Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi Yehova ndi Yesu ali amene akutanthauzidwa pa Miyambo 30:4, pamene pamafunsa kuti: “Dzina lake ndani? Dzina la mwana wake ndani?”
Versi limeneli limachipanga icho kukhala chodziwikiratu mmene munthu aliri ndi nzeru zochepa m’kulinganiza ndi Wam’mwambamwamba. Funso lake longofunsidwa mosayembekezera yankho lingafunsidwe ponena za munthu aliyense, koma mafunso amenewa ayenera kutsogolera munthu wolingalira kwa Mlengi.
Wolemba Aguri anafunsa: “Ndani anakwera kumwamba natsikanso? Ndani wakundika nafumbata mphepo? Ndani wamanga madzi m’malaya ake? Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko? Dzina lake ndani? Dzina la mwana wake ndani, kapena udziwa?“—Miyambo 30:1, 4.
Palibe munthu wopanda ungwiro anapitapo kumwamba ndi kutsikanso ndi nzeru za chilengedwe chonse; ndipo kulibenso munthu aliyense amene ali ndi kuthekera kwa kulamulira mphepo, nyanja, kapena mphamvu za matanthwe zomanga dziko. M’chenicheni, Aguri anafunsa kuti: ‘Kodi mumadziwa dzina kapena mzera wa banja wa munthu aliyense amene anachitapo ichi?’ Tiyenera kuyankha kuti ayi.—Yerekezani ndi Yobu 38:1-42:3; Yesaya 40:12-14; Yeremiya 23:18; 1 Akorinto 2:16.
Chotero, tiyenera kuyang’ana kunja kwa mtundu wa anthu kupeza wina wake amene ali ndi mphamvu yoposa ya munthu ya kulamulira mphamvu za chilengedwe. Ngakhale kuli tero, sitiri olekezera pa kuphunzira ponena za iye mwa kuyang’ana zokwaniritsa zake. (Aroma 1:20) Ichi chiri chifukwa chakuti, monga mmene kunaliri, iye watsikira ndi chidziwitso ponena za iyemwini ndi zintchito zake. lye wapereka chidziwitso chachindunji. lyeanachita ichi, mwachitsanzo, pamene iye ‘anatsika’ kupereka Lamulo kwa Mose pa Phiri la Sinai. (Eksodo 19:20; Ahebri 2:2) lye wathandizanso atumiki ake kuyamikira dzina lake latanthauzo, Yehova. (Eksodo 3:13, 14; 6:3) Pambuyo pake, iye anazindikiritsa Mwana wake, yemwe anatchedwa Yesu ndi amene m’chenicheni anatsika kuchokera kumwamba ndi chidziwitso chowonjezereka ponena za Mlengi.—Yohane 1:1-3, 14, 18.
Ichi chiyenera kutithandiza ife tonse kufikira mapeto ena ake: Mofanana ndi Aguri, sitingapeze nzeru yeniyeni kuchokera ku magwero athuathu. (Miyambo 30:2, 3) Ndipo sitingathe kutchula dzina la munthu aliyense yemwe ali ndi mphamvu zoposerapo kapena chidziwitso. Chotero, tiyenera modzichepetsa kuyang’ana kwa M’modzi amene ali wokhoza kupereka chidziwitso chimene timachifuna. Uyu ali Wopatulikitsa, amene dzina lake tingalidziWe ndi amene Mwana wake anafa kotero kuti tiwomboledwe ndi kupeza moyo wosatha.—Mateyu 20:28.