Kulengeza—Chimene Kungakwaniritse
KWA zaka zingapo tsamba lothera la Nsanja ya Olonda lanyamula kulengeza kwa zofalitsidwa za Baibulo. Posachedwapa, kalata yochokera ku Georgia, U.S.A., inalemekeza kulengeza kumeneko. Wolembayo analongosola kuti anthu aŵiri okwatirana amene mkazi ndi mwamuna wake amaphunzira nawo Baibulo ayankha ku zilengezo zimenezi ndipo apeza, pakati pa zofalitsidwa zina, matepi a makaseti a Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo (Chingelezi). Pambuyo pake, iwo anagula bukhu la Nkhani za Baibulo lenilenilo. Mlembiyo akulongosola zotulukapo zimene bukhu limeneli lakhala nazo pa aŵiriwo:
“Iwo apatsidwa chiyambi cha mbiri yakale kuchokera pa Adamu kupita mtsogolo chakuti kokha mlungu uno kwatulukapo kukhala kwawo okhoza kuwona mafuko osiyanasiyana a anthu mlingaliro loyenera. Pambuyo pa kuŵerenga malemba angapo, monga ngati Machitidwe 17:26 ndi Genesis mutu 10, ndi kulozera ku mbiri yakale ya munthu kuchokera mu bukhu la Nkhani za Baibulo, Jim anawona kuti: ‘Ndinanena kuti sindinali wa tsankho ndi kale lonse, koma kwa nthaŵi yoyamba, usiku uno ndingakhoze kuchinena icho ndipo ndithudi kutanthauza chimenecho.’”
Mlembiyo anatsiriza kuti: “Ndithudi, kulengeza kwanu kwatsogolera ku kukula kwauzimu kokulira m’nthaŵi yochepa.”
Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo liri ndi nkhani za m’Baibulo 116 zimene zimapereka kwa woŵerengayo lingaliro la chimene Baibulo liri. Inu mungalandire makaseti a tepi (Chingelezi), kapena volyumu ya Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kapena zonse ziŵiri mwakungodzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Chongani chimodzi kapena zonse ziŵiri za zotsatirapozi ndi kutumiza chopereka choyenera:
[ ] Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, alubamu ya mawonekedwe ofiira pang’ono yokhala ndi makaseti anayi a Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo (Chingelezi). Ndatsekeramo K54.00. (Kunja kwa Zambia lemberani nthambi ya Watch Tower ya kumaloko kaamba ka chidziŵitso.)
[ ] Tumizani bukhu lokhala ndi zitsanzo la masamba 256 Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, kaamba ka limene ndatsekeramo K20.00. Chonde tumizani zopereka zokwanira.