Msonkhano wa Pa Chaka—October 1, 1988
MSONKHANO WA PA CHAKA wa ziwalo za Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania udzachitidwa pa October 1, 1988, pa Holo ya Msonkhano ya Mboni za Yehova, 2932 Kennedy Boulevard, Jersey City, New Jersey. Msonkhano wa kumayambiriro wa ziwalo zokha udzasonkhanidwa pa 9:30 a.m., kutsatiridwa ndi msonkhano wa pa chaka wachisawawa pa 10:00 a.m.
Ziwalo za Corporation ziyenera kudziŵitsa Ofesi ya Mlembi tsopano kaamba ka kusintha kulikonse kwa makeyala awo olandirira makalata mkati mwa chaka chapita kotero kuti makalata okhazikika a chidziŵitso ndi masinthidwe angafikire iwo mwamsanga itapita August 15.
Makalata amasinthidwewo, omwe adzatumizidwa kwa ziwalo limodzi ndi chidziŵitso cha msonkhano wa pa chaka, ayenera kubwezedwa kotero kuti afikire Ofesi ya Mlembi wa Sosaite posachedwera ndi pa September 1. Chiwalo chirichonse chiyenera kudzaza ndi kubweza kalata yake ya masinthidwe mwamsanga, akumanena kaya iye adzakhalapo pa msonkhanowo mwaumwini kapena ayi. Chidziŵitso choperekedwa pa masinthidwe alionse chiyenera kukhala chotsimikizira pa nsongayi, popeza chidzadaliridwa m’kugamulapo yemwe adzakhalapo mwaumwini.
Chikuyembekezeredwa kuti gawo lonse, kuphatikizapo msonkhano wa nthaŵi zonse wa za bizinesi ndi maripoti, udzamalizidwa pofika 1:00 p.m. kapena mwamsanga pambuyo pake. Sipadzakhala gawo la masana. Chifukwa cha kuchepa kwa malo, chivomerezo chidzakhalapo mwa tikiti yokha. Palibe makonzedwe amene apangidwa kaamba ku kulunzanitsa msonkhano wa pa chaka ndi malaini a telefoni ku malo ena.