Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 7/15 tsamba 30
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Khoti la Sanihedirini Linaweruza Mlandu wa Yesu Kenako Anapita Naye kwa Pilato
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Mmene Yehova Amatithandizira Kukwaniritsa Utumiki Wathu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Pamaso pa Bwalo la Akulu, Kenaka kwa Pilato
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Pamaso pa Sanhedrin, Ndiyeno kwa Pilato
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 7/15 tsamba 30

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Kodi Yesu anali kulozera kwa Yudasi pamene anauza Pilato kuti: “Chifukwa cha ichi iye wondipereka ine kwa inu ali nalo chimo loposa”?​—Yohane 19:11.

Sichikuwoneka kuti Yesu pano anali kulozera kwa Yudasi kapena munthu wina aliyense. Unyinji wa anthu okhala ndi liwongo unakhudzidwa m’zochitika zotsogolera ku kubweretsedwa kwa Yesu pamaso pa Pilato ndi kuyang’anizana ndi imfa.

Mwachidziŵikire, Yudasi angabwere choyamba m’maganizo chifukwa chakuti mtumwi woipa ameneyu anasanduka wopereka. (Yohane 6:64, 71; 12:4-6) Yudasi anakumana ndi akulu ansembe, omwe anafuna “kuchotsa” Yesu. Iwo analipira Yudasi ndalama za siliva 30 kuti ampereke iye. (Luka 22:2-6) Mosakaikira, chotero, Yudasi anali ndi chimo lokulira m’chigwirizano ndi imfa ya Yesu.

Koma Yudasi yekha sanadzetse imfa ya Yesu. Mkulu wa nsembe Kayafa anayambitsa ena kuti aphe Yesu. (Yohane 11:49, 50) Mateyu akulongosola kuti “akulu ansembe a Bwalo Lalikulu Lamilandu la Ayuda” anamuweruza Yesu, iwo anachita monga gulu. “Ndipo ansembe akulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu kuti amuphe iye. Ndipo anammanga iye, namuka naye, nampereka iye kwa Pilato kazembeyo.” (Mateyu 26:59-65; 27:1, 2) M’kuwonjezerapo, pambuyo pakuti Pilato anapeza Yesu wopanda liwongo, “makamu” anafunsa kuti Baraba amasulidwe. M’kusiyanitsa, ponena za Yesu iwo anafuula: “Mpachikeni iye!”​—Mateyu 27:20-23; Yohane 18:40.

Chotero Yesu mwachidziŵikire sanali kulankhula ponena za munthu mmodzi mwachindunji pamene iye anamuuza Pilato kuti: “Chifukwa cha ichi iye wondipereka ine kwa inu ali nalo chimo loposa.” (Yohane 19:11) Ngakhale kuti Yudasi, “mwana wa chitaiko,” mwapadera anali ndi thayo lalikulu la liwongo, ena ambiri anagawanamo m’liwongo kaamba ka chimo la kupha Yesu. (Yohane 17:12) Chimenecho ndicho chifukwa chake pa tsiku la Pentekoste mtumwi Petro anaitana Ayuda kulapa za machimo awo akulu motsutsana ndi Mwana wa Mulungu. (Machitidwe 2:36-38) Ayuda oterowo anali mbali ya mtundu wodzipereka kwa Mulungu wa Yesu, Yehova. Iwo anali nawo maulosi omwe anazindikiritsa Yesu monga Mesiya. Ndipo ambiri a iwo anawona zozizwitsa za Yesu. Chotero iwo ndithudi anali ndi liwongo lokulira la chimo kuposa nduna zomwe sizinali za Chiyuda zomwe zinamutcha Yesu wopanda liwongo.​—Yohane 18:38.

◼ Kodi nchiyani chimene chinali nsonga ya Yehova m’kuwuza Ezekieli kuti nkhope yake idzakhala yolimba, monga nkhope za Ayuda?

Ezekieli anali mneneri wa Mulungu, kutumikira pakati pa Ayuda omwe anatengedwa m’ndende ku Babulo. Andende amenewa mwachiwonekere analingalira kuti Yehova mwanjira ina yake akabwera mwamsanga ku chipulumutso chawo chifukwa iwo anali anthu ake osankhidwa. Iwo sanalandire nsonga yakuti chomwe anakumanizana nacho chinabwera pa iwo chifukwa chakuti iwo analandira kupanda chiyanjo kwake.

Chotero pamene Yehova anatsogoza Ezekieli “kunena nawo mawu anga,” sinali ntchito yopepuka. M’kukonzekeretsa mneneriyo, Mulungu anachenjeza kuti “sadzakumvera, pakuti safuna kundimvera ine; pakuti nyumba yonse ya Israyeli ndiyo yolimba mutu ndi wouma mtima.”​—Ezekieli 3:4, 7.

Pa nsonga imeneyi Mulungu anauza Ezekieli: “Tawona! Ndakhwimitsa nkhope yako itsutsane nazo nkhope zawo ndalimbitsa mutu wako utsutsane nayo mitu yawo. [Monga diamond, NW] ndalimbitsa mutu wako koposa mwala wolimbitsitsa. Usawaope kapena kutenga nkhaŵa pamaso pawo.”​—Ezekieli 3:8, 9.

Anthuwo anali osamvera ndi opanduka. (Ezekieli 2:6) Kodi iwo akakhala okhoza kulaka kapena kutsekereza mthenga wa Mulungu? Ayi. Popeza iye anali ndi chirikizo la Mulungu, Ezekieli sanayenere kukhala wofewa kuposa iwo. Mwala wolimbitsitsa uli mwala wolimba, wolimba kuposa chitsulo. Ngati Ayuda owuma khosiwo, osavomereza akanayenera kuyerekezedwa ndi mwala wolimbitsitsa, mofananamo akanatero Ezekieli. M’kuwonjezerapo, iye anayenera kukhala monga diamond, yolimba koposa pa miyala ya mtengo wapatali; iyo iri yolimba koposa kotero kuti ingakande ngakhale mwala wolimbitsitsa.​—Yeremiya 17:1, 2.

Ichi ndithudi sichikutanthauza kuti anthu a Mulungu lerolino ayenera kulingalira icho chokhumbirika kukhala olimba, osakhudzidwa ndi malingaliro a ena, kapena ngakhale ankhalwe m’kuchita chimene akumva kuti chiri cholondola. Dziŵani chimene mtumwi Petro akufulumiza ponena za kuchita ndi anthu ena: “Khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa, osabwezera choipa ndi choipa kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso.”​—1 Petro 3:8, 9.

Kuchitira chifundo kulinso chimodzi cha zisonkhezero m’kugawana kwathu mbiri yabwino ya Ufumu ndi ena. (Mateyu 9:36-38) Koma pamene tikumanizana ndi kusiyana, kukanidwa, kapena chitsutso chachindunji, sitidzasiya kulengeza uthenga wa Mulungu kaamba ka nthaŵi yathu. Icho chimaphatikizapo kulengeza kuti posachedwapa iye adzabweretsa “chilango kwa iwo osadziŵa Mulungu ndi osamvera uthenga wabwino wa Ambuye wathu Yesu.” (2 Atesalonika 1:6-9) Sitiyenera kutsekerezedwa kapena kubwezedwa. M’lingaliro limeneli tingakhale olimba monga diamond monga mmene Ezekieli anayenera kukhalira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena