Uthenga Kaamba ka Lerolino
Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zimakhala ndi uthenga, monga mmene zadziŵidwira ndi woŵerenga wa posachedwapa yemwe anafunsira kulembetsa ndi kulemba kuti: “Ndakhala ndikuŵerenga magazini anu ndi chikondwerero chachikulu. Ndinali ndi mwaŵi wa kuŵerenga malemba ogwirizana ndi nkhani zosiyanasiyana mkati mwa nthaŵi yanga yopuma.
“Nthaŵi zonse ndimadabwitsidwa pa uthenga wa magazini anu m’chiwunikiro cha nkhani za lerolino. Sichingagogomezeredwe mokwanira ponena za mmene zofalitsidwa zanu ziriri zoyenerera kaamba ka kumvetsetsa kwabwino kwa Baibulo. Magazini anu anali chifukwa chimene ndinagamulirapo kutulutsa Baibulo langa la fumbi ndi kuyang’ana m’bukhu la mabukhu. Ine ndimayang’anadi kutsogolo ku kope lirilonse.”
Inu nanunso mungakhale ndi Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zikutumizidwa kunyumba kwanu. Tumizani kokha K60, ndipo mudzalandira onse aŵiri a magazini amenewa (makope atatu pa mwezi) kaamba ka chaka chimodzi.
Chonde tumizani kulembetsa kwa chaka chimodzi kaamba ka Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ndatsekeramo K60 (Zambia). (Kunja kwa Zambia, lemberani ku nthambi ya Watch Tower ya kwanuko kaamba ka chidziŵitso.)