Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 5/15 tsamba 28-31
  • Khomo Lotseguka ku Zisumbu za San Blas

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khomo Lotseguka ku Zisumbu za San Blas
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Gulu Lokhala ndi Sihalas
  • Ulendo ku Chisumbu cha Dog
  • Ku Msasa ndi Msasa mu Achutupu
  • Zovala Zokongola za Kuna
  • Ntchito Yakwaniritsidwa
Nsanja ya Olonda—1988
w88 5/15 tsamba 28-31

Khomo Lotseguka ku Zisumbu za San Blas

NDEGE ya mainjini aŵiri inazungulira pamwamba pa bwalo loterapo laling’ono m’mphepete mwa gombe. Woyendetsa ndegeyo analengeza kuti msewu wa ndegeyo unali wodzazidwa ndi madzi ndipo sichikakhala chachisungiko kutera. Koma akumapanga kafikiridwe kena, iye analingalira kubweretsa ndegeyo pansi. Pamene ndegeyo inagunda pansi, iyo inadumpha m’mphepete mwa msewu wa miyala, ikumakavulira unyinji wa madzi m’mwamba mlengalenga. Pamene iyo kenaka inaima, tinapuma mpweya wa mpumulo. Kudera nkhaŵa kwathu kunatembenukira ku chimwemwe pamene tinawona mabwenzi athu akutiyembekezera.

Iwo anabwera kuchokera ku chisumbu cha Ustupu, chifupifupi makilomita 1.6 kugombe. Icho chiri chimodzi cha Zisumbu za San Blas, ndandanda ya tizisumbu 350 tomaika madontho ku gombe la kumpoto chakum’mawa kwa Panama kufikira ku malire a Colombia. Zisumbu zimenezi ziri zokhalidwa ndi chifupifupi anthu a chiMwenye 50,000 afuko la Kuna. Tinabwera ndi ntchito.

Gulu Lokhala ndi Sihalas

San Blas iri comarca, kapena gawo logawidwa, la Republic ya Panama. Chisumbu chirichonse chimalamuliridwa ndi Sahilas wakewake, mtundu wa bungwe la kumaloko lopangidwa ndi ziwalo zazimuna zachikulire za m’mudzimo. Oimira ochokera ku Sahilas amapanga bungwe lotchedwa Caciques, lomwe limalamulira pa comarca yonse.

Chiyambire 1969, Mboni za Yehova zakhala zikulalikira mbiri yabwino ya Ufumu mu San Blas, ndipo chifupifupi anthu 50 tsopano amapezeka pa misonkhano yathu. (Mateyu 24:14) Ngakhale kuli tero, olamulira a kumaloko anatikaniza ife chilozero cha kulalikira pa zina za zisumbuzo. Posachedwapa, maSahilas a Ustupu, chisumbu chachiŵiri chokhala ndi anthu ambiri koposa pa gululo, anapempha kufunsana ndi Mboni za Yehova ndi cholinga chofuna kugamulapo kuti kaya atipatse kuzindikiridwa kwa lamulo kapena ayi. Chinawoneka kuti Yehova anali ‘kutsegula chitseko’ kaamba ka ife.​—1 Akorinto 16:9.

Pa msonkhano woyambirira, chodera nkhaŵa chachikulu cha olamulira a kumaloko chinakhala chowonekera. Iwo analoza kuti panali kale zipembedzo zinayi mu mudziwo​—Katolika, Baptist, Church of God, ndi Mormon. Chirichonse cha izi chinali ndi nyumba yaikulu ya tchalitchi, zina za zimene zinali mu mkhalidwe wa kusiidwa. Ndi kusoweka kwa malo pa chisumbupo, ndunazo zikayenera kukhala zochenjera ponena za kulola gulu lina la chipembedzo.

