Kuyankha Kuitana kwa Zisumbu za Micronesia
MAINA monga Truk, Yap, Ponape, Guam, ndi Saipan angamveke ozoloŵereka kwa inu. Koma bwanji ponena za Belau, Rota, Kosrae, Nauru, kapena Kiribati? Izi ndi zina zonse ziri mbali ya zisumbu zoposa 2,000 ndipo zimakhala motalikirana mozungulira pa mtunda wa makilometer 4.8 miliyoni m’mbali zonse zinayi za Western Pacific ndipo monga gulu zodziŵika monga Micronesia, kapena zisumbu zazing’ono.
Mkati mwa dziko lalikulu limeneli, la ukulu wofanana chifupifupi ndi Australia kapena dziko lonse la United States, Mboni za Yehova ziri zotanganitsidwa kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu. (Marko 13:10) Padakali pano, ntchito imeneyi ikuchitidwa ndi ofalitsa a Ufumu chifupifupi 740 mu mipingo 13. Ndithudi, pali chifuno chokulira kaamba ka antchito ochuluka kubweretsa zokolola mu zisumbu zakutali zimenezi za m’nyanja.—Yerekezani ndi Yeremiya 31:10.
Mkati mwa zaka 20 zapita kapena zoposerapo, anthu ochokera ku Hawaii, Philippines, Canada, United States, ndi Australia ayankha ku chiitanochi ndipo atenga utumiki wa umishonale mu zisumbu za Micronesia. Pamene oyambirira a iwo anafika mu 1965, panali ofalitsa a Ufumu 76 okha m’gawo lalikulu limeneli. Mu 1987, ngakhale kuli tero, chiwonkhetso cha anthu 4,510 anapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu Kristu. Mwachiwonekere, ntchito Zachikristu zachikondi mkati mwa zaka zadalitsidwa molemerera.
Lerolino, pali amishonale 49 otumikira pakati pa nyumba za umishonale 14 zomwazikana pakati pa zisumbu, onse akugwira ntchito pansi pa chitsogozo cha nthambi ya Watch Tower Society ya Guam. Chikondi chawo kaamba ka Yehova kaamba ka anansi awo a ku Micronesia chawasonkhezera iwo kuyankha ku chiitano cha umishonale. Ndi zokumana nazo zotani zimene iwo akhala nazo pamene akutumikira mu zisumbu za kutali zimenezi? Ponena za zinenero zatsopano ndi miyambo, ndi zitokoso zotani zimene iwo anafunikira kuzilaka? Ndipo nchiyani chimene chinawathandiza iwo kuti akhalabe m’magawo awo? Tiyeni timve kuchokera kwa ena a iwo ponena za ntchito yawo mu zisumbu zimenezi.
Chitokoso cha Zinenero Zatsopano
Pali zinenero zisanu ndi zitatu kapena zisanu ndi zinayi zazikulu mu Micronesia. Koma chifukwa chakuti izi sizimalingaliridwa kukhala zinenero zolembedwa, chiri chovuta kwa amishonale atsopano kupeza mabukhu ogwiritsira ntchito kuwathandiza kuphunzira. Komabe, iwo amagwira ntchito molimbika pa icho. Njira imodzi yokhutiritsa, iwo anauzidwa, inali kuyesera kugwiritsira ntchito chimene chinaphunziridwa mwamsanga mu ntchito yolalikira. Chabwino, iwo akumbukirabe mikhalidwe yosangalatsa—ndi yochititsa manyazi—imene inabuka pamene anayesera kuchita chimenecho.
Roger, nzika ya ku Hawaii, akukumbukira mkhalidwe umodzi woterowo pamene iye anabwera choyamba ku Belau zaka 13 zapita. “Pamene mwininyumba ananena kuti, ‘Ndine m’Katolika,’ liwu lokha la chiPalau limene ndinadziŵa kuyankha linali ‘Chifukwa ninji?’” Mwininyumbayo kenaka anayamba kulongosola kwakutali. “Sindinamve liwu lirilonse limene ananena. Pamapeto ake, ndinanena liwu lina lokha limene ndinadziŵa. ‘Zikomo kwambiri,’ ndipo ndinachoka!”
