Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 7/15 tsamba 31
  • Chidziŵitso pa Nyuzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chidziŵitso pa Nyuzi
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mizere ya Mbidzi
  • Atumiki Ogwira Ntchito?
  • Mbidzi—Hatchi ya mu Africa Yongodziyendera Mmene Ikufunira
    Galamukani!—2002
  • Maulendo Anga Owona Zinyama mu Africa—Analipo kaamba ka Ine—Kodi Adzakhalapo kaamba ka Ana Anga?
    Galamukani!—1988
  • Kodi Ndani Amene Amatetezera Nyama za Kuthengo za mu Afrika?
    Galamukani!—1993
  • Kuphunzira Baibulo M’malo Osonyezerako Nyama!
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 7/15 tsamba 31

Chidziŵitso pa Nyuzi

Mizere ya Mbidzi

“Mamiliyoni a zaka za chisinthiko” anapatsa mbidzi mizere yake, ikunena tero magazini ya chiBritish World of Wildlife. Chifukwa chake? Asayansi ena amanena kuti mizerayo inasinthika monga chodzichinjirizira mwa kusintha mtundu kuchinjiriza nyamayo kuchokera kwa adani. Yowoneka kukhala yowonjezera chikhulupiriro ku kawonedwe kameneka iri nsonga yakuti mizerayo imawoneka kukhala imatulutsa chiyambukiro chozimiririka pamene ziwonedwa kuchokera kutali. Ngakhale kuli tero, si anthu onse a sayansi amene akuvomereza. Dr. Gerrie de Graaff, wolangiza wa sayansi kaamba ka magazini ya ku South Africa ya nyama za nkhalango Custos, akudziŵitsa kuti: “Sitinganene kuti nyama zimawona zinthu m’njira imene timachitira.” Mwa kulongosola, de Graaff akuloza kuti mkhalidwe wa mbidzi sumagwirizana ndi nthanthi ya kusintha mitundu kwa kupangidwa kwa mizere. Nchifukwa ninji? Chifukwa mbidzi sizimayesera kudzibisa izo zokha monga mmene zimachitira nyama zina zomwe zimadalira pa kubisala mwa kusintha mtundu. Izo ziri zaphokoso ndi zokangalika ndipo zimadzipanga izo zokha kukhala zowonekera mwakudya mu zidikha za poyera.

Okhulupirira mu chisinthiko ena amapereka nthanthi yakuti mizera yowonekera ya mbidzi yakuda ndi yoyera imapanga chinyengo cha kawonedwe. Mogwirizana ndi de Graaff, chitsutso chimodzi chiri chakuti “mikango youkira iri yosakhoza kuzindikira imodzi chifukwa imafanana ndi zina m’gululo,” pamene kuli kwakuti “wina akulingalira kuti mkango umapangitsidwa chizungulire kapena kuŵerengera molakwika kulumpha kwake koyerekeza komalizira.” Koma monga mmene iye wawonera, “nthanthi zimenezi zimadalira pa chidaliro chowoneka ndi chimene mikango imaphera mbidzi.”

M’kumaliza, de Graaff akutsutsa kuti, “pa nthaŵi ino, ife ndithudi sitikudziŵa nchifukwa ninji mbidzi iri ndi mizere.” Ngakhale kuli tero, chifukwa chake, chiri chowonekera kwa ophunzira a Baibulo. Pa Genesis 1:20-25 timauzidwa kuti zolengedwa zonse za pa dziko lapansi zinalengedwa ndi Mulungu “monga mwa mitundu yawo.” Monga chotulukapo chake, dongosolo la chilengedwe la kapangidwe ka thupi liri ndi thayo kaamba ka mizere ya mbidzi. Mizere yoteroyo iri mbali ya makonzedwe osiyanasiyana ozizwitsa a chilengedwe cha Mulungu.

Atumiki Ogwira Ntchito?

Atsogoleri ena a chipembedzo amayembekezera kuwona kusintha kwadzidzidzi m’ntchito yawo mtsogolo mosachedwa. Ichi chinali chodera nkhaŵa chosonyezedwa ndi pasitala wa chiLutheran, Jean-Pierre Jornod, mu Reformiertes Forum, magazini ya chiLutheran yofalitsidwa mu Switzerland. Iye ananena kuti: “Ndingapite patali kufikira pa kuneneratu kuti pasitala wa mu chaka cha 2000 m’nthaŵi zambiri adzakhala ndi ntchito yapadera m’kuwonjezera ku ntchito yake ya upasitala.” Nchifukwa ninji? Iye anawonjezera kuti: “Osati kwenikweni kaamba ka zifukwa za ndalama, koma choyamba ndipo chokulira kwenikweni chifukwa chitaganya chawonjezera chifuno kaamba ka apasitala omwe ali ogwirizana ndi moyo wa tsiku ndi tsiku.”

Akumalongosola pa chifuno chimenechi, Jornod wanena kuti: “Pasitala wa m’chaka cha 2000 adzakhala mwamuna kapena mkazi wodziŵa bwino luso la kulankhulana. Sindikudzinenera kuti matchalitchi adzakhala opanda anthu pa nthaŵiyo, koma pasitala amene anthu amafuna kumufikira adzachoka ku tchalitchi, monga mmene mwapang’ono iriri nkhani lerolino. Uthenga wake, chotero, udzayenera kukhala wowonekera bwinoko, womvekera bwinoko, ndipo wachindunji kwambiri.”

Chiri chodziŵika kuti abusa olipiridwa anali osadziŵika mu Chikristu cha zana loyamba. Mtumwi Paulo, mwachitsanzo, anapereka kaamba ka zosowa zake zakuthupi kupyolera mwa ntchito yakuthupi​—kupanga mahema. Chowonjezerako nchiyani, iye anafikira anthu m’njira yokhutiritsa kwambiri, mwa kuwaphunzitsa iwo “pabwalo ndi kunyumba ndi nyumba.” (Machitidwe 18:3; 20:20, 21, 33, 34) M’kusiyanitsa ndi atumiki olipiridwa a lerolino, akulu kapena abusa, pakati pa Mboni za Yehova akutsatirabe dongosolo iri la m’Malemba la Akristu a m’zana loyamba.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena