Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 3/15 tsamba 30-31
  • Kupita Patsogolo Kwina m’Maphunziro a Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupita Patsogolo Kwina m’Maphunziro a Baibulo
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Sukulu Yophunzitsa Utumiki—Khomo Lalikulu Loloŵera M’ntchito Yochuluka
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Sukulu Imene Ophunzira Ake Amathandiza Anthu Padziko Lonse
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • Anali Kukondwera ndi Chilamulo cha Yehova
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 3/15 tsamba 30-31

Kupita Patsogolo Kwina m’Maphunziro a Baibulo

LACHINAYI, October 1, 1987, kunali kupita patsogolo kwina m’maphunziro a Baibulo operekedwa ndi Sosaite yadziko lonse ya Mboni za Yehova. Iyo inasonyeza kuperekedwa kwa Sukulu ya Maphunziro ya Utumiki yatsopano. Kalasi loyambirira la abale osakwatira 24 linafikapo kaamba ka kuphunzitsidwa kwapadera pa Holo yaikulu ya Msonkhano ya Pittsburgh pa Coraopolis, Pennsylvania. Eninyumba otenthedwa mtima pakati pa Mboni m’gawolo anatsegula nyumba zawo kusunga ophunzira amenewa kaamba ka nyengo yawo ya maphunziro ya milungu isanu ndi itatu.

Ophunzirawo analembetsedwa m’mawa, kulandira mabukhu awo ophunzirira limodzinso ndi malangizo otsegulira. Pa 7:30 madzulo amenewo, Holo ya Msonkhano inadzazidwa ndi Mboni zotenthedwa maganizo 1,518 zofunitsitsa kugawanamo m’kutsegulidwa koyamba kwa sukulu yatsopano imeneyi.

Albert Schroeder, chiwalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anatumikira monga tcheyamani. Pambuyo pa nyimbo ndi pemphero, iye anadziŵitsa Robert Dawson, woyang’anira wa mzinda wa Pittsburgh. Mbale Dawson motentha analandira ophunzira 24 ku Pittsburgh ndi kuyamikira mabanja 13 omwe anadzipereka kupereka malo kaamba ka iwo. Iye anakumbutsa ocherezawo kuti ukakhala mwaŵi wawo kusonyeza chikondi chimene chimakhululukira, kukhulupirira, kuyembekezera, ndi kupirira zinthu zonse. (1 Akorinto 13:7) Iye anakumbutsa ophunzirawo kuti, monga alendo, iwo ayenera kusonyeza kuyamikira, kudzichepetsa, ndi kuthandiza. M’njira imeneyi, ubwenzi ungatulukepo womwe ungathe kwa moyo wonse.

Ophunzirawo kenaka anadziŵitsidwa, aliyense akumapereka dzina lake ndi kumanena kumene anachokera ndi imene inali ntchito yake mu utumiki wa Yehova. Ena anabwera kuchokera ku Puerto Rico, Argentina, Canada, ndi Hong Kong, ambiri a iwo akumabwera kuchokera kumbali ya kum’mawa kwa United States. Pambali pa Chingelezi, ena a iwo amalankhula Spanish, French, Italian, kapena Chinese.

Tcheyamaniyo kenaka anadziŵitsa James Hinderer monga mmodzi wa alangizi. Akumazika ndemanga zake pa Mateyu 7:24, 25, Mbale Hinderer anagogomezera kufunika kwa kutsatira mwa kuchita zinthu, mwakutsatira zimene zaphunziridwa. Chotero, ophunzirawo akakhala akumanga “nyumba” yawo pa thanthwe m’malo mwa m’chenga womayendayenda.

Randall Davis, mlangizi wina, kenaka analankhula ndi ophunzirawo. Akumazika ndemanga zake pa Yesaya 54:13, iye anadziŵa kuti iwo adzakhala akuphunzitsidwa ndi Yehova kotero kuti iwo angakhale okhoza kupereka malangizo kwa ena. Iwo akafunikira kuyedzamira mwamphamvu pa “mthandizi” wowona, mzimu woyera wa Yehova Mulungu.​—Yohane 14:26.

