Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 8/1 tsamba 32
  • Nsanja ya Olonda pa Kaseti—Dalitso Lozizwitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nsanja ya Olonda pa Kaseti—Dalitso Lozizwitsa
  • Nsanja ya Olonda—1988
Nsanja ya Olonda—1988
w88 8/1 tsamba 32

Nsanja ya Olonda pa Kaseti​—Dalitso Lozizwitsa

Chimenecho ndi chimene anthu ambiri koposa akhala akunena. Wogulitsa woyendayenda wa inshuwaransi mu California anawona: “Ndimayenda pa msewu kaŵirikaŵiri. Ndimagwiritsira ntchito dongosolo la kaseti ya galimoto kuseŵerera matepiwo ndipo ndakhala wokhoza kumvetsera ku Nsanja ya Olonda, (m’Chingelezi) kope lirilonse, nthaŵi zambiri kuti ndipeza chuma cha chakudya chauzimu.”

Kalata ina, yochokera ku California, ikulongosola kuti: “Ndithudi matepi amenewa ali chimwemwe kwa ine, ndipo ndikudziŵa kuti ali mphatso yochokera kwa Mulungu wowona, Yehova. Ndimawakonda iwo ndipo ndimagwiritsira ntchito mwaŵi uliwonse kumvetserako. Ndimadzimva kuti ndikuika chidziŵitso cha mtengo wapatali m’mutu wanga m’malo mwa zopanda pake. Ndithudi, ‘zikomo’ yekha sangalongosole mokwanira mmene kukhala ndi matepiwo kumandipangira ine kudzimva.”

Mlembi wochokera ku Utah akunena kuti: “Pamene kuli kwakuti iwo kotheratu sangalowe m’malo mwa kuŵerenga kokulira ndi kuŵerenganso kwa nkhanizo, thandizo lawo ‘m’kuzamitsa’ chowonadi silinganyalanyazidwe. Tsopano mkazi wanga ndi ine timamvetsera mwakachetechete kunyumba kapena pamene tiri m’galimoto.”

Kodi mungasangalale kukhala ndi winawake akukuŵerengerani kope lirilonse la Nsanja ya Olonda kaamba ka chaka chotsatirachi? Chabwino, chotero, dzazani ndi kutumiza kapepala kotsatiraka, limodzi ndi chopereka choyenerera, ndi kulandira kulembetsa kwanu kwa Nsanja ya Olonda pa makaseti tepi. Kujambulidwa kwa kope iriyonse ya magaziniyo pa kaseti imodzi kudzatumizidwa kwa inu, makaseti aŵiri pa mwezi, 24 kaamba ka kulembetsa kwa chaka chonse. Choperekacho chiri kokha K288.00 (Zambia). Kwa anthu otsimikiziridwa kukhala akhungu kapena mwakuthupi osakhoza kuŵerenga zinthu zoŵerenga za nthaŵi zonse, kulembetsa kwa pa chakako kudzakhala kokha K96.00 (Zambia).

Chonde tumizana kulembetsa kwa chaka chimodzi kaamba ka makaseti a Nsanja ya Olonda. Chongani kabokosi koyenerera, ndi kutumiza chopereka choyenerera.

[ ] Chingelezi, chaka chimodzi. Ndatsekeramo K288.00.

[ ] Chingelezi, chaka chimodzi. Ndatsekeramo K96.00, limodzinso ndi chikalata chovomereza ponena za kulemala kwanga (monga choperekedwa ndi magulu kaamba ka akhungu, adokotala, akatswiri a malo a zopangapanga za opunduka, kapena ena).

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena