Msonkhano wa Pachaka—October 6, 1990
MSONKHANO WA PACHAKA wa ziŵalo za Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania udzachitidwa pa October 6, 1990, pa Holo Yamsonkhano ya Mboni za Yehova, 2932 Kennedy Boulevard, Jersey City, New Jersey. Msonkhano woyambirira wa ziŵalo zokha udzakhalako pa 9:30 a.m., wotsatiridwa ndi msonkhano wa pachaka wa anthu onse pa 10:00 a.m.
Ziŵalo za Sosaite ziyenera kudziŵitsa Ofesi ya Mlembi tsopano zakusintha kulikonse kwa makeyala awo olandirira makalata kumene kungakhale kutachitika mkati mwa chaka chapitacho kotero kuti zikalata zanthaŵi zonse zoperekera chidziŵitso ndi zikalata zowaitanira zikawafikire mwamsanga pambuyo pa August 15.
Zikalata zoitanira, zomwe zidzatumizidwa kwa ziŵalo limodzi ndi chidziŵitso cha msonkhano wa pachaka, ziyenera kubwezedwa kotero kuti zifikire Ofesi ya Mlembi wa Sosaite osati pambuyo pa September 1. Chiŵalo chirichonse chiyenera kulemba ndi kubweza mwamsanga chikalata chake choitanira, akumanena kuti kaya adzafika iye mwini pamsonkhanopo kapena ayi. Chidziŵitso choperekedwa pa chikalata choitanira chirichonse chiyenera kukhala chotsimikizirika pa mfundo imeneyi, popeza kuti ndicho chimene chidzagwiritsiridwa ntchito kudziŵira amene adzafika iwo eni mwachindunji.
Kukuyembekezeredwa kuti programu yonse, kuphatikizapo msonkhano wokambitsirana ntchito ndi malipoti, zidzamalizidwa podzafika 1:00 p.m. kapena mwamsanga pambuyo pake. Sipadzakhala programu yamasana. Chifukwa chakuchepa kwa malo, ofikapo adzaloledwa kokha ngati ali ndi tikiti. Palibe makonzedwe amene adzapangidwa a kulunzanitsa msonkhanowu wa pachaka ndi malo ena mwa nsambo za telefoni.