‘Linandithandiza Kwambiri’
Achichepere ndithudi amafunikira thandizo lerolino, ndi kufalikira kwa kudzipha kwa achichepere, mimba, uchidakwa, kugwiritsira ntchito anamgoneka molakwika, ndi mavuto ena. Koma nkuti kumene iwo angapeze ilo? Wachichepere wochokera ku Buffalo, New York, analembera Watchtower Society:
“Ndaŵerenga bukhu lanu . . . Your Youth—Getting the Best Out of It. Ndiyenera kunena kuti mwalemba bukhu labwino. Landithandiza ine kwambiri ndipo ndikudziŵa kuti lingachite chofananacho kwa winawake. . . . Ndapereka bukhu langa kwa bwenzi langa, ndipo iye wapanga kupita patsogolo. Zikomo kwambiri, Bwana, kuŵirikiza nthaŵi miliyoni, kaamba ka kulemba bukhu labwino kwambiri limenelo.”
Nanunso mungalandire bukhu la chikuto cholimba la mtengo wapamwamba limeneli kaamba ka anthu achichepere mwakungodzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka, limodzi ndi chopereka chanu.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu la chikuto cholimba, la masamba 192 Your Youth—Getting the Best out of It. Ndatsekeramo K8.00.