Kupyolera mwa wotembenuza, tinalongosola kuti m’maiko oposa 200 kuzungulira dziko lapansi, Mboni za Yehova zagawirako ku ubwino wa m’mudzi mwa miyezo ya makhalidwe abwino apamwamba imene amasunga. Tinatsimikizira ndunazo kuti misonkhano tsopano idzayamba kuchitidwa m’nyumba za Mboni za kumaloko, ndipo ngati chidzafikira kukhala choyenerera kumanga malo apadera osonkhanira, siidzafikira kukhala yosagwiritsiridwa ntchito, popeza kuti pa misonkhano yathu anthu amapezekako bwino.

Pambuyo pa kukambitsirana kwa chifupifupi ora limodzi, ndunazo zinalingalira za kupereka nkhaniyo ku msonkhano wotsatira wa Sahilas, wochitika pambuyo pake mkati mwa mlunguwo. Tikayenera kudikira kaamba ka yankho.

Ulendo ku Chisumbu cha Dog

M’malo mwa kungodikira, tinalingalira za kuchezera Achutupu, kapena Chisumbu cha Dog, ndi uthenga wa Ufumu. Bwato lathu, lotchedwa La Torre del Vigia (Nsanja ya Olonda), liri lopakidwa mowala ndi utoto wofiira ndi wobiriŵira ndipo linaikidwa ndi motor ya kunja. Bwatolo limaima mosiyana kotheratu ndi macayucos ena ambiri, kapena ngalawa, zomangiliridwa pa makochezi. Ulendo wa mphindi 45 kudutsa nyanja za mafunde unatibweretsa ife ku Achutupu.

Achutupu chiri chisumbu chodziŵika chaching’ono cha ku malo otentha, chokhala ndi mitengo ya mngole ndi magombe a mchenga. Koma ndi chiŵerengero chachifupifupi 2,000, icho chinawoneka kukhala chodzaza ndi anthu. Mizera ya misasa ya kumaloko inali paliponse, yosiyanitsidwa kokha ndi tinjira tating’ono, tosakonzedwa bwino. Timisasato tonse tinawoneka tofanana. Zipupa, zopangidwa ndi nsungwi zomangiliridwa mozungulira mkombelo wowonda wa nthambi za mtengo, zinaima kokha 1.5 m pamwamba ndipo zinafoleredwa ndi denga lalitali, lochindikala la makwata a kanjedza. Mkatimo, munali kokha malo amodzi okwanira kaamba ka banja lonse. Panalibe mazenera, koma mipata pakati pa nsungwizo inalola kuwala kokwanira ndi mpweya kulowamo.

Tisanachezere nyumbazo ndi uthenga wathu wa Baibulo, tinalingalira kutsatira mwambo wa kumaloko wa kufikira mafumu a m’mudziwo kupeza chilolezo chawo. Chotero tinalunjika ku holo ya m’mudziwo, nyumba yaikulu pakati pa mzindawo.

Mkati mwa holoyo munali mwa mdima, koma pamene maso athu anazolowera, tinawona mizera ya mabenchi ya mitengo okhazikitsidwa mozungulira malo otseguka pakati. Zithunzi za maSahilas ofunika apapitapo zinali paliponse. Chifukwa cha mdimawo, zithunzizo, ndi bata, malowo anawoneka ngati mkati mwa tchalitchi. Pakati pa zonsezi panali amuna asanu, ena ataseyama pa mipando ya ndakhuta ndalema, ena atakhala pa mabenchi. Mwachiwonekere, iwo anali mafumu a mudziwo.

Akulankhula m’chinenero cha kumaloko, Bolivar, mmodzi wa Mbonizo yemwe anabwera ndi ife kuchokera ku Ustupu, analongosola chifuno cha ulendo wathu. Panthaŵi yomweyo, tinapatsidwa kulandiridwa kwa ubwenzi ndipo chilolezo chinaperekedwa kwa ife kuitanira pa anthu a m’mudzimo.

Ku Msasa ndi Msasa mu Achutupu

Amwenye a Kuna ali achimwemwe, anthu aubwenzi. Pamene tinayenda m’makwalala, ana anathamangira kwa ife, akumaitana “Mergui! Mergui!” kutanthauza “alendo.” Iwo anafuna kugwirana nafe chanza. Panali amuna ochepera pafupipo, ndipo tinauzidwa kuti ambiri a iwo anali ku mapuloti awo a minda m’dziko lalikulu.

Tinaitanidwa kulowa mkati panyumba iriyonse. Mkazi wanyumbayo anali kutikhazika ife pa mipando yolemerera, yamtengo yopangidwa ndi manja, ndipo banja lonselo linali kukhala mozungulira kumvetsera mosamalitsa. Tisanachoke, tinali kupatsidwa chakumwa chopangidwa ndi cocoa, coffee, kapena zipatso zina za kumaloko. Ichi chinatsatiridwa ndi tambula ya madzi kaamba ka kutsukuluza mkamwa mwathu. Mogwirizana ndi mwambo wa kumaloko, chinali choyenera kulavulira madziwo pansi. Ife mwamsanga tinaphunzira kutenga kokha chakumwa chochepera panthaŵi iriyonse, tikumakumbukira kuti panali nyumba zambiri zofunika kuzifikira.

Pa msasa umodzi, tinawona zosemasema zamitengo chifupifupi 50 za misinkhu yosiyanasiyana zitandandalikidwa m’mphepete mwa chipata cholowera. Bolivar analongosola kuti izi zinali kaamba ka kuthamangitsa mizimu yoipa. Pamene mkazi anabwera ku chitseko ndi kutiuza ife kuti mwamuna wake sanali bwino, tinamvetsetsa chifukwa chimene mafanowo anali pamenepo, popeza matenda kaŵirikaŵiri amagwirizanitsidwa ndi ziwanda.

Pambuyo pa kutiitana ife kulowa mkati, tinawona mwamunayo atagona pa mpando wa ndakhuta ndalema. Zolenjekedwa ndi nthambo pamwamba pake zinali unyinji wa timbale tating’ono tomangiliridwa ndi mivi ya nsonga zofiira zolunjikitsidwa pa munthu wodwalayo. Izi zinali kulingaliridwa kuti ziwopsye mizimu yoipa. Pansipo panali zipanda zambiri zokhala ndi zosemasema zazing’onozing’ono, akaliwo a fodya, ndi nyemba za cocoa zopera. Izi zinalingaliridwa kutonthoza mizimu. Bolivar anayesera kutonthoza banjalo mwa kuwauza iwo ponena za lonjezo la Mulungu la kuchotsa matenda onse, ndipo iwo analandira mabukhu ena a Baibulo. Kachiŵirinso, panali mwambo wa chakumwa ndi chikho cha madzi.

Zovala Zokongola za Kuna

Zowonekera za chilendo pa zisumbuzo ziri zovala zokongola za Amwenye a Kuna. Ngakhale kuti amuna kaŵirikaŵiri amavala zovala za mtundu wa Kumadzulo lerolino, akazi amakondabe kavalidwe ka mwambo wawo kokhala ndi shawelo yofiira, bulauzi yodula manja, ndi siketi yofika m’mawondo. Mbali ya ku mtunda kwa bulauziko kaŵirikaŵiri imakhala ndi mtundu wowala kwambiri. Mbali yapakati imatchedwa mola, imene alendo kaŵirikaŵiri amagula ndi kugwiritsira ntchito monga chokongoletsa pa chipupa. Iyo iri ntchito ya zigamba ya nsalu yokongola m’kakonzedwe ka kumaloko ka mbalame, nsomba, ndi zinyama. Siketiyo kaŵirikaŵiri imakhala chidutswa cha nsalu yodera yokhala ndi mbali zowala, yomangidwa mozungulira thupi ndi kulowetsedwa mkati m’chiwuno. Akazi ambiri a Kuna amameta tsitsi lawo kukhala lalifupi, ngakhale kuti akazi ambiri achichepere osakwatiwa amalola tsitsi lawo kuti likule motalikirapo.