Albert Schroeder kenaka analankhula ponena za mmene madzulowo anamukumbutsira iye za kupita patsogolo kwina m’maphunziro a Baibulo. Iye anakumbukira February 1, 1943, pamene ophunzira zana limodzi, alangizi anayi (kuphatikizapo iye), ndi alendo ochokera ku Brooklyn anasonkhana pa South Lansing, New York, kaamba ka kutsegulira kwa Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower. Zaka zoposa 44 kuyambira pamenepo, Sukulu ya Gileadi yakhala ndi dalitso la Yehova, monga mmene zikuwonekera m’kufalitsa amishonale ophunzitsidwa ndi Baibulo 6,000 padziko lonse lapansi. Mbale Schroeder kenaka anadziŵitsa maphunziro osiyanasiyana odzaphunzitsidwa mu Sukulu ya Maphunziro a Utumiki. Pakati pa awa pali Maphunziro a Baibulo, Gulu la Teokratiki (lomwe limalunjikitsa chidwi chokulira pa mathayo a oyang’anira ndi atumiki otumikira), Kuyang’anira kwa Mulungu, ndi Kulankhula Poyera. Iye anaitaniranso chisamaliro ku mabukhu ophunzirira osiyanasiyana, kuphatikizapo Reasoning From the Scriptures. Pomaliza, Mbale Schroeder anadziŵitsa kukwaniritsidwa kwa Yesaya 45:23, akumanena kuti otsutsa a chipembedzo, m’chenicheni, anali kupinda mawondo awo kwa Mulungu chifukwa anali atadziŵa kuti Mboni za Yehova ziri zolondola m’mbali za mankhwala, lamulo, ndi ndandanda ya masiku a Baibulo.

“Khalani Otsanza Paulo” unali mutu wosankhidwa ndi mlankhuli wotsatira, Karl Klein wa Bungwe Lolamulira. Iye anasonyeza mmene mtumwi Paulo mobwerezabwereza anafunsira ena kumutsanzira iye. Iye akanachita chimenecho, popeza anali kutsanzira Kristu. (1 Akorinto 11:1) Ophunzirawo anachenjezedwa kutsanzira Paulo m’chidziŵitso chake ndi luso m’kugwiritsira ntchito Malemba, kulimba mtima kwake ndi changu polalikira, m’kupanda dyera kwake, m’kudekha kwake ndi kudzichepetsa, ndi m’kupirira kwake moleza mtima.

Theodore Jaracz, yemwenso ali chiwalo cha Bungwe Lolamulira, kenaka anapereka nkhani ya kupereka, “Sukulu Yatsopano​—Kaamba Ka Chifuno Chanji?” Iye anayamba mwa kuwona kuti awo amene anadzipereka kaamba ka sukuluyi anavomereza kutumikira kulikonse kumene angafunidwe m’munda wa dziko lonse. Ndi mboni zoposa mamiliyoni atatu ndi kota mu mipingo yoposa 54,000, pali chifuno chokulira kaamba ka amuna oyeneretsedwa kuweta, kuphunzitsa, ndi kutenga chitsogozo mu ntchito yokulira yolengeza. Papitapo, Yehova ananeneratu kuti iye adzapereka “zaufulu mwa anthu.” (Masalmo 68:18) Iye anachita ichi mu nthaŵi za atumwi, monga mmene chalongosoledwera ndi mtumwi Paulo pa Aefeso 4:8-11. Lerolino, Yehova akupereka ‘zaufulu mwa anthu’ ndipo akuphunzitsa ena a iwo kupyolera mwa sukulu yatsopanoyi.

Mbale Jaracz mowonjezera anadziŵitsa kuti pamene ophunzira onse ali ndi kuthekera kwachibadwa, Kristu angasonkhezere izi. Koma icho chimatenga kuyesetsa. Ndipo mlankhuliyo analongosola chidaliro kuti ophunzira 24 adzapanga kuyesayesa kumeneko. Iye analoza kuti sipangakhale kupatuka kuchokera ku miyezo yolungama ya Yehova ndipo ananena kuti awo otenga chitsogozo angathandize mwachitsanzo chawo chaumwini ndi chisonkhezero. M’mbali zambiri zadziko lapansi, pali chifuno chokulira kaamba ka amuna oyeneretsedwa kulandira mathayo a gulu. Chifuno chimenechi chimaphatikizapo ngakhale mipingo yaikulu yomwe ingakhale kokha ndi mkulu mmodzi kapena aŵiri ndi chiŵerengero chochepa cha atumiki otumikira. Chotero chiri chomvekera chifukwa chimene Sukulu ya Maphunziro a Utumiki inafunikira kukhazikitsidwa​—kuphunzitsa akulu ndi atumiki otumikira osakwatira kutumikira kulikonse m’munda wa dziko lonse. Monga chotulukapo cha kuphunzitsidwa kwawo, iwo adzakhala okonzekeretsedwa bwino kusamalira kaamba ka chiwonjezeko monga abusa.

Mboni zonse za Yehova zingapereke chiyamiko kwa Mulungu kaamba ka kupanga Sukulu ya Maphunziro a Utumiki kukhala yothekera. M’kumaliza, Mbale Jaracz ananena kuti: “Ndiri wotsimikizira kuti tonsefe tiri ogwirizana m’malingaliro ndi m’kudzimva kulinga kwa Yehova monga momwe zasonyezedwera pa Masalmo 79:13: ‘Potero ife anthu anu ndi nkhosa za pabusa panu tidzakuyamikani kosatha; tidzafotokozera chilemekezo chanu ku mibadwo mibadwo.’” Kenaka, ndi nyimbo ndi pemphero, chochitika chokumbukika ndi chachimwemwe chimenechi chinafika kumapeto.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena