Ufulu wa Chipembedzo Usungidwa mu India
MLANDU wa pa August 11, 1986, wa pa Bwalo Lalikulu Koposa la Milandu mu New Delhi unadzidzimutsa mamiliyoni. Panthaŵi imene utundu unali kukhala wamphamvu, ochepa anayembekezera kuti ufulu wa chipembedzo wa kagulu kochepa kosadziŵika ka chipembedzo udzalemekezedwa. Koma pambuyo pa kusanthula kosamalitsa kwa nsonga, bwalo la milandu lapamwamba la ku India linalamula kuti ana a Mboni za Yehova sangakakamizidwe kuimba nyimbo ya utundu. M’chosankha chosamalitsa bwalo la milandulo linanena kuti:
“Tiri okhutiritsidwa, m’nkhani yaposachedwayi, kuti kuchotsedwa kwa ana atatu kuchokera ku sukulu kaamba ka chifukwa chakuti chifukwa cha kusunga mosamalitsa chikhulupiriro chawo cha chipembedzo, iwo sagwirizana m’kuimba nyimbo ya utundu pa kusonkhana kwa m’mawa ngakhale kuti iwo amaimirira mwaulemu pamene nyimboyo ikuimbidwa, kuli kulakwira kwa kuyenera kwawo koyambirira ‘ku ufulu wa chikumbumtima ndi kudzinenera kwaufulu, kuchita ndi kusatsa chipembedzo.’”
Woweruza O. Chinnappa Reddy ndi Woweruza M. M. Dutt a pa Bwalo Lalikulu Koposa la Milandu la ku India anali oweruza amene anamva umene tsopano uli mlandu wotchuka wa nyimbo wa Mboni za Yehova.
Mmene Nkhaniyo Inabukira
Chifupifupi theka la Mboni za Yehova 8,000 mu India zimapezeka mu boma laling’ono la Kerala ku mbali ya kum’mwera ya mtundu waukulu umenewu. M’sukulu zambiri kumeneko, nyimbo ya utundu imaimbidwa tsiku ndi tsiku. Mwambo mu sukulu yapadera imene ikutchulidwa pano unali wakuti ophunzira onse adziyimba nyimboyo mogwirizana. Ana a Mboni za Yehova, ngakhale kuli tero, anagoima kokha pamene enawo anaimba. Monga mmene chiweruzo cha Bwalo Lalikulu Koposa la Milandu chinanenera: “Palibe wina aliyense amene anasamala. Kulibe aliyense amene anadandaula. Palibe aliyense amene anachinganizira icho kukhala chopanda ulemu kapena chosasonyeza utundu. Anawo anasiidwa m’mtendere ku zikhulupiriro zawo.” Uwu unali mkhalidwe kwa zaka zambiri.
Kenaka inafika July 1985. Chiwalo cha Bungwe Lopanga Malamulo a Boma chinatsutsa kuti iye anaganiza kuti icho chinali chosayenera kwa aliyense kukana kuimba nyimbo ya utundu. Kukambitsirana kunatsatirapo, ndipo zimene anakambitsirana zinafalitsidwa mu manyuzipepala ambiri otchuka a m’dzikolo.
Olamulira a masukulu ambiri mu Kerala, amene kufikira panthaŵi imeneyo anali kumverera chisoni ana a Mboni za Yehova, anachita mantha chifukwa cha kutsutsa kwa Bungwe Lopanga Malamulo ndi kufalitsa kotsutsa. Monga chotulukapo chake, ana a Mboni za Yehova anachotsedwa kuchokera pa sukulu limodzi ndi linzake.
Ana Alimbana ndi Boma
V. J. Emmanuel, amene ana ake atatu a ang’ono Bijoe, Binu Mol, ndi Bindu, anachotsedwa pa sukulu, anafuna chiwongolero chalamulo. Mr. Emmanuel anali wokhutiritsidwa kuti lamulo linali ku mbali yawo, Iwo anadziŵa kuti, molingana ndi Mbali ya Lamulo 25 (1) ya Lamulo la India, “anthu onse mofanana ali ndi ufulu wa chikumbumtima ndi kuyenera kwa kudzinenera mwaufulu mwakuchita ndi kupititsa patsogolo chipembedzo.”
