononga mzindawo.

Rahabi akumanga chingwe chofiira pawindo la nyumba yake.

Amunawo anatuluka mu Yeriko pogwiritsa ntchito chingwe chomwe Rahabi anamanga pawindo lake. Rahabi anatsatira zonse zomwe amuna aja anamuuza, n’kumangirira chingwe chofiira chija pawindo. Molimba mtima, sanaulule za nkhaniyi. Iye akanatha kuphedwa ngati asilikali akanatulukira zomwe anachita. Anamveranso zomwe amuna aja anamuuza kuti iye ndi a m’banja lake adzakhalebe m’nyumbamo. N’zosakayikitsa kuti atamva zoti Yehova anagawanitsa madzi amutsinje wa Yorodano, Rahabi sanakayikire kuti anasankha bwino. N’kutheka kuti pomwe Aisiraeli anazungulira mzindawo kwa masiku 7, mumzindawo munali chisokonezo. Pa tsiku la 7, ansembe ataliza malipenga komanso asilikali atafuula, Rahabi ndi anthu am’banja lake anali pamodzi ndipo anatetezeka makoma a mzindawo atagwa.

Nkhondoyo itatha, amuna aja anatulutsa Rahabi ndi am’banja lake. Nyumba yake, yomwe inali mbali ya khoma la mpanda sinawonongedwe. Mogwirizana ndi malangizo amene Yoswa anapereka, Rahabi ndi anthu am’banja lake sanaphedwe. Patapita nthawi, Rahabi anakhala mbali ya mtundu wa Isiraeli. Iye anakwatiwa ndi munthu wa ku Isiraeli n’kubereka ana. Patadutsa zaka zambiri, mumzere wa mbadwa zake munabadwa Yesu Khristu yemwe anali wolimba mtima kuposa munthu aliyense. (Mat. 1:​5, 16) Yehova anadalitsa Rahabi chifukwa cha chikhulupiriro komanso kulimba mtima kwake.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • Yoswa 2:​1-24; 5:1; 6:​14-25

  • Aheberi 11:​30, 31

  • Yakobo 2:​24, 25

Funso lokambirana:

Kodi Rahabi anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. Kodi Rahabi ankakhala moyo wotani ku Yeriko? (w13 11/1 12 ¶4–13 ¶1)

  2. 2. Kodi timadziwa bwanji kuti amuna aja sanapite kunyumba kwa Rahabi kukachita zachiwerewere? (it “Hule” ¶16-wcgr)

  3. 3. N’chifukwa chiyani padenga la nyumba ya Rahabi panali mapesi ambiri a fulakesi, nanga fulakesiyo anali wantchito yanji? (it “Fulakesi” ¶2-4-wcgr) A

    Thanks for your interest in my photos/Moment Open via Getty Images

    Chithunzi A: Munda wa fulakesi

  4. 4. N’chifukwa chiyani Rahabi sanalakwitse kupusitsa asilikali a mfumu? (w04 12/1 9 ¶1) B

    Rahabi akupereka malangizo kwa amuna awiri ochokera kwa mfumu.

    Chithunzi B

Zomwe Tikuphunzirapo

  • N’chifukwa chiyani Rahabi ankafunika kulimba mtima kuti asiye kuchita zachiwerewere n’kuyamba kutumikira Yehova limodzi ndi Aisiraeli? Kodi ophunzira Baibulo angaphunzire chiyani kwa Rahabi?

  • Ngakhale kuti Baibulo limaletsa kunama, kodi Akhristu angaphunzire chiyani kwa Rahabi ngati adani a anthu a Mulungu atatikakamiza kuti tiulule zinthu zachinsinsi zokhudza abale athu? (Miy. 11:13; Mlal. 3:7; Aef. 4:25) C

Mlongo amumanga ndipo sakulankhulapo pomwe woyang’anira ndende akumufunsa mafunso. Woyang’anira ndendeyo akuloza mapepala omwe ali patebulo ndipo chapafupi paima msilikali wolondera.

Chithunzi C

Chithunzi C

  • Mungatsanzire kulimba mtima kwa Rahabi m’njira zinanso ziti?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Rahabi akadzaukitsidwa?

Phunzirani Zambiri

Kodi nkhani ya Rahabi ingatiphunzitse chiyani ngati tikufuna kudzapulumuka pa tsiku la Yehova?

“Kodi Mapeto Ayenera Kudzakupezani Muli Kuti?” (w09 5/15 6-8)

Gwiritsani ntchito zithunzi zofotokoza nkhani za m’Baibulo kuti muthandize ana anu kuganizira zomwe zinachitika munkhaniyi.

“Rahabi Anatsatira Malangizo” (ijwis nkhani 11)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena