Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Yesu ananena kuti, “Mukadakhala osawona, simukadakhala nalo chimo.” (Yohane 9:41) Kodi iye anatanthauza kuti anthu ena ali opanda machimo?
Ayi, anthu onse lerolino ali ochimwa, monga mmene analiri onse m’zana loyamba, kusiyapo Yesu iyemwini. M’mawu amenewa ochokera pa Yohane 9:41, Yesu anali kulozera ku mkhalidwe wachindunji wa chimo.
Kholo lathu lakale limodzimodzilo linaipitsa mbadwa zake zonse ndi chimo. Adamu analengedwa wangwiro, wopanda chimo. (Deuteronomo 32:4; 2 Samueli 22:31) Pamene sanamvere malangizo okulira a Yehova, Adamu anakhala wopanda ungwiro. Kuchimwa kwakukulukulu kumatanthauza “kuphonya chikwangwani.” Adamu mowonadi anachita chimenecho. Chotero mwa kuphwanya lamulo la Mulungu, Adamu anakhala wochimwa.
Tonsefe tayambukiridwa chifukwa chakuti tonsefe tinabwera kuchokera kwa Adamu. Inu mungachitire chitsanzo chimenechi mwanjira iyi: Munthu wobadwa ndi kulemala m’mitsempha angakupatsire kwa mbadwa zake zonse; iwo akakhoza kukhala ndi kulemala kofananako. Sayansi yamakono ingatsimikizire kaya kulemala kwa m’mitsempha kwinakwake kumakhalapo mwa khanda lomawumbidwa m’mimba kapena wobadwa chatsopano, koma Yehova amapita kuposa pamenepo. Iye amavumbula kuti kulemala kokulira kunakhalapo mwa Adamu ndipo kuti kwapatsidwa kwa tonsefe. Kulemala kumeneku kuli chimo. “Uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu] ndi imfa mwa uchimo, chotero imfa inafikira anthu onse chifukwa chakuti anthu onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Mkhalidwe wochimwa umenewu waika anthu kuchokera pa chigwirizano ndi Mlengi, m’kuwonjezera ku kubweretsa pa iwo matenda ndi imfa. Palibe munthu pambali pa Yesu yemwe anakhalapo wolungama ndi wosatemberedwa ku imfa.—Aroma 5:18-21; 6:23; 2 Mbiri 6:36.
M’Baibulo, ngakhale kuli tero, munthu yense payekha nthaŵi zina amatchulidwa kukhala “ochimwa” chifukwa cha kudziŵika monga ochita chimo owonekera kapena mkhalidwe wokulira wa chimo. (Luka 19:2-7; Marko 2:16, 17; 14:41) Chimenecho, ndithudi, sichimatanthauza kuti anthu otsala ali angwiro, opanda chimo. Akanakhala tero, iwo sakanakalamba ndipo potsirizira pake kufa.
Cholembedwa mu Yohane mutu 9 chinaphatikiza munthu yemwe anabadwa wakhungu koma yemwe kuwona kwake kunabwezeretsedwa ndi Yesu. Munthuyo mwaumwini anali wosakhoza kuŵerenga Malemba, komabe anali ndi chidziŵitso chokhala ndi polekezera. Iye anadziŵa kuti Mulungu samamvetsera zopempha za ochimwa odzifunira. Chenicheni chakuti Yehova anapatsa mphamvu Yesu kuchita chozizwitsa cha kubwezeretsa kuwona chinatsimikizira kuti Yesu anali mneneri. Afarisi onyanda, ngakhale ndi tero, anakana kulandira umboni wanzeru wa munthuyu, ndipo anamponya kunja.—Yohane 9:13-17, 26-34.
Pambuyo pa chimenechi, Yesu ananena kuti: “Kudzaŵeruza ndadza ine ku dziko lino lapansi: kuti osapenya apenye ndi kuti iwo akupenya akhale osawona.” (Yohane 9:39) Inde, pamaziko a kulalikira kwake, machitachita ena, ndi malo m’zifuno za Mulungu, anthu akakhoza kaya kuwona kwauzimu ndi kuyenda m’kuwunika kapena akakhoza kukhala mu mdima wauzimu. (Yesaya 9:1, 2; 42:6, 7; Mateyu 4:13-17; 6:23; 2 Petro 1:9; 2 Akorinto 4:4) Ngati atsogoleri a chipembedzo akanakhala kokha Ayuda osadziwa kanthu okhala kokha ndi chimo wamba la munthu, kusalandira kwawo Mesiya kukanakhulukidwa. Koma iwo, omwe anadzinenera kukhala “akuwona,” kapena kumvetsetsa, anali owuma mutu mwapadera chifukwa chakuti anali ndi chidziŵitso chokulira cha Lamulo ndi Mawu aulosi a Mulungu. Chotero kukana kwawo Yesu kunali chimo lowopsya lomwe linawakana iwo kuposa mmene kupanda ungwiro kwawo kwachibadwa ndi chimo la umunthu kunachitira. Chotero, Yesu anawuza Afarisi kuti: “Mukadakhala osawona, simukadakhala nalo chimo. Koma tsopano munena kuti, ‘Tipenya.’ Chimo lanu likhala.”—Yohane 9:41.