Kukumbukira Imfa ya Yesu
Mkati mwa phwando laling’ono, Yesu Kristu anagwiritsira ntchito vinyo ndi mkate wopanda chotupitsa monga zophiphiritsira za moyo wa munthu umene iye anayenera kuwupereka nsembe kaamba ka mtundu wa anthu. Pamene anali kukhazikitsa phwando limeneli, iye ananena kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.”—Luka 22:19.
Chaka chatha, anthu 8,965,221 anakumbukira Yesu mwa kupezekapo pa Chikumbutso cha imfa yake pa misonkhano yapadera yochitidwa ndi Mboni za Yehova. Mukuitanidwa motentha kudzapezekapo pa kusunga Chikumbutso kwa chaka chino pa Nyumba ya Ufumu ya kufupi ndi kwanu. Chidzachitidwa pa Lachisanu, April 1, pambuyo pa kulowa kwa dzuŵa. Fufuzani ndi Mboni za Yehova za kumaloko kaamba ka nthaŵi yeniyeni.