Ripoti la Olengeza Ufumu
Yehova Adalitsa Osunga Umphumphu mu Cyprus
YESU ananena kwa otsatira ake: “Ngati anazunza ine, adzazunza inunso.” (Yohane 15:20, NW) Ndipo Yehova, kupyolera mwa mneneri Yesaya, ananena kuti: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula.” (Yesaya 54:17) Kanenedwe kaŵiri konseka katsimikizira kukhala kowona mu Cyprus, kumene Mboni za Yehova zosunga umphumphu ziri zotanganitsidwa kulalikira mbiri yabwino.
◻ “Tchalitchi cha Greek Orthodox chakhala chokangalika kuyesayesa kuderera ntchito yathu,” likutero ripoti lochokera ku dziko limenelo. “Ansembe amagawira masamba osindikizidwa kutizenga ife mlandu wa zinthu za mitundu yonse ndi kuuza anthu kupewa kukambitsirana ndi Mboni za Yehova. Iwo amafikira pa kuchezera anthu amene akuphunzira Baibulo ndi Mboni ndi kuyesa kuwakhumudwitsa iwo. Mu Paphos, wansembe wodziŵa zaumulungu anayesera kukhutiritsa anthu atatu osiyanasiyana kusiya kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Pa zochitika zitatu zosiyana aliyense wa atatuwo, anaitana mbale kukakambitsirana ndi wodziŵa zaumulungu ameneyu. Mwachimwemwe, onse atatuwo tsopano ali kuyanjana mokangalika ndi gulu la Yehova.” Ichi ndithudi, chinamuipira wansembeyo, yemwe anachitira ndemanga kuti, “Sindidzakambitsirananso ndi Mboni za Yehova.” Ansembe ena anafikira pa kumenya ena a abale pamene iwo anali mu utumiki. Kaŵirikaŵiri, ngakhale kuli tero, zoyesayesa za atsogoleri a chipembedzo zimalephera, ndipo anthu ambiri tsopano akutenga kaimidwe kawo kaamba ka Yehova.
◻ Chokumana nacho chotsatirachi chochokera ku Cyprus chimasonyeza kuti kusunga umphumphu pansi pa chitsutso kumabweretsa madalitso. Mwamuna wa mkazi wina anaphedwa mkati mwa nkhondo ya 1974, kumusiya iye ndi mtsikana wachichepere woti amulere. Mkaziyo anakwatiwanso. Wokwiitsidwa ndi kunyenga kwa atsogoleri a chipembedzo ndi kusatsimikizirika kwa mtsogolo, iye anavomereza kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Iye anapita patsogolo mofulumira ndi kuyamba kuuza achibale ake zinthu zabwino zimene anali kuphunzira. Chitsutso chinayamba. Chiyeso chachikulu kwambiri chinabwera pamene mwana wake wa mkazi wa zaka 15 zakubadwa anachitira ndemanga kuti: “Ndataya bambo wanga, ndipo ngati simusiya kuphunzira ndi Mboni za Yehova, ndidzakukanani kukhala mayi wanga. Ndidzakhala wamasiye.” Mosasamala kanthu za chimenecho, mkaziyo anapitirizabe kuphunzira.
Tsiku lina mtsikanayo anachezera bwenzi lake m’chipatala. Pa kama lina lapafupipo la m’chipatala, Mboni inali kuchezera mnansi wake pamene wansembe anabwera kudzawona wodwala mmodzimodziyo. Kukambitsirana kunayambika pakati pa mbaleyo ndi wansembe. Mbaleyo anali wodekha ndi waluso, akumagwiritsira ntchito Baibulo kulongosola kaimidwe kake. Wansembeyo, kumbali ina, anali waukali. Iye anakweza liwu lake, koma palibe ndi nthaŵi imodzi yomwe pamene anatsegula Baibulo. Mtsikanayo anawonerera chochitikacho ndipo anasangalatsidwa ndi chifundo cha mbaleyo ndi chenicheni chakuti anagwiritsira ntchito Baibulo. Madzulo amenewo, pamene mbaleyo ndi mkazi wake anachezera mayi wake kaamba ka phunziro la Baibulo, mtsikanayo analongosola chimene chinachitika ku chipatala ndi kuwafunsa iwo: “Kodi mungaphunzirenso ndi ine?” Tsopano mtsikanayo akuphunzira Baibulo kaŵiri pa mlungu, ndipo mwamunayo nayenso akuphunzira. Ndipo mayiyo ali wofalitsa wobatizidwa.
Zowonadi, Yehova akudalitsa atumiki ake osunga umphumphu mu Cyprus!
[Chithunzi patsamba 7]
Mtumwi Paulo anakumananso ndi chitsutso mu Paphos