Mafunso Amene Anthu Akufunsa Ponena za Zakumwa Zoledzeretsa
“ANTHU anzeru sakumwa vinyo mpang’ono pomwe.” Analengeza chotero mtsogoleri wa chipembedzo wa ku Nigeria. Osati kale kwambiri, ganizo lotero likanatsutsidwa kukhala losalekereredwa ndi losonyeza kusalingalira kokwanira. Komabe, lerolino, lingaliro la kutsutsa kumwa zoledzeretsa likukula m’mbali zina za dziko lapansi.
Mwachitsanzo, Kufufuza kwakuwona malingaliro a anthu kwaposachedwapa mu Reader’s Digest (U. S. ) kunavumbulutsa kuti “anthu a ku Amerika ayamba kumwa mocheperako.” Magazini ya Time mofananamo inasimba kuti “Amerika akuchepetsa [kumwa kwa zakumwa zoledzeretsa], ndipo akuchita motero paliwiro lofulumira kusiyana ndi panthawi ina iriyonse chiyambire pamene Chiletso chinayamba kugwira ntchito mu 1920.” France akusimba za kuchepera mu kumwa vinyo.
Chifukwa cha chikhoterero chimenechi kulinga ku kudziletsa? Ena adzutsa mfuu pa zinthu zowopsya zomwe zimawoneka pamisewu chifukwa cha oyendetsa magalimoto oledzera. “Mu 1983,” inalengeza motero Reader’s Digest, “kumwa zoledzeretsa . . . kunathera [United States] $89. 5 biliyoni mu ntchito zotaika ndi zotulutsidwa, kusamalira kwa umoyo, katundu wotaika ndi upandu, limodzinso ndi zosakazidwa zosawerengeka ku miyoyo ya banja ya awo amene anakhudzidwa.” Ndiyeno, nchosadabwitsa, kuti UN’s World Health Organization posachedwapa inavomereza kuti maboma ‘aike malire kukukhalako kwa zinthu zoledzeretsa mu chikondwerero cha umoyo ndi makhalidwe abwino a chiwerengero chawo cha anthu.’—New Nigerian, March 16, 1983.
Ena akukangana ngakhale kaamba ka kuletseratu. Mtsogoleri wa chipembedzo wa ku Nigeria wogwidwa mawu pamwambapo analengeza kuti: “Miyambo 20:1 imanena mwachindunji kuti awo amene amamwa vinyo siali a nzeru.” Ndipo anatsimikizira wolalikira winanso kuti: “Malemba Oyera amaletsa kumwa zoledzeretsa mu bukhu la Yesaya,” akumalozera ku mawu a pa Yesaya 5:11, 12, ndi 22.
M’chiyang’aniro cha zilengezo zoterozo, anthu amadabwa: Kodi nchiyani chimene mawu Amalemba oterowo amatanthauza? Kodi Baibulo kwenikwenidi limandandalika kuletsa kwa kumwa zoledzeretsa? Kodi Yesu iyemwini sanamwepo vinyo kapena kodi madzi a mphesa osaledzeretsa anaphatikizidwamo? M’chiyang’aniro cha ngozi zodziwikiratu zophatikizidwa, kodi chingakhale chabwino koposa kwa Akristu kusala kumwa zakumwa zoledzeretsa? Mayankho ku mafunso awa angapezeke mwa kuyang’ana mu Baibulo ilo leni.