GAWO 2
Kuyambira Nthawi ya Mafumu Kufika Nthawi Yomanganso Yerusalemu
Gawoli likufotokoza zomwe zinachitika m’zaka pafupifupi 600. Tiyamba ndi kukambirana zokhudza Yonatani, mwana wa Mfumu Sauli kenako tikambirana za Davide yemwe anali mfumu yoyamba yokhulupirika ya Isiraeli. Tikambirananso za anthu osiyanasiyana mpaka nthawi imene anthu a Mulungu anabwerera kuchoka ku ukapolo ku Babulo n’kuyambanso kumanga Yerusalemu. Tilimbikitsidwa ndi zitsanzo za Abigayeli, Natani, Eliya, Danieli, Esitere, Nehemiya ndi ena ambiri. Anthuwa anakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mwachitsanzo, ena ankalamulira anthu a Yehova opanduka, ena anafunika kukhala okhulupirika pamene mafumu awo anali osakhulupirika komanso ena ankafunika kuchenjeza anthu a Mulungu kuti asamalambire mafano ndiponso kuchita zoipa.