Kenaka Dipatimenti yowona pa kuchitika kwa chiweruzo Mchilungamo ya Bwalo Lalikulu la Milandu la Kerala linamva nkhaniyo, koma inakana pempho la V. J. Emmanuel. Ichi chinali chodzidzimutsa kwambiri chifukwa Lamulo la India silinena kuti nyimbo ya utundu iyenera kuimbidwa kusonyeza ulemu kaamba ka iyo. Limangonena kokha kuti nzika ziyenera “kugwirizana ndi Lamulolo ndi kulemekeza malingaliro ake ndi malamulo, Mbendera ya Utundu ndi Nyimbo ya Utundu.” Palibe nkomwe lamulo lina lofunsa nzika zonse za India kuimba nyimbo ya utundu.
Nkhaniyo inapititsidwa ku Bwalo Lalikulu Koposa la Milandu la India. Mu kulamulira kopambanitsa mu Bwalo Lalikulu la Milandu la Kerala, chiweruzo cha Bwalo Lalikulu Koposa la Milandu chinanena kuti: “Bwalo Lalikulu la Milandu linadzisokeretsa ilo lokha ndi kuchoka pa nsonga yeniyeni. Iwo analingalira, mu tsatanetsatane weniweni, liwu lirilonse ndi lingaliro la Nyimbo ya Utundu ndi kumaliza kuti palibe liwu lirilonse kapena lingaliro mu Nyimbo ya Utundu limene lingalakwire ziyeneretso za chipembedzo cha aliyense.” Komabe, monga mmene Bwalo Lalikulu Koposa la Milandu molondola linadziŵira, “chimenecho sindicho chochititsa nkomwe.”
Nkhani iri ya chipembedzo, yakuti, kuyenera kwa aliyense kusunga ufulu wa kulambira. Nsonga iri yakuti, Mboni za Yehova sizimaimba nyimbo ya utundu m’dziko lirilonse. Nyimbo zoterozo ziri, m’chenicheni, nyimbo kapena mapemphero oikidwa m’kuimba, ndipo Mboni za Yehova mowona mtima zimatsutsa kuimba izo. “Izo zimakana kuimba kwenikweni,” chiweruzo cha Bwalo Lalikulu Koposa la Milandu ya India momvetsetsa chinalongosola kuti, “chifukwa chakuwona mtima kwawo kwa chikhulupiriro ndi mokhutiritsidwa kuti chipembedzo chawo sichimavomereza iwo kugwirizana m’miyambo kokha ngati iri mapemphero kwa Yehova Mulungu wawo.”
Mwachiwonekere, Lamulo la India limapereka mwaŵi “ku ufulu wa kulankhula ndi kulongosola,” womwe umaphatikizapo ufulu wa kukhala chete. Chimenecho ndi chimene anawo anali kuchita pamene nyimboyo inali kuimbidwa mkati mwa kusonkhana kwa m’mawa pa sukulu—iwo anakhala chete. Komabe, olamulira a maphunziro pa Kerala m’chenicheni, anali kuika chiletso pa kukhala chete. Chotero funso linabuka kuti kaya chiletso chotero chinali chogwirizana ndi kuyenera koperekedwa ndi Lamulo.
Bwalo Lalikulu Koposa la Milandu linamaliza pankhaniyi kuti: “Tinganene kamodzi kuti palibe kakonzedwe ka lamulo kamene kamayeneretsa aliyense kuimba Nyimbo ya Utundu ndiponso sitikuganiza kuti chiri kupanda ulemu ku Nyimbo ya Utundu ngati munthu amene aimirira mwaulemu pamene Nyimbo ya Utundu ikuimbidwa sakugwirizanamo m’kuimbako.”
Monga mmene chawonekera poyambirirapo, thayo la nzika iriyonse, molingana ndi Lamulo, liri ‘kulemekeza Nyimbo ya Utundu.’ Ponena za ulemu woterowo, Prevention of Insults to National Honor Act of 1971 inanena kuti: “Aliyense amene mwadala akana kuimba Nyimbo ya Utundu kapena kupangitsa chisokonezo ku msonkhano uliwonse wolowetsedwa mu kuimba koteroko ayenera kulangidwa mwakuikidwa m’ndende pa utali umene ungafutukuke ku zaka zitatu, kapena kulipira, kapena zonse ziŵiri.” Ana a Mboni za Yehova, ngakhale kuli tero, sanaletse wina aliyense kuimba nyimbo ya utundu. Iwo sanapangitsenso chisokonezo kwa aliyense wosonkhana wodzilowetsa m’kuimba koteroko.
Chiwopsyezo ku Umodzi wa Mtundu?
Chimodzi cha chifukwa cha Bomalo chinali chakuti kuimba nyimbo ya utundu kunali kofunikira kaamba ka umodzi ndi umphumphu wa dziko. Komabe, kodi kuimba kokakamizidwa kwa nyimbo ya utundu m’chenicheni kumaperekadi kaamba ka umodzi wa dziko kapena ku umphumphu wa nzika zake?
Mosangalatsa, nyimbo ya utundu ya India iri kokha m’chinenero cha boma limodzi, ndipo chotero siimamvetsetsedwa ndi ambiri a anthu a ku India amene amaimba iyo. Chotero, kwa ambiri, kuimba nyimbo ya utundu kuli mwinamwake kopanda tanthauzo ndipo kuli, moyenerera, mwambo wopanda phindu. Mboni za Yehova sizimagwirizana mu miyambo yoteroyo. Izo zimapemphera kokha kwa Mulungu wawo, Yehova.
Chinanenedwanso kuti ngati chiweruzo cha Bwalo Lalikulu Koposa la Milandu chidzapita ku chiyanjo cha Mboni za Yehova, chidzakhala chiwopsyezo ku chisungiko chadziko. Koma Mboni za Yehova mu India ziri zochepa kwambiri, kumafika ku chiŵerengero cha kokha anthu 8,000. Kodi kagulu kochepa kameneka kangapereke chiwopsyezo ku mtundu wa anthu oposa 800 miliyoni? Pambali pa icho, Mboni za Yehova zimadziŵika kudziko lonse kaamba ka kuwona mtima kwawo ndi kumvera ku malamulo a maboma pansi pa amene iwo amakhala.
Mu Nigeria loya ananena kuti: ‘Mboni ziri nzika zopereka msonkho ndi zomvera lamulo. Mboni iriyonse imene ingakhale yowona mtima ku chipembedzo chake ku utali wa kumvera icho pa chiwopsyezo chakutaya mwaŵi winawake mofananamo ingakhale yowona mtima mu zinthu zina zambiri. Chifukwa chimene amakanira kuba ndalamama za boma pamene ena a anzake akuimba nyimbo ya utundu ndipo panthaŵi imodzimodziyo akuba ndalama chiri chakuti Baibulo lake limene limamufunsa iye kusaimba nyimbo ya utundu limamuuzanso kuti sayenera kuba.’
Mawu omalizira a chiweruzo chenicheni cha Bwalo Lalikulu Koposa la Milandu ali oyenerera. Iwo ananena kuti: “Tikungofuna kokha kuwonjezerako: mwambo wathu umaphunzitsa kulekerera; nthanthi yathu imaphunzitsa kulekerera; lamulo lathu limachita kulekerera; tiyeni tisasungunule icho.” Kodi boma ndi atsogoleri adzayamikira lingaliro labwino limeneli? Kodi chosankha cha Bwalo Lalikulu Koposa la Milandu chidzakhala chomalizira? Kokha nthaŵi ndi imene idzanena.
[Zithunzi patsamba 23]
Ana atatu amene mwaulemu anakana kugawanamo mu mapwando a utundu
Banja lodzipereka la ana atatuwo
Anthu awa anawerenga za nkhani ya bwalo la milanduyo, kuphunzira Baibulo, ndipo anabatizidwa