Salvador, yemwe anabwera ku Truk ndi mkazi wake, Helen, zaka khumi zapitazo, amakumbukira kuyesera kufunsa mkazi wa chiTrukese ngati iye anafuna kukhala wachimwemwe (pwapwa). M’malo mwake, iye anafunsa ngati anafuna kukhala ndi pakati (pwopwo). Ndipo Zenette, yemwe anabwera kuchokera ku Canada ndi mwamuna wake, David, akukumbukira nthaŵi imene iye anayesera kunena kuti “Zikomo kwambiri” (kilisou) koma anamaliza kunena kuti “Ntchentche yomwa mwazi.” (kiliso). Mosasamala kanthu za chimenecho, iwo amadziŵa mawu onsewa bwino lomwe tsopano.
Pamene James anasamutsidwa kupita ku chisumbu cha Kosrae pambuyo pa kutumikira zaka zinayi mu Ponape, anayenera kuyambanso. Iye mwapadera amakumbukira akuyesera kukhala waubwenzi ndi mwininyumba mmodzi. Koma m’malo mofunsa kuti, “Muli bwanji?” iye anamuza kuti, “Ndiwe wopusa”! Tsopano, pambuyo pa zaka khumi, iye akunena kuti: “Poyamba, chinali chovuta kunena ena a mawu a chiKosrea chifukwa anamveka mofanana ndi mawu olumbira m’Chingelezi.”
Zokumana nazo zoterozo, ngakhale kuli tero, sizinakhumudwitse amishonale amenewa kuleka kupita patsogolo mu maphunziro awo a chilankhulo. “Pali zochepa zimene wina angachite kuthandiza anthu popanda kuphunzira chinenero,” anatero mishonale mmodzi. “Ichi chimapereka chikhumbo chenicheni cha kuphunzira mwakhama.”
Miyambo ndi Kukhulupirira Malaulo
Kwa achatsopano, yambiri ya miyamboyo inawonekera yosangalatsa. Mwachitsanzo, David anakumana ndi mwamuna amene anatcha ana ake a amuna atatu Sardine, Tuna, ndi Spam. Pambuyo pake, iye anadziŵitsidwa kwa amuna atatu omwe ankatchedwa Chikhumbo, Chimo, ndi Kulapa. Zenette anachipeza icho chachilendo kuti anthu anatchula agogo awo Papa ndi Mama ndipo makolo awo ndi maina awo oyamba. Pamene Sheri choyamba anabwera kuchokera ku Hawaii, iye anaganiza kuti chinali chosangalatsa kwambiri kuti anthu anali kugwiritsira ntchito mphuno zawo kuloza njira. Ndipo chinatenga nthaŵi yaitali kuzoloŵerana ndi mwambowo: Pamene mkazi waloŵa pa malo osonkhanirana aunyinji, iye “amayenda” pa mawondo ake kupita ku “Mpando” wake pansi kusonyeza ulemu kwa amuna.
Zambiri, nazonso, ziri zikhulupiriro za malaulo. Mu Zisumbu za Marshall, mwachitsanzo, pamene wina afa banja limaika chakudya, ndudu, ndi maluŵa pa manda a womwalirayo. Kapena pamene mbalame iuluka mozungulira nyumba ikuimba, ichi chimatengedwa kutanthauza tsoka ndi kuyandikira kwa imfa ya wina m’banjamo.
Ena mu zisumbuzo alinso olowetsedwa mozama mu kukhulupirira mizimu. Jon anali mmodzi wa iwo. Iye poyamba anali mkulu mu tchalitchi cha Protestanti, iye anali wokhoza kutulutsa mizumu mwapemphero ndi kugwiritsira ntchito mankhwala okonzekeretsedwa kuchokera ku mafuta a coconut.
“Tsiku lina nkhope yonyansa ya chiwanda yaikulu monga chitseko inawonekera pa khomo la nyumba yanga,” Jon akulongosola. Choyamba Jon anaganiza kuti anali kulota koma mwamsanga anazindikira kuti iye anali wogalamuka.
