Ripoti la Olengeza Ufumu
Mbiri Yabwino Ipambana mu Cyprus Mosasamala Kanthu za Chitsutso
MTUMWI Paulo analalikira mbiri yabwino ya Ufumu mu Cyprus (Kupro). (Machitidwe 13:4-12) Umo munali mu 47-48 C.E. Lerolino, mbiri yabwino ikulalikidwa m’chisumbu chokongola chimenechi ndi Mboni za Yehova 1,154 ndipo mu April wa chaka chino, 2,570 anapezeka pa utumiki wa Chikumbutso, chomwe chimasonyeza kuti pali owona mtima ambiri ndi anthu owopa Mulungu m’chisumbuchi. Koma pamene kuli kwakuti anthu ambiri amalandira uthenga wodzetsa mtendere wa Baibulo woperekedwa ndi Mboni za Yehova, atsogoleri achipembedzo a Greek Orthodox, mofanana ndi atsogoleri achipembedzo a Chiyuda m’tsiku la Yesu, amatsutsa ntchitoyo. (Yohane 15:20) Ofesi ya nthambi ya ku Cyprus ikulemba kuti: “Koposa ndi kalelonse, Tchalitchi cha Greek Orthodox chikusonyeza kugamulapo kwake kwa kusonkoneza ntchito yathu yolalikira.” Kenaka ripotilo likulongosola mmene atsogoleri achipembedzo amanyazitsira abale mu utimiki wawo wa kunyumba ndi nuymba ndi kuyesa kuwaputa iwo kotero kuti awapangitse iwo kulowetsedwa m’kukangana. Iwo kenaka amawapatsa mlandu wa kupangitsa msokonezo, koma abale amakana kuputidwa ndi kuchokapo.
Ndithudi, chitsutso cha atsogoleri achipembedzo kaŵirikaŵiri chimawagwera, monga mmene chokumana nacho chotsatirachi chikusonyezera: “Miyezi yoŵerengeka yapitayo, mkazi anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo posachedwapa mwamuna wake anagwirizana naye. Kenaka katswiri wa za maphunziro aumulungu anachezera okwatirana aŵiriwa, akumayembekeza kuwagonjetsa iwo kuleka phunziro lawo la Baibulo. Katswiri wa maphunziro a zaumulunguyo anayesera kulongosola Utatu kwa iwo. Pambuyo pa kanthaŵi mwamunayo anasokoneza ndi kunena kuti: “Sindikumvetsetsa mmene Yesu, tsopano yemwe ali m’mwamba m’thupi laumunthu, monga mmene inu mukunenera, akakhoza panthaŵi imodzimodziyo kukhala mmodzi ndi Mulungu yemwe ali m’mkhalidwe wauzimu.’ Yankho la katswiri wa maphunziro a zaumulunguyo linali lakuti; ‘Chabwino, iwe sufunikira kmvetsetsa chirichonse.’ Munthu wokondwerayo ananena kuti: ‘Koma ndimamvetsetsa kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu ndipo osati Mulungu iyemwini. Sindifuna kumva chirichonse chonena za Utatu.’ Pa chimenechi katswiri wa zamaphunziro aumulunguyo ananyamuka ndi kunena mwaukali kuti: ‘Wapita patali kwambiri ndi phunziro lako la Baibulo. Sungakhoze kusintha.’”
Tsopano mkaziyo akupezeka pa misonkhano yonse ndipo anabatizidwa pa Msonkhano Wachigawo wa “Khulupirirani Yehova.” Mwamunayo akuptitirizabe ndi phunziro lake ndipo akupezekapo pa misonkhano ina.
“Chotero, mosasamala kanthu za zoyesayesa zawo, atsogoleri achipembedzo sakufikiritsa chonulirapo chawo,” lalongosola tero ripoti lochokera ku ofesi ya nthambi ya ku Cyprus. “M’malomwake, chomwe tikuwona chiri chakuti anthu okondwerera ambiri tsopano akupezeka pa misonkhano kuposa ndi kalelonse. Panthaŵi imodzimodziyo, abale ali ogamulapo kwenikweni kupereka mbiri yabwino kwa anthu owona mtima.” Yehova akuchirikiza okhulupirika ake monga mmene iye analonjezera kuti adzatero pa Yeremiya 1:19: “Ndipo adzamenyana ndi iwe koma sadzakuposa, chifukwa ‘Ine ndiri ndi iwe,’ ati Yehova, ‘kukulanditsa.’”