Akaziwo amawoneka kukhala akukondwera ndi kuvala zokongoletsera zambiri. Ndolo za golidi, mikanda ya m’khosi, zibangiri, ndi zipini ziri zofala. Kaŵirikaŵiri zipangizo zonsezi za banja, zomwe zingafike ku zikwi za madola, zimavalidwa ndi akazi m’njira imeneyi. Zodziŵika, kachiŵirinso, ziri zomangira zawo za m’miyendo ndi m’mikono. Izi zimapangidwa ndi mikanda ya orange, yachikasu, ndi mitundu ina ndipo ingakhale yautali wochokera ku 5 kufika ku 15 cm mu lifupi. Akazi amaika mikandayo ku chingwe pa ulusi wautali ndipo kenaka kuwuzungulitsa molimba m’miyendo ndi m’manja awo. Mapangidwe ochenjera amafikiridwa mwa kusiyanitsa mitundu ya mikandayo pa ulusiwo. Zovalazo zimamangidwa molimba kotero kuti zingavalidwe kwa miyezi panthaŵi imodzi popanda kuzichotsa ngakhale pamene akusamba. Kuti akwaniritse kukongola kwawo, mzera woloza pansi wakuda umalembedwa kapena kutemeredwa motsika pakati pa mphumi yawo ndi mphuno, ukumathera pa mlomo wa m’mwamba.

Ulendo wathu wosangalatsa ku Achutupu unayenera kufupikitsidwa, popeza tinayenera kubwerera ku Ustupu m’nthaŵi yabwino kaamba ka kukumana ndi maSahilas. Pa makochezi, anthu ambiri anali kuyembekezera kupeza mabukhu ena a Baibulo kuchokera kwa ife. Tinali achimwemwe kusiya zimene tinali nazo ndi iwo.

Ntchito Yakwaniritsidwa

Kubwerera mu Ustupu, holo ya mudziwo inadzazidwa ndi mazana a anthu ofunitsitsa kupeza ngati Mboni za Yehova zikazindikiritsidwa mwalamulo kapena ayi. Motero tinalinso ife. Pamene zochitikazo zinapita patsogolo, tcheyamani anapereka chizindikiro cha kuvomereza Mboni za Yehova kugwira ntchito monga chipembedzo pa chisumbupo. Pamene anaitana khamu kupereka kawonekedwe kawo, mitima yathu inagunda mofulumira. Kokha anthu aŵiri anatsutsa; ambiri a iwo anavomereza.

Pomalizira, chipanicho chinasankha kupereka chilolezo cha lamulo kaamba ka ife kupanga misonkhano ndi kulalikira ku khomo ndi khomo ndi kukhala ndi chosankha cholembedwa m’zolembera zawo. Chotero, Mboni za Yehova zinakhala chipembedzo choyamba pa chisumbupo kukhala ndi kugwira ntchito kovomerezedwa molembedwa. Ena onse anali kokha ndi zivomerezo za pakamwa. Tinali achimwemwe chotani nanga ndi oyamikira kaamba ka chipambano chimenechi!

Chikuyembekezeredwa kuti chosankha chimenechi chidzatsegula khomo kaamba ka mbiri yabwino ya Ufumu kulalikidwa ku zisumbu zonse za San Blas. Pali chifukwa chirichonse cha kudzimvera monga mmene anachitira wamasalmo pamene ananena kuti: “Yehova achita ufumu! Dziko lapansi likondwere. Zisumbu zambiri zikondwere.”​—Masalmo 97:1.

[Mapu patsamba 28]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

PANAMA

Panama City

San Blas Islands

Gulf of Panama

Caribbean Sea

COLOMBIA

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena