Chiwonjezeko Chabwino “Kuseri kwa Mapiri”
HAITI inali republiki yoyamba yachikuda Kumadzulo kupeza ufulu. Dzina lake limachokera ku chinenero cha chiArawak cha ku India ndipo limatanthauza “mapiri.” Indedi pali mwambi wakale wa chinenero cha Creole womwe umati: “Kuseri kwa mapiri kuli mapiri.” Aka ndi kalongosoledwe kabwino ka dziko la Haiti.
Mu zaka zaposachedwapa chinachake chodziŵika kwambiri chakhala chikuchitika kuno “kuseri kwa mapiri.” Chiŵerengero chowonjezereka chavomereza ku kulalikidwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu ndipo atenga kaimidwe kawo kaamba ka Yehova ndi Mfumu yake yoikidwa. (Yesaya 60:22) Kufika mu 1980 avereji ya chifupifupi ofalitsa 3,000 inali kuchitira ripoti utumiki wa m’munda mwezi uliwonse, ndipo ofesi ya nthambi m’mzinda waukulu wa dzikolo wa Port-au-Prince inali yaing’ono kwambiri kusamalira kaamba ka zosowa zawo. Malo atsopano anafunikira. Chotero mu November 1984 kumangidwa kwa malo atsopano kunayambika mu Santo, malo osangalatsa kunja kwa mzinda wa Port-au-Prince.
Choyamba malowo anafunikira kuchinjirizidwa ndi khoma lautali wa 1,200m. Kampani ya kumaloko inapanga zidina za simenti kaamba ka khomali, koma Mboni za kumaloko zinalembedwa ntchito, ndipo odzipereka ambiri anagwira ntchito kothera kwa mlungu, kukwaniritsa projekitiyo. Kenaka ntchito yomanga inayamba, ndipo mkati mwa nyengo ya zaka zoposa zitatu, odzipereka aunyinji oposa pa zana limodzi kuchokera ku mipingo ya mu Port-au-Prince anathandiza kothera kwa mlungu. Ziwalo za Antchito Odzipereka a Programu Yomanga ya Mitundu Yonse anabwera kuchokera ku United States, Canada, ndi maiko ena—ambiri akumadzilipirira iwo eni—kudzathandiza.
Pamene kumangako kunapita patsogolo, vuto losawonedweratu linachitika. Kumbali imodzi ya malowo, kuli phompho. Mkati mwa nyengo ya mvula, mitsinje ya madzi imasefukira m’phompholo, kupangitsa kukokoloka kwa nthaka kokulira. Ichi m’kupita kwanthaŵi chikanapangitsa kugwa kwa mpanda wozungulirawo womwe unali mbali ya malowo. Chotero khoma lochinjiriza linamangidwa m’gombe mwenimweni mwa mtsinjewo ndipo malowo tsopano ali otetezeredwa bwino kuchokera ku madzi aukali omwe amathamanga mkati mwa nyengo ya mvula.
Ndi thandizo la Yehova, malo abwino anamalizidwa. Nthambiyo inapangidwa m’mtundu wa U yopangidwa ndi simenti ndi njerwa. Mbali yake ya kumanzere iri ndi zipinda zogona zisanu ndi zitatu, chipinda chochapira zovala, ndi laibrale. Mbali ya kulamanja iri ndi mosungira mabukhu. Mbali ya kutsogolo kwa nyumbayo, malo olandirira alendo a akulu mokwanira bwino amalandira abale omwe amafika kuchokera kumbali zosiyanasiyana zadzikolo panthaŵi zosiyanasiyana mkati mwa mwezi ndi cholinga chofuna kudzatenga magazini ndi mabukhu awo kaamba ka mipingo yawo yosiyanasiyana. Kutsogoloko kulinso maofesi, chipinda chodyera, ndi kichini.
Limodzi ndi ofesi ya nthambi, Holo ya Msonkhano yatsopano yokhala chifupifupi anthu 3,000 inapangidwanso pamalowo. Mbali ziŵiri za holoyo ziri zotseguka, kotero kuti awo okhala mkati amaziziritsidwa mokhazikika ndi mpepho—mpumulo wolandiridwa kuchokera ku dzuŵa lotentha la ku Haiti. Palinso kichini yamakono, yokhala ndi ziwiya zokwanira ndi malo operekera zakumwa zoziziritsa, limodzinso ndi damu lobatiziramo ndi malo opalila matabwa. Pabwalo mosangalatsa pabzyalidwa timitengo tatifupitifupi ta kumalo otentha ndi maluŵa.
Cha kumayambiriro kwa 1987, chiŵerengero cha Mboni “kuseri kwa mapiri” chinawonjezeka kufika ku oposa 4,700. Chinali chochitika chachikulu chotani nanga kwa onse a iwo kubwera pamodzi pa January 25, 1987, kaamba ka kupereka kwa nyumba ziŵiri zabwino zimenezi! Abale ena ochokera ku maiko a kunja omwe anagwira ntchito pamalowo kumayambiriro anabwerera ndi mabanja awo kudzagawana pa chochitikacho.
Programu ya kupereka inayamba masana ndi ziwalo zosiyanasiyana za Komiti ya Nthambi zikulongosola kufunika kokulira komwe kunaliko kaamba ka nyumba zatsopano zimenezi chifukwa cha chiwonjezeko chabwino chomwe chinali kutenga malo mu Haiti. Pambuyo pa kupuma kwachidule, 5,384 opezekapo anawonetsedwa programu ya zithunzithunzi yosonyeza mbali zosiyanasiyana za ntchito yomangayo.
Pomalizira, nkhani yopereka inaperekedwa ndi Charles Molohan, woyang’anira wa gawo wochezera wochokera ku Brooklyn, New York. Mbale Molohan analankhula za kufunika kwa kumanga kaamba ka kulambira kowona kwa Chikristu. Iye analongosola mmene Nowa ndi banja lake analiri pakati pa ogwira ntchito omanga oyambirira, ndipo kumaliza kwawo gawo lawo la ntchito mokhulupirika kunatanthauza chipulumutso kaamba ka banja la anthu, limodzinso ndi kupitiriza kwa kulambira kowona padziko lapansi. Ntchito ina yomanga ya makedzana inali kachisi wa Herode, koma uyu anawonongedwa chifukwa sanagwiritsiridwe ntchito kupititsa patsogolo kulambira kowona. (Mateyu 23:38) Lerolino, tiyenera kukhala otanganitsidwa kumangirira chikhulupiriro ndi mikhalidwe ina ya Chikristu ngati tikayenera kupewa chotulukapo chofananacho.
Chinalidi chochitika chodzutsa maganizo ndi chosangalatsa. Pamene chinatha, onse amene analipo anabwerera kunyumba zawo akudziŵa kuti ntchito yomanga yatsopano imeneyi m’dzikoli “kuseri kwa mapiri” idzapitiriza kuchita ntchito yabwino m’kusonkhanitsa alambiri owona mu mbali iyi ya Caribbean.
[Zithunzi patsamba 31]
Mbali zowonekera za Holo ya Msonkhano (pamwamba kulamanja) ndi nthambi yatsopano