“Chiwandacho chinandiuza ine kuti chinali maziko a mphamvu zanga za matsenga. Ichi chinandidzidzimutsa ndipo chinandipangitsa ine kudabwa nchifukwa ninji ziwanda zinali kugwira ntchito kupyolera mwa ine, dikoni mu tchalitchi, ndipo nchifukwa ninji minisitala iyemwini anafuna mautumiki anga auchiwanda.” Jon mwamsanga anafikiridwa ndi amishonale a Mboni ndipo anayamba kuphunzira Baibulo.
“Chinandibweretsera ine chimwemwe chachikulu kuphunzira chowonadi ponena za ziwanda ndi mmene ndingazindikirire chipembedzo chowona,” Jon akukumbukira. Iye anachoka mu tchalitchi chake ndi kuleka kupitiriza machitachita ake auchiwanda. Lerolino iye akuchenjeza ena kupewa machitachita onse auchiwanda.—Deuteronomo 18:9-13; Chivumbulutso 21:8.
Kufikira Zisumbu Zazing’ono
Kutenga mbiri yabwino kwa anthu pa zisumbu zazing’ono za kunja chiri chitokoso chenicheni. Kaŵirikaŵiri njira yokha ya kuwafikira iwo iri kuguliratu malo pa bwato za mkati mwa coconut zowuma. Pamene bwatolo liima pa ka chisumbu kalikonse kwa maora ochepa kapena masiku kutenga katundu, amishonalewo ndi olengeza ena a Ufumu amazitanganitsa iwo eni m’kuchitira umboni kwa anthu apachisumbupo. Kuwulutsa mawu pa wailesi kwa mlungu ndi mlungu iri njira ina ya kubweretsera mbiri yabwino kwa iwo.
Nzika za pa zisumbu za kunjazo kaŵirikaŵiri zimayenda ku zisumbu zazikulu za pakati kaamba ka chakudya, chisamaliro cha mankhwala, ndi sukulu. Pamene ali kumeneko, iwo angafikiridwe ndi Mboni za Yehova ndipo angapeze mabukhu a Baibulo. Chikondwerero chimatsatiridwa ndi makalata kapena pamene ofalitsa achezera zisumbu zawo. Okwatirana aŵiri anafikiridwa mwanjira imeneyo mu Majuro mu Zisumbu za Marshall ndipo kenaka anabwerera ku chisumbu cha kwawo cha Ailuku, pamtunda wa 400 km. Iwo anayamba kupanga kupita patsogolo m’kumvetsetsa kwawo kwa Baibulo. Mwamsanga iwo anathetsa kugwirizana kwawo ndi tchalitchi chawo, kulembetsa mwalamulo ukwati wawo, ndipo anabatizidwa. Tsopano onse aŵiri mwachangu akulalikira pa chisumbu chawo chakutali, kaŵirikaŵiri akumatumikira monga apainiya othandizira.
Amishonale mu Ponape, Truk, ndi Belau amagwiritsira ntchito mabwato awo kaamba ka kuchitira umboni wa pa zisumbu. Popeza palibe malo okocheza m’malo ambiri, iwo kaŵirikaŵiri amayenera kuyenda kupita kugombe m’matope ofika m’mawondo awo. Nzika zambiri ziri zaubwenzi ndipo zimalandira alendowa mwakuyala mphasa kaamba ka iwo ndi kuwapatsa iwo madzi ozizira a coconut. Banja lonse limaitanidwa ndipo limamvetsera mosamalitsa. Chifukwa chakuti ambiri sakhala ndi ndalama, sichiri chachilendo kuwona ofalitsa akubwerera pambuyo pa masiku aŵiri kapena atatu ndi mabwato awo atadzaza ndi zipatso zolandiridwa m’kusinthana ndi mabukhu a Baibulo.
