GAWO 1
Kuyambira Nthawi ya Inoki Kufika Nthawi ya Oweruza
Losindikizidwa
Nkhani zimene zili m’gawoli zinachitika mkati mwa zaka pafupifupi 2,200. Tiyamba kukambirana zokhudza Inoki yemwe analipo pa nthawi imene Adamu anali ndi moyo, mpaka kudzafika nthawi ya mneneri Samueli, yemwe anadzoza mfumu yoyamba ya Isiraeli. Tikambirana zitsanzo za anthu amene anasonyeza kulimba mtima ngati Nowa, Abulahamu, Sara, Mose, Rahabi, Debora ndi Gidiyoni. Ena anayenda maulendo ataliatali ndipo anakumana ndi zinthu zoopsa pomwe ena anamenya “nkhondo za Yehova.” Anthu onsewa anasonyeza kulimba mtima pochita utumiki umene anapatsidwa ndi Mulungu yemwe ankamukonda kwambiri.