“Bukhu Iri liyenera kulandira Mphatso“
Kalata yotsatirayi inalandiridwa kuchokera ku East Orange, New Jersey, U. S. A.
“Wokondedwa Bwana:
“Posachedwapa ndinali ndi chisangalalo cha kuwerenga bukhu lakuti Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Oeation? Ndinalitenga ilo mwangozi pamene ndinali kugwira ntchito mu chipinda cha makalata pantchito yanga. Ndipo ndinaganiza kuti bukhulo linali losangalatsa kwambiri. Anthu amene anakonzekeretsa ntchito yozizwitsa kwambiri imeneyi ayenera kuyamikiridwa. Sindipereka ziyamikiro zaulere, koma iwo kwenikwenidi ali ndi ziyamikiro zanga.
“Ndiri ndi ana akazi awiri okongola kwambiri, wa zaka khumi ndi chimodzi ndi wa zisanu ndi ziwiri. Ndiri wotsimikizira kuti bukhuli lidzatsimikizira kukhala chida chamtengo wapatali ku maphunziro awo oyambirira amene akulandira tsopano. Bukhulo linalembedwa bwino kwambiri ndi zilembo zazikulu—zazikulu kaamba ka maso a Atate Okondedwa a okalamba. Bukhuli liyenera kulandira mphatso [mfupo] chifukwa chakuti liri lokongola kwambiri, lokhala ndi zisonyezero zabwino koposa ndipo loyalidwa mwadongosolo. . . . Chonde ndiuzeni ndikuti ndipo ndimotani mmene ndingawordere. Ndikufuna makope atatu, chotero chonde tumizani maformu owordera ndi mitengo mwamsanga monga mmene kungathekere.”
Mungapeze kope ya chofalitsidwa chabwino kwambiri chimenechi mwakudzaza ndi kutumiza kasilipi kotsatiraka limodzi ndi chopereka cha K20. 00 yokha.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu la masamba 256 Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Ndatsekeramo K20. 00.