Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 11/15 tsamba 30-31
  • Kuchokera ku Ukapolo wopanga Njerwa kupita ku Ufulu!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchokera ku Ukapolo wopanga Njerwa kupita ku Ufulu!
  • Nsanja ya Olonda—1987
Nsanja ya Olonda—1987
w87 11/15 tsamba 30-31

Kuchokera ku Ukapolo wopanga Njerwa kupita ku Ufulu!

KODI mapyramids a ku Giza (apafupi ndi Cairo wamakono) amabweretsa kumalingaliro kugwiritsira ntchito molakwa akapolo pansi pa dzuŵa lotentha kukokera miyala yaikulu m’malo ake? Ndipo kodi m’malingalira akapolo a Chihebri pakati pa iwo?

Kwenikweni, mapyramids a Aigupto owonedwa pa tsamba lotsatirapo anakhalako pambuyo pa nthaŵi imene banja la atate a Yosefe Yakobo (kapena, Israyeli) anasamukira ku Aigupto. Koma chimene chinagwiritsiridwa ntchito mofala kwambiri kupambana kumanga ndi miyala yaikulu chinali kugwiritsira ntchito kwa njerwa, zopangidwa ndi mamiliyoni pansi pa dzuŵa lotentha limodzimodzilo.

Ahebri omwe analandiridwa mu Aigupto mkati mwa nthaŵi ya Yosefe anadalitsidwa ndi Mulungu ndi kuchuluka, kubweretsa chiwopsyezo kwa anthu a ku Aigupto. Timaŵerenga: “Chotero anawaikira [Ahebri] mafumu amphamvu kaamba ka chifuno cha kuwasautsa iwo ndi akatundu awo; ndipo anamanga mizinda . . . Aigupto anawagwiritsa ana a Israyeli ntchito yosautsa. Nawaŵitsa moyo wawo ndi ntchito yolimba ya dothi ndi ya njerwa.”​—Eksodo 1:7-14.

Kulamanja, mungawone kuti njerwa zikali kupangidwa mu Igupto, zina zikuphikidwa mu ng’anjo zonga zimene zikuwoneka pano. (Yerekezani ndi Genesis 11:1-3; 19:28) Mwachiwonekere, ngakhale kuli tero, njerwa zakale za ku Igupto zinali kuumitsidwa ndi dzuŵa. Chomwe chikupitiriza chiri kugwiritsira ntchito udzu m’kupanga njerwa. Udzu umawoneka mu njerwa zopezedwa mu mabwinja a Beereseba wakale (chithunzi chomwe chikuwoneka mkati).

Kuphatikiza udzu kunalimbitsa njerwa. Kuti azipange, matope (kapena makande), madzi, ndi udzu zinali kupondedwa mwapang’onopang’ono ndi mapazi, kenaka kuikidwa mu zikombole, ndipo pomalizira zinali kuyanikidwa kuti ziume. Tangolingalirani kugwira ntchito yoteroyo tsiku limodzi lalitali pambuyo pa linzake. Zowonadi, mungamvetsetse chifukwa chimene Aisrayeli ‘anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wawo, nalira, ndipo kulira kwawo kunakwera kwa Mulungu [wowona, NW] chifukwa cha ukapolo wawo.’​—Eksodo 2:23.

Yehova anawamva iwo ndipo anatumiza Mose kwa Farao kukatengera Aisrayeli ufulu. M’malomwake, Farao wodzitama anawonjezera katundu wawo. Tsopano anayenera kudziperezera okha udzu, akusungilira unyinji wa njerwa monga kale. Nkulekeranji, popeza ichi chinali monga chilango cha imfa! Mulungu ananena kuti: “Tsopano udzawona chomwe ndidzachitira Farao, pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite.”​—Eksodo 5:1–6:1.

Mwinamwake mumadziŵa zotsala. Yehova anali ndi mphamvu za kugonjetsa Farao wodzikwezayo. Pambuyo pa mliri wa chikhumi, Mulungu ‘anatulutsa ana a Aisrayeli mu dziko la Aigupto.’ (Eksodo 12:37-51) Mwakusiya kumbuyo mapyramid, njerwa, ndi ukapolo waukali, Aisrayeli anayenda kulinga ku Dziko Lolenjezedwa. Nsonga za mbiri yakale zimenezi ziyenera kutitsimikizira ife za kuthekera kwa Yehova Mulungu m’kupanga ufulu wowona kwa Akristu m’dziko latsopano likudzalo, ndi Paradaiso wake wa padziko lapansi.​—Yerekezani ndi Aroma 8:20, 21.

[Chithunzi chachikulu patsamba 31]

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

Photos, pages 30, 31: Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena