Msonkhano wa pa Chaka—October 7, 1989
MSONKHANO WA PA CHAKA wa ziŵalo za Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania udzachitidwa pa October 7, 1989, pa Holo ya Msonkhano ya Mboni za Yehova, 2932 Kennedy Boulevard, Jersey City, New Jersey. Msonkhano wa kumayambiriro wa ziŵalo zokha udzasonkhanidwa pa 9:30 a.m., kutsatiridwa ndi msonkhano wa pa chaka wachisawawa pa 10:00 a.m.
Ziŵalo za Corporation ziyenera kudziŵitsa Ofesi ya Mlembi tsopano kaamba ka kusintha kulikonse kwa makeyala awo olandirira makalata mkati mwa chaka chapita kotero kuti makalata okhazikika a chidziŵitso ndi masinthidwe angawafikire iwo mwamsanga itapita August 15.
Makalata amasinthidwewo, omwe adzatumizidwa kwa ziŵalo limodzi ndi chidziŵitso cha msonkhano wa pa chaka, ayenera kubwezedwa kotero kuti afikire Ofesi ya Mlembi wa Sosaite posachedwera ndi September 1. Chiŵalo chirichonse chiyenera kudzaza ndi kubweza kalata yake ya masinthidwe mwamsanga, akumanena kaya iye adzakhalapo pa msonkhanowo mwaumwini kapena ayi. Chidziŵitso choperekedwa pa masinthidwe aliwonse chiyenera kukhala chotsimikizirika pa nsongayi, popeza chidzadaliridwa m’kugamulapo yemwe adzapezekapo mwaumwini.
Chikuyembekezeredwa kuti gawo lonse, kuphatikizapo msonkhano wa nthaŵi zonse wa za bizinesi ndi maripoti, udzamalizidwa pofika 1:00 p.m. kapena mwamsanga pambuyo pake. Sipadzakhala gawo la masana. Chifukwa cha kuchepa kwa malo, chivomerezo chidzakhalapo mwa tikiti yokha. Palibe makonzedwe amene apangidwa kaamba ka kulunzanitsa msonkhano wa pa chaka ndi malaini a telefoni ku malo ena.