Kudzipereka Nsembe ndi Mphoto
Kwa amishonale, moyo mu zisumbu suli wofanana ndi mmene unaliri kunyumba. Iwo anayenera kuzoloŵerana ndi kusoweka kwa magetsi ndi kuperewera kwa madzi, akumadalira pa madzi a mvula kaamba ka madzi awo. Pa zisumbu zina, palibe dongosolo la magetsi, madzi, kapena zimbudzi, palibe misewu ya tara, ndipo palibenso magalimoto. Koma amishonale aphunzira kukhala okhoza kusintha. “Pamene ndiwona abale akumaloko akukhala m’nyumba zomangidwa ndi mitendo yotaidwa ndi matabwa oika pansi, timadzimva achifundo kaamba ka iwo, ndipo ichi chimathandiza kutipanga ife kukhala olinganizika m’zosowa zathu ndi zofuna,” akuwona tero Julian, yemwe watumikira mokhulupirika kwa zaka 17 mu Guam ndi Zisumbu za Marshall.
Rodney ndi Sheri anabwera ku Truk kuchokera ku Hawaii. Iye akuvomereza: “Mowona mtima, ndinakumana ndi kudzidzimutsidwa kwa mwambo.” Tsopano, zaka khumi pambuyo pake, iye akulemba kuti: “Tiri ndi ntchito yokhutiritsa kwambiri yoti tiichite kuno. Tiri ndi zinthu zabwino ndi zokhumudwitsa; nthaŵi zina timadzimva kukhala okhumudwitsidwa ndi osungulumwa. Koma tikufuna kupitiriza kulondola cholinga chathu m’moyo m’ntchito ya umishonale kuno.” Ndipo Sheri mosangalala akuwonjezera kuti: “Anthu odzipereka mwaumwini ali anthu achimwemwe.”
Ndithudi, kudzipereka kwawo kwaumwini kukufupidwa molemerera. Clemente ndi mkazi wake, Eunice, omwe anabwera ku Zisumbu za Marshall zaka khumi zapita, tsopano amatsogoza maphunziro a Baibulo apa nyumba 34 pa mlungu. “Khumi ndi anayi a ophunzira awo asonyezera kudzipereka kwawo kwa Yehova mwakumizidwa m’madzi,” iye akusimba tero, “ndipo enawo akupita patsogolo kulinga ku ubatizo. Ntchito yopulumutsa moyo yoteroyo iri ndi phindu lalikulu m’maso mwathu.” James, mishonale kwa zaka zoposa khumi, akunena kuti: “Kuwona kupirira kwa abale athu a ku Kosrea chaka ndi chaka kuli dalitso lenileni.” Mu Belau, Roger akuchitira ndemanga kuti: “Tadalitsidwa ndi Nyumba ya Ufumu yatsopano ndi gulu lomvera la ofalitsa.” Ndipo kuyang’ana m’mbuyo mkati mwa zaka, Placido akunena kuti: “Chitsogozo cha Yehova ndi mzimu woyera zatsimikiziridwa m’miyoyo yathu. Ichi chatithandiza ife kutsendera kufupi kwa iye.”
Zokumana nazo zoterozo zalimbikitsa amishonale kukhalabe m’magawo awo. Ambiri a iwo angayang’ane m’mbuyo ndi kukumbukira kupangidwa kwa mpingo woyamba m’dera lawo. Mofanana ndi mtumwi Paulo, iwo ali ndi chimwemwe chapadera ‘cha kusamanga pa maziko a munthu wina.’ (Aroma 15:20) Kudzimva kwawo kukulongosoledwa bwino ndi ndemanga iyi: “Padakali ntchito yambiri yoti ichitidwe. Ndikhulupirira kuti Yehova adzatsegula mwaŵi wambiri kubweretsa ena ambiri onga nkhosa mu zisumbu izi, ndipo tiri ndi mwaŵi kugawana mu icho.”
“Madalitso a Yehova—alemeretsa, sawonjezerapo chisoni,” likutero Baibulo pa Miyambo 10:22. Awo amene ayankha ku chiitano cha umishonale mu zisumbu za Micronesia mowonadi akumana ndi dalitso limeneli limodzi ndi chimwemwe ndi zikhutiritso zomwe zimabwera kuchokera ku kutumikira Yehova.