Nkhani kaamba ka Chilengedwe
Mkazi wachichepere yemwe anapezeka ku koleji mu Iowa, U.S.A., akulemba ponena za mmodzi wa aphunzitsi ake: “Ndikukumbukira njira yake yophunzitsira ponena za kapangidwe ka thupi la munthu ndi kugwira ntchito kwa ziwalo za thupi. Iye mwamphamvu anakhulupirira mwa Mlengi, komabe mafunso a chisinthiko anali kufunsidwa ndi ophunzira.”
Pamene yemwe anali wophunzira ameneyu analandira kope la bukhu la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? iye analingalira za mphunzitsi wake ndi kumtumizira kope. Mphunzitsiyo anayankha:
“Ndiri pakati pa bukhulo, ndipo monga mmene ndinayembekezera, ilo liridi mtundu wa chinthu cholozerako chimene kaŵirikaŵiri ndinakhumba kuti ndinali nalo kuti ndichirikize zikhulupiriro zanga. M’kawonedwe kanga, ilo liri labwino koposa! Loperekedwa bwino ndiponso lolembedwa bwino koposa. Kufufuza konse komwe ndinakhumba kuti ndikanakhala ndi nthaŵi ya kukuchita kapena chikhoterero cha kukuchita kwachitidwa kaamba ka iye! Ndiponso, chikundisangalatsa ine kuti unadziŵa mtundu wa bukhu limene ndinafuna kukhala nalo. Zikomo kwambiri!”
Mwinamwake inunso mungasangalale kukhala ndi chofalitsidwa chomwe chimapanga nkhani yabwino yotero kaamba ka chilengedwe. Mungalandire Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka ndi kutsekeramo kokha K20.00.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu la masamba 256 Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Ndatsekeramo K20.00 (Zambia).